Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 4/8 tsamba 20-23
  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi cha Mulungu kwa Odwala
  • Kodi Ndani Amene Amayambukiridwa ndi Kachilombo ka Aids?
  • Zimene Zikudziŵika Pakali Pano
  • Kodi Mudzachita Motani?
  • Nayonso Mikhole ya Aids Ingathandize
  • Kodi Ndani Amene Ali Pangozi?
    Galamukani!—1986
  • Aids Zimene Makolo ndi Ana Ayenera Kudziŵa
    Galamukani!—1991
  • AIDS—Vuto la Azaka Zapakati pa 13 ndi 19
    Galamukani!—1991
  • AIDS—Kodi Ndili Paupandu?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 4/8 tsamba 20-23

Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS

“MTSOGOLERI Wachipembedzo Apeza Zitseko Zotsekedwa, Atayambukiridwa ndi AIDS” ndiwo unali mutu wa nkhani ina mu The New York Times. Nyuzipepalayo inasimba za nkhani ya mtsogoleri wina wachipembedzo cha Baptist amene mkazi wake ndi ana aŵiri anayambukiridwa ndi kachilombo ka AIDS kuchokera m’mwazi umene mkaziyo anathiridwa mu 1982 (ana aŵiriwo anayambukiridwa ali m’mimba). Pambuyo pake, iye ndi banja lake analetsedwa kupita kumatchalitchi osiyanasiyana a Baptist chifukwa cha nthendayo. Atagwiritsidwa mwala, analeka kupita kutchalitchi ndi kusiya kukhala mtsogoleri wachipembedzo cha Baptist.

Kugwiritsidwa mwala kwa mwamuna ameneyu pa kulephera kwa tchalitchi chake kuchitapo kanthu kukudzutsa mafunso angapo: Kodi Mulungu amasamala anthu odwala, kuphatikizapo awo amene ali ndi AIDS? Kodi angathandizidwe motani? Kodi ndinjira zofuna kusamala zotani zimene zifunikira kutsatiridwa popereka chitonthozo Chachikristu kwa awo amene ali ndi AIDS?

Chikondi cha Mulungu kwa Odwala

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu Wamphamvuyonse amachitira chifundo chachikulu awo amene amavutika. Pamene anali padziko lapansi, Yesu nayenso anasonyeza chisoni chochokera mumtima kwa odwala. Ndipo Mulungu anampatsa mphamvu ya kuchiritsa anthu matenda awo onse, monga momwe Baibulo limasimbira kuti: “Makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa.”—Mateyu 15:30.

Ndithudi, lerolino Mulungu sanapatse munthu aliyense wa padziko lapansi mphamvu ya kuchiritsa mozizwitsa monga momwe Yesu anachitira. Koma ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti posachedwapa, m’dziko latsopano la Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Baibulo limalonjeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” (Chivumbulutso 21:4) M’kukonda kwake anthu kwakukulu, Mulungu walinganiza mankhwala achikhalire othetsera matenda onse kotheratu, kuphatikizapo AIDS.

Salmo 22:24 limati ponena za Mulungu: “Sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisira nkhope yake; koma pomfuulira iye, anamva.” Chikondi cha Mulungu chilipo kwa awo amene amampempha chithandizo mowona mtima.

Kodi Ndani Amene Amayambukiridwa ndi Kachilombo ka Aids?

Kwakukulukulu AIDS ndinthenda yotengedwa chifukwa cha njira ya moyo ya munthu. Anthu ambiri oyambukiridwa nayo amavomereza mogwirizana ndi Salmo 107:17 limene limati: “Anthu opusa azunzika chifukwa cha zolakwa zawo, ndi chifukwa cha mphulupulu zawo.”

Pamene munthu anyalanyaza miyezo ya Baibulo ndi kuloŵa muunansi wa kugonana kunja kwa makonzedwe aukwati a Mulungu, ngozi ya kuyambukiridwa ndi AIDS kapena kupatsa ena imakhala yotsimikizirika kwambiri. Ndiponso, pamene anthu osiyanasiyana abwerekana masingano obayira pamtsempha mankhwala oledzeretsa, iwo angayambukiridwe ndi AIDS ndipo akhoza kupatsira kachilombo kake kwa ena. Ndiponso, ambiri agwidwa ndi AIDS mwa kuthiridwa mwazi wa owupereka oyambukiridwa ndi nthendayo.

