Zimene Tingachite Kuti Tizisangalala ndi Nyimbo za Ufumu
Atumiki a Mulungu amaona kuti nyimbo ndi mphatso yabwino kwambiri yochokera kwa Mulungu. (Yak. 1:17) M’mipingo yambiri, abale amasangalala kumvetsera Nyimbo za Ufumu zimene zimaimbidwa chapansipansi misonkhano isanayambe kapena ikatha. Kumvetsera nyimbo zauzimu kumatitsitsimula tikamafika pa misonkhano. Zimatithandiza kukonzekeretsa maganizo pa nkhani yolambira. Komanso kumvetsera nyimbo zatsopano za m’buku la nyimbo kumatithandiza kuzolowera kaimbidwe kake ndipo zimenezi zimatithandizanso kuti tiziimba bwino. Nyimbo za Ufumu zimene zimaimbidwa misonkhano ikatha zimakhala zotsitsimulanso pamene tikucheza ndiponso kulimbikitsana ndi abale athu. Choncho, bungwe lililonse la akulu likonze zoti pampingopo azimvetsera nyimbo za zipangizo zokha za Sing to Jehovah—Piano Accompaniment misonkhano isanayambe kapena ikatha. Koma ayenera kuonetsetsa kuti nyimbozi sizikukwera mawu kwambiri moti n’kulepheretsa abale kucheza bwinobwino.