Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira October 9
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 12: “Lingalirani Ntchito Zodabwitsa za Mulungu.” Kambani mawu oyamba m’nthaŵi yosaposa mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani zina mwa zithunzi za m’buku latsopano zothandiza kuyamikira ulosi wa Yesaya.
Mph. 25: “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?” Kukambirana kogwira mtima kochititsidwa ndi woyang’anira utumiki. Mutaŵerenga chilengezo chomwe chili m’kalata ya Sosaite ya July 3, 2000 yopita kwa akulu, perekani kope limodzi la Uthenga wa Ufumu Na. 36 kwa aliyense wopezeka pamsonkhanowu. Ndiyeno pitirizani kukambirana nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani zimene mpingo wakonza kuti umalize kufola gawo lonse. Nenani mmene tingathandizire atsopano ndiponso ana kuti ayenere kukhala ofalitsa osabatizidwa. Chitani chitsanzo chachidule cha ulaliki. Gogomezerani kufunika kwakuti aliyense achite nawo mokwanira ndaŵala imeneyi.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kuti mu ulaliki pamapeto a mlungu tidzagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pamodzi ndi Uthenga wa Ufumu Na. 36.
Mph. 15: “Zida Zimene Zimaphunzitsa, Kusonkhezera, ndi Kulimbikitsa.” Nkhani. Nenani mwachidule mbiri ya mmene Sosaite inayambira kupanga makaseti avidiyo. (Onani buku la Proclaimers, masamba 600-601.) Amene ali nayo vidiyo imeneyi angabwereke anzawo amene alibe, kapena angaonere pamodzi.
Mph. 20: Tonsefe Tingasonyeze Mzimu Waupainiya. Kukambirana kwa wochititsa phunziro la buku ndi wachiŵiri wake, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1997, patsamba 22-3. Kambiranani chifukwa chake kukhala ndi apainiya ambiri mumpingo kuli kolimbikitsa ndiponso mmene ena onse angachirikizire kuti zimenezi zitheke. Kambirananinso njira zimene tingalimbikitsire amene akuchita upainiya pakalipano kuti apitirize komanso mmene mpingo wonse ungakhalire wachangu pautumiki.
Nyimbo Na. 131 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Konzekerani Misonkhano Mokwanira. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Phindu limene timapeza pamisonkhano kwenikweni limadalira pa zimene timachita pokonzekera. Pendani malingaliro othandiza operekedwa mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1998, masamba 15-16, ndime 8-11. Pemphani omvetsera kusimba zimene achita kuti apeze nthaŵi yofunika kuti akonzekere mokwanira.
Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 30
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mu utumiki wakumunda a October.
Mph. 12: Zokumana Nazo Pogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Pemphani ofalitsa osiyanasiyana kusimba zotsatira zabwino zimene apeza pogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Itanani apainiya okhazikika ndi othandiza kuti asimbe mmene akuyamikirira kuwonjezeka kwa ntchito m’ndaŵala imeneyi ndiponso mwayi umene ali nawo woyenda ndi ofalitsa osiyanasiyana.
Mph. 25: “Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi—Mbali Yachiŵiri—Mwa Kukhala Ofalitsa Ufumu.” Nkhani yokambidwa mwa mafunso ndi mayankho ndi mkulu wa banja lachitsanzo chabwino. Ŵerengani ndime ngati nthaŵi ingakuloleni.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 6
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Pendani mmene ntchito yogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 ikuyendera. Lengezani kukula kwa gawo limene lafoledwa kale ndiponso zimene zikufunika kuti timalize gawolo podzafika pa November 17.
Mph. 20: Kodi Timakhulupirira Chiyani? Mbale achite ulendo wobwereza kwa munthu amene anafunsa funso lakuti, “Kodi Mboni za Yehova zimaphunzitsa chiyani chomwe chimawapangitsa kukhala osiyana ndi zipembedzo zina?” Kambiranani mfundo zofotokozedwa m’bokosi la patsamba 6 mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1998. Fotokozani mmene zipembedzo zina zimanyalanyazira kapena kukana choonadi cha Baibulo chofunika chimenechi chifukwa chokonda ziphunzitso za anthu.
Mph. 10: Kuimba—Mbali Yofunika pa Kulambira Kwathu. Wochititsa phunziro la buku akukambirana ndi ofalitsa aŵiri ponena za kaimbidwe kawo pamisonkhano yachikristu. Waona kuti kuimba kwawo n’kogwetsa ulesi pang’ono. Akukambirana nawo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1997, masamba 27-8. Akuphunzira mawu a nyimbo imodzi imene ikaimbidwe pa Phunziro la Nsanja ya Olonda mlungu umenewo, monga momwe Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, inanenera patsamba 20, ndime 12. Mwa kuona kuimba kukhala kofunika, timatamandadi Yehova mochokera mumtima.
Nyimbo Na. 223 ndi pemphero lomaliza.