Komabe, mwachisoni, ziŵerengero zazikulu kwambiri za anthu opanda chifukwa zikuyambukiridwa ndi kachilombo ka AIDS, ndipo zimenezi zikuchitika m’njira zingapo. Mwachitsanzo, anthu ambiri a muukwati okhulupirika, kupyolera m’liwongo limene silili lawo, akuyambukiridwa ndi AIDS kupyolera muunansi wa kugonana ndi anzawo amuukwati oyambukiridwa kale. Ndiyenso, makamaka m’madera ena, peresenti yowopsa ya makanda ikuyambukiridwa ndi kachilombo ka AIDS kuchokera kwa anakubala oyambukiridwa nako, zikumapangitsa khanda lobadwa chatsopano lokhala ndi AIDS limenelo kukhala limodzi la mikhole ya tsoka koposa. Ndiponso, ogwira ntchito zachipatala ndi ena agwidwa ndi nthendayo chifukwa cha ngozi zochitika pamene anali kusamalira mwazi wa matendawo.

Mulimonse mmene AIDS imapezedwera ndi munthu, Malemba amafotokoza momvekera bwino kuti Mulungu alibe liwongo la kupatsirana kwa nthenda yakupha imeneyi. Ngakhale kuti lerolino unyinji wa awo amene ayambukiridwa adzidzetsera okha nthenda ya AIDS ndipo apatsa ena mwa khalidwe limene lili losagwirizana ndi miyezo ya Baibulo, maperesenti akusintha, akumasonyeza ziŵerengero zazikulu za mikhole yopanda chifukwa, monga ngati makanda ndi anzawo a muukwati okhulupirika.

Gulu la World Health Organization likunena kuti kuzungulira padziko lonse akazi tsopano akuyambukiridwa kaŵirikaŵiri ndi kachilombo ka AIDS pafupifupi mofanana ndi amuna ndi kuti podzafika chaka cha 2000, unyinji wa odwala nthendayo udzakhala wa akazi. Ogwira ntchito za umoyo mu Afrika akunena kuti 80 peresenti ya anthu odwala AIDS “amapatsidwa nthendayo mwa kugonana kwa mwamuna ndi mkazi, ndipo pafupifupi ena onse amapatsiridwa ndi nakubala kwa mwana wake mkati mwa kukhala ndi pakati kapena pa kubadwa kwa mwana.”

Komabe, pamene kuli kwakuti Mulungu amatsutsa kuswa malamulo ake alionse, kuphatikizapo kuswa malamulo kumene kumachititsa mavuto otero, iye amafulumira kusonyeza chifundo kwa onse amene amavutika. Ngakhale awo amene agwidwa ndi AIDS mwa machitachita oipa akhoza kupindula ndi chifundo cha Mulungu mwa kulapa ndi kuleka kuchita chimene chili choipa.—Yesaya 1:18; 1 Akorinto 6:9-11.

Zimene Zikudziŵika Pakali Pano

Vuto la AIDS nlapadziko lonse. Pamene kuli kwakuti asayansi akutsimikiziritsa anthu kuti “kachilombo ka HIV sikamapatsiridwa kwa munthu wina mwawamba,” kumeneku sikuli kotonthoza kwambiri kwa mamiliyoni amene ali nako kale ndi mamiliyoni amene adzayambukiridwa nako m’zaka zimene zikudzazo. Umboni ukusonyeza kuti iko kakufalikira padziko lonse lapansi.

Polankhula mwachidule za njira zozoloŵereka zopatsirana, buku lina likuti: “Pafupifupi anthu onse okhala ndi HIV amapatsidwa kachilomboko mwa kugonana kapena mwa kuthiriridwa mwazi wa woyambukiridwa nako.” Polingalira ndemanga za akatswiri ochuluka a zamankhwala, lipoti lina likuti: “Kuti munthu ayambukiridwe, payenera kukhala kuloŵetsedwa kwa zinthu za madzi za m’thupi (kaŵirikaŵiri mwazi kapena ubwamuna) zochokera kwa munthu woyambukiridwa kuloŵa m’thupi la munthu wosayambukiridwa.”

