Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w23 November tsamba 20-25
  • Kodi Yehova Amayankha Mapemphero Anga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yehova Amayankha Mapemphero Anga?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI TIZIYEMBEKEZERA KUTI YEHOVA ACHITA ZOTANI?
  • KODI YEHOVA AMAYEMBEKEZERA KUTI TIZICHITA CHIYANI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSINTHA ZINA ZOMWE TIMAPEMPHA?
  • Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
w23 November tsamba 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 49

Kodi Yehova Amayankha Mapemphero Anga?

“Mudzandiitana komanso mudzabwera n’kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.”—YER. 29:12.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

ZIMENE TIPHUNZIREa

1-2. N’chiyani chingatichititse kuganiza kuti Yehova sakuyankha mapemphero athu?

“UZISANGALALA chifukwa cha Yehova ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.” (Sal. 37:4) Limenelitu ndi lonjezo losangalatsa kwambiri. Koma kodi tiziyembekezera kuti Yehova angatipatse nthawi yomweyo zimene tikumupempha? N’chifukwa chiyani tikufunsa funso limeneli? Taganizirani zitsanzo izi. Mlongo akupemphera kuti alowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Koma zaka zikupita ndipo sakuitanidwa. M’bale wachinyamata akupempha Yehova kuti amuchiritse matenda ake aakulu kuti azitumikira bwinobwino mumpingo, koma sakuchira. Makolo akupempherera mwana wawo kuti apitirize kukhala m’choonadi koma mwanayo akusankha kusiya kutumikira Yehova.

2 N’kutheka kuti inunso munapempha Yehova zinazake koma simunayakhidwe mpaka pano. Zimenezi zingakupangitseni kuganiza kuti Yehova amayankha mapemphero a anthu ena osati anu. Apo ayi mukhoza kumaganiza kuti munalakwitsa zinazake. Mlongo wina dzina lake Janiceb anamvapo choncho. Iye ndi mwamuna wake ankapemphera kuti adzapite ku Beteli. Janice anati: “Ndinkakhulupirira kuti tiitanidwa ku Beteli pasanapite nthawi yaitali.” Koma banjali silinaitanidwe ndipo zaka zinkangodutsa. Mlongoyu anati: “Ndinakhumudwa kwambiri ndipo zinandisokoneza. Ndinkadzifunsa kuti kodi ndinamulakwira chiyani Yehova? Ndakhala ndikupemphera kwa nthawi yaitali kuti ndipite ku Beteli. Ndiye n’chifukwa chiyani sakuyankha pemphero langa?”

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Nthawi zina tingamakayikire ngati Yehova amamvetsera mapemphero athu. Anthu ena okhulupirika akale ankaganizanso choncho. (Yobu 30:20; Sal. 22:2; Hab. 1:2) N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamakayikire kuti Yehova adzayankha mapemphero anu? (Sal. 65:2) Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tikambirane mfundo zotsatirazi: (1) Kodi tiziyembekezera kuti Yehova achita zotani? (2) Kodi Yehova amayembekezera kuti tichita chiyani? (3) N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha zinthu zina zimene timapempha?

KODI TIZIYEMBEKEZERA KUTI YEHOVA ACHITA ZOTANI?

4. Mogwirizana ndi Yeremiya 29:​12, kodi Yehova akulonjeza kuti adzachita chiyani?

4 Yehova analonjeza kuti aziyankha mapemphero athu. (Werengani Yeremiya 29:12.) Mulungu wathu amakonda atumiki ake okhulupirika choncho sanganyalanyaze mapemphero awo. (Sal. 10:17; 37:28) Koma izi sizikutanthauza kuti azitipatsa chilichonse chomwe tingamupemphe. Tiyenera kudikira mpaka m’dziko latsopano kuti tidzalandire zinthu zina zimene timapempha.

5. Kodi Yehova amaganizira chiyani poyankha mapemphero athu? Fotokozani.

5 Yehova amayankha mapemphero athu mogwirizana ndi cholinga chake. (Yes. 55:​8, 9) Mbali ina ya cholingacho ndi yakuti padzikoli padzakhale anthu osangalala, ogwirizana komanso omvera ulamuliro wake. Koma Satana amanena kuti anthu angamasangalale ngati atamadzilamulira okha. (Gen. 3:​1-5) Pofuna kusonyeza kuti zimene Satana amanena ndi zabodza, Yehova walola kuti anthu azidzilamulira. Koma ulamuliro wa anthu wayambitsa mavuto ambiri amene tikukumana nawo masiku ano. (Mlal. 8:9) Timadziwanso kuti Yehova sangathetse mavuto onse panopa. Atati azichita zimenezi, anthu ena akhoza kumanena kuti ulamuliro wa anthu ndi wothandiza ndipo ukhoza kuthetsa mavuto a anthu.

6. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti nthawi zonse Yehova adzachita zinthu mwachikondi komanso mwachilungamo?

6 Mapemphero akhoza kukhala ofanana koma Yehova n’kuyankha m’njira zosiyana. Mwachitsanzo, Mfumu Hezekiya atadwala kwambiri anapempha Yehova kuti amuchiritse ndipo Yehova anamuchiritsadi. (2 Maf. 20:​1-6) Koma mtumwi Paulo atapempha Yehova kuti amuchotsere minga m’thupi, yomwe mwina inali matenda enaake, Yehova sanachotse vuto lakelo. (2 Akor. 12:​7-9) Chitsanzo china ndi cha mtumwi Petulo ndi Yakobo. Onsewa ankayembekezera kuphedwa ndi Mfumu Herode. Mpingo unkapempherera Petulo ndipo n’kutheka kuti unkapemphereranso Yakobo. Koma Yakobo anaphedwa pomwe Petulo anamasulidwa m’njira yodabwitsa. (Mac. 12:​1-11) Ndiye tikhoza kumadabwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Petulo koma Yakobo n’kumusiya kuti aphedwe?’ Baibulo silifotokoza chifukwa chake.c Koma chomwe tikudziwa ndi chakuti nthawi zonse Yehova “sachita zinthu zopanda chilungamo.” (Deut. 32:4) Komanso tikudziwa kuti iye ankasangalala ndi onse awiri. (Chiv. 21:14) Nthawi zina zinthu zimene sitimaziyembekezera ndi zimene zimachitika. Koma popeza timakhulupirira kuti nthawi zonse Yehova amayankha mapemphero athu mwachikondi komanso mwachilungamo, sitikayikira njira zimene amasankha poyankha mapemphero.—Yobu 33:13.

7. Kodi tiyenera kupewa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Tiyenera kupewa kumadziyerekezera ndi anthu ena. Mwachitsanzo, tikhoza kupempha Yehova kuti atithandize pa zinthu zina koma zinthuzo osachitika. Kenako tikhoza kumva kuti munthu wina anapemphanso zomwezo ndipo zikuoneka kuti Yehova wamuyankha. Zoterezi zinachitikira mlongo wina dzina lake Anna. Mwamuna wake dzina lake Matthew, ankadwala khansa ndipo iye ankapemphera kuti achire. Pa nthawi yomweyo panalinso alongo awiri achikulire omwe ankadwala khansa. Anna ankapempherera kwambiri Mwamuna wake komanso alongo awiriwa. Alongowa anachira koma Matthew anamwalira. Poyamba Anna ankaganiza kuti Yehova anathandiza alongo awiriwa kuti achire. Ngati zili choncho, n’chifukwa chiyani Mulungu sanayankhe mapemphero ake oti mwamuna wake achire? Sitinganeneretu chomwe chinathandiza alongo awiriwa kuti achire. Koma chomwe tikudziwa ndi choti Yehova wakonza njira yoti adzathetsere mavuto athu onse ndipo amafunitsitsa kuukitsa anzake omwe amwalira.—Yobu 14:15.

8. (a) Mogwirizana ndi Yesaya 43:​2, kodi Yehova amatithandiza bwanji? (b) Kodi kupemphera kungatithandize bwanji tikakumana ndi mavuto aakulu? (Onerani vidiyo yakuti Pemphero Limatithandiza Kupirira.)

8 Yehova adzapitiriza kutithandiza nthawi zonse. Iye ndi Bambo wathu wachikondi ndipo sasangalala kutiona tikuvutika. (Yes. 63:9) Komabe iye satiteteza ku mavuto onse amene timakumana nawo, omwe ali ngati mitsinje kapena malawi a moto. (Werengani Yesaya 43:2.) Ngakhale zili choncho, iye amatilonjeza kuti angatithandize ‘kudutsa,’ kapena kuti kupirira zinthu ngati zimenezi. Iye sadzalola kuti mavuto atilepheretse kukhalabe okhulupirika kwa iye. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu kuti utithandize kupirira. (Luka 11:13; Afil. 4:13) Choncho sitikayikira kuti tidzakhala ndi zonse zomwe timafunikira kuti tipirire komanso tikhalebe okhulupirika kwa iye.d

KODI YEHOVA AMAYEMBEKEZERA KUTI TIZICHITA CHIYANI?

9. Mogwirizana ndi Yakobo 1:​6, 7, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova adzatithandiza?

9 Yehova amayembekezera kuti tizimudalira. (Aheb. 11:6) Nthawi zina mavuto athu angaoneke aakulu moti sitingathe kuwapirira. Mwinanso tingakayikire ngati Yehova angatithandize. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti ndi mphamvu za Mulungu, ‘tingakwere khoma.’ (Sal. 18:29) Choncho m’malo mokayikira, tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro chonse kuti ayankha mapemphero athu.—Werengani Yakobo 1:​6, 7.

10. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu.

10 Yehova amayembekezera kuti tichita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. Mwachitsanzo, m’bale angapemphe Yehova kuti amuthandize pamene akupempha abwana ake kuti akapezeke ku msonkhano wachigawo. Kodi Yehova angayankhe bwanji pemphero limeneli? Iye angamuthandize m’baleyo kuti alimbe mtima kukalankhula ndi abwana akewo. Koma m’baleyo ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi pempheroli popita kwa abwana akewo kukapempha. Mwinanso angafunike kupempha abwanawo mobwerezabwereza. Angathenso kupempha mnzake kuntchitoko kuti asinthane nthawi yogwirira ntchitoyo. Nthawi zina angathenso kupempha kuti asapatsidwe ndalama pa tsiku lomwe sanagwire ntchitolo.

11. N’chifukwa chiyani timafunika kupemphera mobwerezabwereza za vuto linalake?

11 Yehova amayembekezera kuti tizipemphera mobwerezabwereza tikakumana ndi mavuto. (1 Ates. 5:17) Zimene Yesu ananena zimasonyeza kuti nthawi zina sitingapatsidwe nthawi yomweyo zimene tapempha. (Luka 11:9) Choncho musamataye mtima. Muzipempherabe mochokera pansi pamtima komanso mobwerezabwereza. (Luka 18:​1-7) Tikamapemphera mobwerezabwereza timamusonyeza Yehova kuti nkhaniyo ndi yofunika kwambiri kwa ife. Timamusonyeza kuti timakhulupirira kwambiri kuti atithandiza.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSINTHA ZINA ZOMWE TIMAPEMPHA?

12. (a) Kodi ndi funso liti lomwe tiyenera kudzifunsa pa nkhani ya zimene timapempha, nanga n’chifukwa chiyani? (b) Kodi mapemphero athu angasonyeze bwanji kuti timalemekeza Yehova? (Onani bokosi lakuti, “Kodi Zimene Ndimapempha Zimasonyeza Kuti Ndimalemekeza Yehova?”)

12 Ngati zimene tapempha sizikuchitika tiyenera kudzifunsa mafunso atatu. Funso loyamba ndi lakuti, ‘Kodi zimene ndikupemphazi ndi zoyenera?’ Nthawi zambiri anthu timaganiza kuti timadziwa zomwe ndi zoyenera kwa ifeyo. Koma zomwe timapempha zikhoza kukhala zosathandiza kwenikweni. Tikamapempherera vuto linalake, pakhoza kukhala njira ina yabwino yothetsera vutolo kusiyana ndi imene tikupempha. Ndipo zinthu zina zomwe tingapemphe zingakhale zosagwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, taganizirani za makolo omwe tawatchula kumayambiriro aja. Iwo anapempha Yehova kuti mwana wawo apitirizebe kukhala m’choonadi. Zimene anapemphazi zikhoza kuoneka ngati zoyenera. Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha kumutumikira, ngakhalenso ana. (Deut. 10:​12, 13; 30:​19, 20) M’malo mwake makolowo angapemphe Yehova kuti awathandize kuti azimufika pamtima mwanayo n’cholinga choti azikonda Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi.—Miy. 22:6; Aef. 6:4.

Kodi Zimene Ndimapempha Zimasonyeza Kuti Ndimalemekeza Yehova?

Yehova ndi Atate wathu wachikondi ndipo amafuna kuyankha mapemphero athu. Komabe iye ndi Mlengi, choncho timafunikanso kumupatsa ulemu. (Chiv. 4:11) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Atate wathu wakumwambayu tikamapemphera?

  • Muzionetsetsa kuti zimene mukupempha zikugwirizana ndi cholinga cha Mulungu komanso muzikhala ndi zolinga zoyenera. (1 Yoh. 5:14) Mapemphero athu sayenera kukhala osonyeza kudzikonda, n’kumangopempha zofuna zathu zokha. Yakobo anachenjeza Akhristu a m’nthawi yake kuti mapemphero awo sangayankhidwe ngati amapempha “ndi cholinga choipa,” kapena kuti zolinga zadyera.—Yak. 4:3.

  • Popemphera, musamakhale ngati mukulamula. (Mat. 4:7) Muzikhulupirira kuti Yehova amadziwa njira yabwino yoyankhira mapemphero anu. Ndipo nthawi zina angayankhe m’njira imene simumayembekezera.—Aef. 3:20.

  • Muzikumbukira kumuthokoza pa zinthu zimene amakupatsani tsiku lililonse. Iye amasangalala kwambiri mukamamuthokoza chifukwa wakuthandizani.—Akol. 3:15; 1 Ates. 5:​17, 18.

13. Mogwirizana ndi Aheberi 4:​16, kodi ndi pa nthawi iti pomwe Yehova angatithandize? Fotokozani.

13 Funso lachiwiri lomwe tingadzifunse ndi lakuti, ‘Kodi ino ndi nthawi yoti Yehova andipatse zimene ndikupemphazi?’ Mwina tingamafune kuti Yehova aziyankha mapemphero athu nthawi yomweyo. Koma zoona n’zakuti Yehova amadziwa nthawi yabwino yoti atithandize. (Werengani Aheberi 4:16.) Ngati sitinapatsidwe nthawi yomweyo zimene tapempha, mwina tingamaone kuti Yehova wakana zomwe tapemphazo. Koma mwina zingakhale kuti iye wayankha kuti, ‘Dikira kaye.’ Chitsanzo ndi m’bale wachinyamata tinamutchula uja, yemwe anapempha kuti achiritsidwe. Ngati Yehova atamuchiritsa modabwitsa, Satana anganene kuti m’baleyo akupitiriza kutumikira Yehova chifukwa chakuti wamuchiritsa. (Yobu 1:​9-11; 2:4) Kuwonjezera pamenepo, Yehova anakonza kale nthawi yoti adzathetse matenda onse. (Yes. 33:24; Chiv. 21:​3, 4) Choncho sitimayembekezera kuti Yehova azichiritsa anthu modabwitsa masiku ano. Ndiye m’baleyo angapemphe Yehova kuti amupatse mphamvu komanso mtendere wamumtima kuti apirire matendawo komanso apitirize kumutumikira mokhulupirika.—Sal. 29:11.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Janice?

14 Taganizirani za Janice yemwe anapemphera kuti akatumikire ku Beteli. Panadutsa zaka 5 kuti azindikire mmene Yehova anayankhira pemphero lake. Iye anati: “Yehova anagwiritsa ntchito nthawi imeneyi pondiphunzitsa kuti ndikhale munthu wabwino. Ndinkafunika kuti ndizimukhulupirira kwambiri. Ndinkafunika kusintha mmene ndinkaphunzirira pandekha. Komanso ndinkafunika kuti ndizisangalala posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wanga.” Patapita nthawi, Janice ndi mwamuna wake anapatsidwa utumiki woyang’anira dera. Poganizira zimene zinachitika, iye anati: “Yehova anayankha mapemphero anga m’njira imene sindinkayembekezera. Panatenga nthawi kuti ndizindikire kuti iye anandiyankha bwino ndipo ndimasangalala kuti ndaona umboni wakuti ndi wachikondi komanso wokoma mtima.”

Chithunzi 1. Alongo awiri, aliyense akudzaza fomu yofunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Mlongo aliyense akupemphera asanadzaze fomuyo. 2. Mmodzi mwa alongo aja akusangalala kuonetsa alongo ena mu Nyumba ya Ufumu kuphatikizapo mlongo yemwe anadzazanso fomu uja, kalata yomuitana kuti akalowe sukulu. 3. Mlongo yemwe sanaitanidwe uja akupemphera kwa Yehova kenako akulemba kalata. Patapita nthawi, akulalikira m’dziko lina komanso kugwira nawo ntchito zomangamanga.

Ngati mukuona kuti Yehova sanayankhe pemphero lanu, yesani kupempha zinthu zina (Onani ndime 15)f

15. N’chifukwa chiyani nthawi zina sitingafunike kutchula mwachindunji zimene tikufuna popemphera? (Onaninso zithunzi.)

15 Funso lachitatu lomwe tiyenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi mwina ndiyenera kusintha n’kuyamba kupempherera zinthu zina?’ Ngakhale kuti nthawi zina tingatchule mwachindunji zinthu zimene tikufuna, nthawi zina sitingafunike kutchula mwachindunji zimene tikufuna kuti tione zimene Yehova angatipatse. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wachitsikana yemwe ankapemphera kuti akalowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Iye ankafuna kulowa sukuluyi n’cholinga choti akalalikire komwe kukufunikira olalikira ambiri. Choncho pamene ankapemphera kuti akalowe sukuluyi, ankafunika kupemphanso Yehova kuti amuthandize kudziwa mwayi wina wa utumiki umene angachite. (Mac. 16:​9, 10) Ndiyeno akanachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake pofunsa woyang’anira dera ngati m’mipingo yapafupi mukufunika apainiya ambiri. Apo ayi akanatha kulembera kalata ofesi ya nthambi kuti adziwe komwe kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri.e

16. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?

16 Munkhaniyi taphunzira zoti tingakhale otsimikiza kuti Yehova amayankha mapemphero athu mwachikondi komanso mwachilungamo. (Sal. 4:3; Yes. 30:18) Nthawi zina iye sangayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera. Koma Yehova sanganyalanyaze mapemphero athu. Iye amatikonda kwambiri ndipo sangatisiye. (Sal. 9:10) Choncho “muzimudalira nthawi zonse” popemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima.—Sal. 62:8.

PA NKHANI YA PEMPHERO, . . .

  • kodi tiziyembekezera chiyani kwa Yehova?

  • kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani?

  • n’chifukwa chiyani nthawi zina timafunika kusintha zimene timapempha?

NYIMBO NA. 43 Pemphero Loyamikira Mulungu

a Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhulupirira kuti nthawi zonse Yehova amayankha mapemphero athu mwachikondi komanso mwachilungamo.

b Mayina ena asinthidwa.

c Onani nkhani yakuti “Kodi Mumakhulupirira Kuti Yehova Amachita Zinthu M’njira Yoyenera?” mu Nsanja ya Olonda ya February 2022, ndime 3-6.

d Yehova amatithandiza kupirira mayesero. Kuti mudziwe zambiri, onerani pa jw.org vidiyo yakuti, Pemphero Limatithandiza Kupirira.

e Ngati mungafune kukatumikira m’dziko lina, onani malangizo omwe angakuthandizeni mu buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 10, ndime 6-9.

f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Alongo awiri akupemphera kuti akalowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Mlongo mmodzi akuitanidwa kusukuluyo pomwe winayo sakuitanidwa. M’malo mokhumudwa, mlongo yemwe sanaitanidweyo akupempha Yehova kuti amuthandize kuzindikira mwayi wina wa utumiki. Kenako akulembera kalata ofesi yanthambi n’cholinga choti adziwe komwe kukufunikira olalikira ambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena