-
2 Timoteyo 4:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto.+ Ndakhalabe ndi chikhulupiriro. 8 Panopa andisungira chisoti chachifumu cha olungama.+ Ambuye, woweruza wachilungamo,+ adzandipatsa mphotoyi pa tsikulo.+ Sikuti adzapatsa ine ndekha, koma adzapatsanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.
-
-
Chivumbulutso 20:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Kenako ndinaona mipando yachifumu ndipo amene anakhala pamipandoyo anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndinaona miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni za Yesu komanso chifukwa cholankhula za Mulungu. Inde, ndinaona miyoyo ya anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake ndipo sanalandire chizindikiro pazipumi zawo ndi padzanja lawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu+ kwa zaka 1,000.
-