Komabe, mawu akuti “pafupifupi anthu onse” ndi “kaŵirikaŵiri” amavomereza kuthekera kwa njira zina. Chotero pamene kuli kwakuti njira zake zambiri zopatsira AIDS zikudziŵidwa lerolino ndi awo amene ali m’ntchito ya zamankhwala, m’zochitika zina zochepa kwambiri, njira yoyambukiridwa ndi kachilomboko singadziŵike. Chifukwa chake, pangafunikirebe kusamala.

Kodi Mudzachita Motani?

Anthu pafupifupi 12 miliyoni kufikira 14 miliyoni padziko lonse ngoyambukiridwa kale ndi kachilombo ka AIDS. Ndipo kuyerekezera nkwakuti mamiliyoni ena ambiri adzayambukiridwa podzafika kuchiyambi kwa zaka zana likudzalo. Chotero, mothekera muli, ndipo mwina posapita nthaŵi mudzakhala ndi awo amene ali ndi nthendayi. Mwachitsanzo, m’mizinda yaikulu, kukhudzana kozoloŵereka ndi anthu otero kumachitika tsiku ndi tsiku kumalo a ntchito, kumalesitilanti, kumaholo akanema, kumabwalo azamaseŵero, m’mabasi, m’sitima za pansi, m’ndege, m’sitima za pamtunda, ndiponso m’malo ena a anthu onse.

Chotero, mowonjezereka, Akristu angakumane, ndi kusonkhezeredwa kuthandiza anthu odwala AIDS amene akufuna kuphunzira Baibulo, kufika pamisonkhano Yachikristu, ndi kupanga kupita patsogolo kufikira pakudzipatulira kwa Mulungu. Kodi ndimotani mmene Akristu ayenera kuchitira ndi zosoŵa zimenezi za mikhole ya AIDS? Kodi pali njira zofuna kusamala zimene zikakhala zothandiza kupindulitsa wodwalayo ndi awo amumpingo Wachikristu?

Polankhula mozika pamafufuzidwe aposachedwapa, kukhudzana kozoloŵereka sikumachititsa kupatsirana kwa AIDS. Chotero kukuonekera kukhala kwanzeru kuti munthu satofunikira kukhala ndi mantha omkitsa a kukhala pakati pa anthu a AIDS. Ndipo popeza kuti odwala AIDS ali ndi dongosolo lodzitetezera lofooka kwambiri, tiyenera kukhala osamala kuti asayambukiridwe ndi kachilomboko ka matenda ozoloŵereka kamene tingakhale nako m’thupi. Chivulazo chochitidwa m’thupi lawo chifukwa cha matenda a kachilombo otero chingakhale chachikulu.

Chifukwa cha mkhalidwe wowopseza moyo wa AIDS, kuli kwanzeru kukumbukira njira zina zabwino za kusamala polandira munthu wodwala AIDS m’mayanjano athu kapena aja a mpingo Wachikristu. Choyamba, pamene kuli kwakuti palibe chilengezo chapoyera chimene chiyenera kupangidwa, tingafune kudziŵitsa mmodzi wa akulu mumpingo za mkhalidwewo kotero kuti akakhale wokonzekera kupereka yankho lokoma mtima ndi loyenerera kwa aliyense amene angafune kudziŵa za nkhaniyo.

Popeza kuti kachilomboko kakhoza kupatsiridwa m’mwazi wa munthu woyambukiridwa nako, kungakhale kwabwino kuti mipingo igwiritsire ntchito imene imatchedwa kuti universal precautions (malangizo otetezera onse) poyeretsa zimbudzi ndi madondolozi, makamaka ngati madondoloziwo ali a mwazi. “Universal precautions” ndiwo mawu osankhidwa ndi akatswiri azamankhwala kufotokoza mpambo wa malamulo mwa umene mwazi uliwonse wochokera kwa munthu aliyense umalingaliridwa kukhala wamatenda ndi wothekera kukhala wangozi ndipo chifukwa chake umasamaliridwa mwanjira yapadera. Chifukwa chakuti Nyumba Yaufumu ili malo a anthu onse, kungakhale kwanzeru kukhala ndi zinthu zoyeretsera pafupi limodzinso ndi bokosi la magulovu a Latex kapena vinyl kaamba ka kusamalira koyenera ndi kuyeretsa ngati patachitika ngozi. Msanganizo wa 10 peresenti woyeretsera (madzi a Clorox) umavomerezedwa kaŵirikaŵiri kaamba ka kuyeretsera madondolozi a mwazi.

M’zochita zathu zonse ndi ena, kuphatikizapo odwala AIDS, Akristu akulangizidwa kutsatira chitsanzo cha Yesu. Kuchitira kwake chifundo awo amene anali odwala, komabe owona mtima m’chikhumbo chawo cha kukondweretsa Mulungu, nkoyenerera kuti tikutsanzire. (Yerekezerani ndi Mateyu 9:35-38; Marko 1:40, 41.) Komabe, popeza kuti pakali pano palibe mankhwala a AIDS, nkoyenera kuti Mkristu atenge njira zosamala pamene akupereka chithandizo chotonthoza kwa awo amene akudwala nthendayo.—Miyambo 14:15.

Nayonso Mikhole ya Aids Ingathandize

Wodwala AIDS wanzeru amazindikira kuti ena amawopa nthenda imeneyi. Motero, chifukwa cha kulemekeza malingaliro a awo amene akufuna kukhala othandiza, kungakhale bwino kwambiri kwa mkhole wa AIDS kusayambitsa mchitidwe wosonyeza chikondi wapoyera monga ngati kukumbatira ndi kupsompsona. Ngakhale ngati pali kuthekera kochepa kapena ngati palibiretu kuthekera kwakuti zisonyezero zotero zikhoza kufalitsa nthendayo, kudziletsa kumeneku kudzasonyeza kuti wodwalayo ali wolingalira ena, motero akumapindula ndi kulingaliridwa kofananako ndi ena.a

Pozindikira kuti ambiri ali ndi mantha a kusadziŵa chimene chingachitike, munthu wa AIDS sayenera kukwiya mofulumira ngati iyeyo sanaitanidwe kunyumba za ena panthaŵi yomweyo kapena ngati kuonekera kuti kholo lina likuletsa mwana wake kuyandikirana naye kwambiri. Ndipo ngati limodzi la Maphunziro Abuku Ampingo likuchitidwira pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova, kungakhale kwanzeru kwa munthu wa AIDS kusankha kuti adzikasonkhana kumeneko, mmalo mwa kukasonkhana m’nyumba ina ya munthu wina, pokhapokha ngati munthuyo wakambitsirana za mkhalidwewo ndi mwininyumbayo.

Anthu odwala AIDS ayenera kusamalitsanso ponena za ena, mwachitsanzo, pamene akukhosomola kwambiri ndipo akudziŵika kuti ali ndi tuberculosis (kholodzi). Pamenepo akafunikira kugwiritsira ntchito zitsogozo za kutetezera umoyo wa chitaganya pamkhalidwe umenewu ponena za njira za kudzipatula.

Mkhalidwe wina umene munthu wopanda liwongo angayambukidwire nayo ndiwo mwa kukwatirana ndi munthu wina amene ali ndi kachilombo ka AIDS mosadziŵa. Kufunika kwa kusamala m’mikhalidwe yotero kungakhale makamaka kofunika kwambiri ngati munthuyo kapena aŵiri onsewo ofuna kukwatirana anali osadzisungira kapena anagwiritsirapo ntchito singano kudzibayira mankhwala oledzeretsa asanafikire pachidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu. Popeza kuti pali chiŵerengero chomakula cha anthu amene ali oyambukiridwa mosaonekera ndi HIV (ndiko kuti, amene zisonyezero zake sizinaonekerebe), sikungakhale kosayenera kwa munthu kapena kwa makolo odera nkhaŵa kupempha kupimidwa AIDS m’mwazi kwa woyembekezeredwa kudzakhala wa muukwati chitomero kapena ukwati usanachitike. Chifukwa cha mkhalidwe wosakaza ndi wakupha wa nthenda imeneyi, woyembekezeredwa kukhala wa muukwati winayo sayenera kukhumudwa ngati pempholo laperekedwa.

Ngati kupimidwako kusonyezadi nthendayo, kukakhala kosayenera kwa munthu woyambukiridwayo kuumiriza woyembekezeredwa kukhala wa muukwatiyo kupitirizabe chibwenzi chawo kapena chitomero ngati woyembekezeredwa kukhala wa muukwati winayo akufuna kuthetsa unansiwo. Ndipo kukakhala kwanzeru kwa aliyense amene kalelo anali ndi njira ya moyo wosadzisungira ya ngozi kwambiri, amene anali wachiwerewere kapena amene anagwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa mwa kubaya singano pamtsempha, kusankha mwaufulu kukapimidwa asanayambe chibwenzi. Mwanjira imeneyi, malingaliro opsinjika angapeŵedwe.

Motero, monga Akristu tikufuna kuchita zinthu mwachifundo ndipo osati kunyansidwa ndi anthu amene ali ndi AIDS, komabe, tikumazindikira kuti malingaliro a anthu angakhale osiyanasiyana pankhani yovuta imeneyi. (Agalatiya 6:5) Sizonse zimene zikudziŵika ponena za nthenda yonga AIDS, chotero pangakhale chikayikiro kwa anthu ambiri ponena za nkhani zophatikizidwamo. Lingaliro lachikatikati la nkhaniyo likakhala la kupitirizabe kulandira mikhole ya AIDS mumpingo Wachikristu ndi kuisonyeza chikondi ndi ubwenzi, pamene kuli kwakuti panthaŵi imodzimodziyo chisamaliro choyenera cha kudzitetezera ife eni ndi mabanja athu panthendayo chikuchitidwa.

[Mawu a M’munsi]

a Kodi nchiyani chimene munthu amene akudziŵa kuti ali ndi AIDS ayenera kuchita pamene akufuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kubatizidwa? Chifukwa cha kulemekeza malingaliro a ena, kungakhale kwabwino kwa iwo kupempha ubatizo wamtseri, ngakhale kuti palibe umboni wakuti AIDS yapatsiridwa kwa munthu kupyolera m’dziwe losambira. Pamene kuli kwakuti Akristu ambiri a m’zaka za zana loyamba anabatizidwa pa masonkhano aakulu apoyera, ena anabatizidwa mwamtseri chifukwa cha mikhalidwe yosiyanasiyana. (Mac. 2:38-41; 8:34-38; 9:17, 18) Njira ina ingakhale yakuti woyembekezera ubatizo wodwala AIDS abatizidwe pomaliza.

[Bokosi patsamba 21]

Anandichititsa Chifundo

Tsiku lina pamene ndinali muutumiki wa m’khwalala, ndinafikira mkazi wina wachichepere wa zaka pafupifupi 20 zakubadwa. Maso ake aakulu ofiirira anaonekera kukhala achisoni kwambiri. Poyesa kuyambitsa makambitsirano onena za Ufumu wa Mulungu, ndinamsonyeza limodzi la matrakiti amene ndinagwira m’dzanja. Mosazengereza iyeyo anasankha lakuti Chitonthozo kwa Opsinjika Mtima. Anayang’anitsitsa trakitilo nandiyang’ana ndipo anati ndi liwu lachisoni kwambiri: “Mbale wanga wangomwalira kumene ndi AIDS.” Ndisanamalize kupepesa kwanga, iyeyo anati: “Nanenso ndikufa ndi AIDS, ndipo ndili ndi ana aang’ono aŵiri.”

Anandichitsa chifundo, ndipo ndinamuŵerengera m’Baibulo ponena za mtsogolo mmene Mulungu walonjeza anthu. Iyeyo mwasontho anati: “Kodi Mulungu angasamale bwanji za ine tsopano lino pamene kuli kwakuti sindinasamale za iye?” Ndinamuuza kuti kuchokera m’phunziro la Baibulo, iye angafikire pa kuzindikira kuti Mulungu amalandira aliyense amene amalapa mowona mtima nafikira pakumdalira ndi kudalira nsembe yadipo ya Mwana wake. Anayankha kuti: “Ndikukudziŵani. Ndinu a ku Nyumba Yaufumu ya kumunsi kwa msewuko—koma kodi munthu wonga ine angalandiridwe m’Nyumba yanu Yaufumu?” Ndinamtsimikizira kuti angaterodi.

Pamene anali kupitirizabe ulendo wake, atagwirira buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi trakiti lake, ndinalingalira kuti, ‘Ndikhulupirira kuti adzapeza chitonthozo chimene Mulungu yekha angapereke.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena