-
Machitidwe 2:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu wa ku Nazareti ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyera. Anatero kudzera muntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ ngati mmene inunso mukudziwira. 23 Munthu ameneyu, amene anaperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu+ ndi kudziwiratu kwake zamʼtsogolo, munachititsa kuti aphedwe pokhomeredwa pamtengo ndi anthu osamvera malamulo.+
-