Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/15 tsamba 26-30
  • Mmene mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Limbikitsani Ndi Mawu
  • “Chirikizani Ofooka”
  • Akulu Okhala Ndi Lilime Lophunzira
  • Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
    Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
  • Mmene Mungathandizire
    Galamukani!—2001
  • Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/15 tsamba 26-30

Mmene mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe

EPAFRODITO, wophunzira Wachikristu wa zaka za zana loyamba, anachita tondovi. Iye adatumidwa kukasamalira zosoŵa za mtumwi Paulo yemwe anali m’ndende koma anadwala kwambiri. Ngakhale kuti Epafrodito anachira, iye anachita tondovi chifukwa chakuti mpingo wakwawo, umene unamtuma ku Roma, ‘udamva kuti anadwala.’ (Afilipi 2:25, 26) Pokhala ali kutali koma akumafuna kupumitsa maganizo awo kunabweretsa kuchita tondovi. Mwachidziŵikire, iye analingaliranso kuti anamulingalira kukhala wolephera. Kodi akanathandizidwa motani kupezanso chimwemwe chake?

Epafrodito anabwezedwa ku mpingo wakwawo ku Filipi atatenga kalata yochokera kwa mtumwi Paulo. M’kalatayo, Paulo analangiza mpingowo kuti: “Mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa.” (Afilipi 2:27-30) Akristu a ku Filipi analimbikitsidwa kumuyanja Epafrodito mwathithithi m’njira imene ikayenerera mkhalidwe wapadera wa mpingo Wachikristu. Mawu awo otonthoza akamsonyeza kuti anawonedwa kukhala wofunika, inde, ‘wochitiridwa ulemu.’ Chisamaliro chachimwemwe chimenechi chikamuthandiza kupeza mpumulo ku kuchita tondovi kwake kwamaganizo.

Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti ngakhale kuti Akristu onse ‘amakondwera mwa Ambuye,’ ena pakati pawo amavutika ndi mitundu ina ya kuchita tondovi. (Afilipi 4:4) Kuchita tondovi kwamaganizo kwakukulu kuli vuto lowopsya lamalingaliro limene lafikira pa kutsogoza ku kudzipha. Nthaŵi zina, tsatanetsatane wa ubongo ndi zinthu zina zakuthupi zimaloŵetsedwamo. Mosasamala kanthu za izo, kaŵirikaŵiri kuchita tondovi kungachepetsedwe ndi thandizo lozindikira loperekedwa ndi ena. Motero, Paulo anapereka chilangizo chakuti: “Lankhulani motonthoza kwa miyoyo yopsyinjika.” (1 Atesalonika 5:14, NW) Chotero, mipingo ya Mboni za Yehova iyenera kupereka mwachimwemwe chirikizo lamaganizo kwa miyoyo yopsyinjika. Thayo limeneli linazindikiridwa ndi gulu Lachikristu lamakono kumbuyoko mu 1903, popeza kuti The Watch Tower panthaŵiyo inanena za miyoyo yopsyinjika, kapena okomoka mtima kuti: “Okomoka mtima ndi ofooka, akafunikira thandizo, chirikizo, chilimbikitso.” Koma kodi mungathandize motani miyoyo yopsyinjika?

Choyamba, mwakusonyeza “chifundo,” mungakhale okhoza kuthandiza wochita tondovi kuvumbula “nkhaŵa” ya mu mtima mwake. Pambuyo pake, “mawu abwino” ochokera kwa inu angamuthandize kukondwera. (1 Petro 3:8; Miyambo 12:25) Kungomulola kulankhula momasuka ndi kuzindikira kudera nkhaŵa kwanu kungabweretse mpumulo waukulu. “Ndinali ndi mabwenzi angapo amene ndikanawatsanuliradi mtima wanga,” analongosola motero Mary, Mkristu wosakwatiwa amene analimbana ndi kuchita tondovi. “Ndinafuna winawake womvetsera.” Kukhala ndi winawake amene mungagawane naye malingaliro amkati a msautso za moyo kungatanthauze zambiri.

Komabe, zambiri zimafunikira kuposa kungomvetsera ndi kupereka chilangizo chosazama chonga ngati, “Udziyang’ana ku mbali yabwino ya moyo” kapena, “Udzilingalira motsimikiza.” Ndemanga zoterozo zingasonyeze kusoŵeka kwa kuchitirana chifundo ndi kukhala zosathandiza kotheratu pamene wina ali wochita tondovi, mongadi mmene Miyambo 25:20 ikusonyezera ponena kuti: “Monga wovula malaya tsiku lamphepo . . . Momwemo woyimbira nyimbo munthu wachisoni.” Ndemanga zotsimikizirika zosakhala zenizeni zingasiye munthu wochita tondovi akudzimva moipirako. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zoyesayesa zoterozo sizimalongosola zifukwa za kuchita tondovi kwake.

Limbikitsani Ndi Mawu

Munthu wochita tondovi kwadzawoneni samangodzimva wachisoni koma mwinamwake wopanda pake ndi wopanda chiyembekezo. Liwu Lachigriki lotembenuzidwa “miyoyo yopsyinjika,” m’chenicheni limatanthauza “a moyo waung’ono.” Katswiri wina Wachigriki akulongosola liwuli motere: “Wina amene akusautsidwa ndi vuto loterolo, kotero kuti mtima wake umalefuka.” Motero, mphamvu zake zamalingaliro zatha, ndipo ulemu wake waumwini watsika.​—Yerekezerani ndi Miyambo 17:22.

Kholo Yobu linati: “Ndikadakulimbikitsani ndi mkamwa mwanga.” (Yobu 16:5) Liwu Lachihebri lakuti “kulimbikitsa” nthaŵi zina limatanthauzidwa “kulimbitsa” kapena “kupatsa mphamvu.” Limagwiritsidwa ntchito kulongosola mmene kachisi ‘analimbitsidwira’ mwa kumkonzanso. (Yesaya 41:10; Nahumu 2:1; 2 Mbiri 24:13) Mawu anu ayenera kumanganso mwaluso ulemu waumwini wa munthu wochita tondovi, njerwa ndi njerwa, kunena kwake titero. Kuchita zimenezi kumafunikira kuti mukondweretse “mphamvu [yake] ya kulingalira.” (Aroma 12:1, NW) Kope la 1903 la The Watch Tower logwidwa mawu poyambapo linati ponena za ochita tondovi: “Akumasoŵa . . . ulemu waumwini, amafunikira kusonkhezeredwa pang’ono, kuti atulutse maluso amene ali nawo, kaamba ka chilimbikitso chawo ndi kaamba ka dalitso la banja lonse lachikhulupiriro.”

Chitsanzo cha m’Baibulo cha Elikana ndi mkazi wake wochita tondovi Hana chimasonyeza mmene mungalimbikitsire ndi mawu, monga mmene anachitira Yobu. Elikana anali ndi akazi aŵiri. Mmodzi wa iwo, Penina, anali ndi ana angapo, koma Hana anali wouma. Mwachidziwikire, Hana anadzilingalira kukhala wopanda pake. (Yerekezerani ndi Genesis 30:1.) Monga kuti katundu ameneyu sanali wolemera mokwanira, Penina anamnyodola kotero kuti analira ndi kukana kudya. Ngakhale kuti Elikana sanazindikire kuya kwa kuvutika kwake, powona mkhalidwe wake, anafunsa kuti: “Hana, umaliriranji? ndipo umakaniranji kudya? ndipo mtima wako uwawa ninji?”​—1 Samueli 1:1-8.

Mafunso achifundo, osapatsa mlandu a Elikana anampatsa Hana mwaŵi wolongosola malingaliro ake. Kaya iye anayankha kapena ayi, iye anathandizidwa kusanthula chifukwa chimene amadzimverera wopanda pake. Chotero, moyo wochita tondovi unganene kuti, ‘Ndine munthu woipa.’ Mungafunse kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji mukudzimva motero?’ Kenaka mvetserani mosamalitsa pamene akukutsanulirani mmene amamverera mu mtima mwake.​—Yerekezerani ndi Miyambo 20:5.

Kenaka Elikana anafunsa Hana funso lolimbikitsa iri: “Ine sindiri wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?” Hana anakumbutsidwa za chikondi chake kaamba ka iye, mosasamala kanthu za kuuma kwake. Mwamunayo analingalira mkaziyo kukhala wofunika koposa, ndipo chotero anamaliza kuti: ‘Chabwino, sindiri wopanda pake kwenikweni. Ndimamkondadi mwamuna wanga!’ Mawu a mwamunayo anamlimbitsa Hana, popeza kuti anayamba kudya ndi kupita ku kachisi.​—1 Samueli 1:8, 9.

Mongadi mmene Elikana analiri wachindunji ndi kukokera chisamaliro cha mkazi wake ku chifukwa chakudzilingalira bwino, awo amene akukhumba kuthandiza anthu ochita tondovi ayenera kuchita zofananazo. Mwachitsanzo, Mkristu wotchedwa Naomi ananena izi ponena za zimene zinamthandiza kupezanso chimwemwe chake: “Mabwenzi ena anatamanda mmene ndinalerera mwana wanga, mmene ndinasamalirira nyumba yanga, ndi mmene ndinawonekera mosasamala kanthu za kuchita tondovi kwanga. Chilimbikitso chimenechi chinathandiza kwambiri!” Inde, chiyamikiro choyenerera chimathandiza munthu wochita tondovi kuwona mikhalidwe yake yabwino ndi kupanga kuyerekeza koyenera kwa ubwino waumwini.

Ngati mkazi wanu ali wochita tondovi, bwanji osayesa kummangirira mogwirizana ndi mawu a pa Miyambo 31:28, 29? Pamenepo timaŵerenga kuti: “Mwamuna wake namtama, nati, Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro, Koma iwe uposa onsewo.” Chikhalirechobe, mkazi wochita tondovi sangalandire kulingaliridwa koteroko, popeza kuti angamadzimve kukhala wolephera chifukwa cholephera kusamalira ntchito zapanyumba bwino lomwe monga mmene amalingalirira kuti ayenera kutero. Komabe, mwakumkumbutsa za mkazi amene iye ali mkati, ndi zimene anali asanachite tondovi, mungakhale okhoza kumkhutiritsa kuti kutamanda kwanu sikuli kusyasyalika. Mungavomerezenso kuti akukupanga kuyesayesa kwakukulu. Munganene kuti: ‘Ndidziwa zimene chakutengera kuchita zimenezi. Nchoyamikirika chotani nanga kuti ukukupanga kuyesayesa kwakukulu!’ Kulandira chivomerezo ndi chitamando cha mnzake wa mu ukwati ndi ana, awo amene amamdziŵa bwino kwambiri, n’kofunika koposa pomangirira ulemu waumwini.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:33, 34.

Kugwiritsira ntchito zitsanzo za Baibulo kungathandize munthu wochita tondovi kuwona masinthidwe a kalingaliridwe amene angakhale ofunika. Mwachitsanzo, mwinamwake munthuyo amakaikira mopambanitsa malingaliro a ena. Mungakambitsirane chitsanzo cha Epafrodito ndi kufunsa kuti: ‘Kodi muganiza kuti anachitiranji tondovi pamene anadziŵa kuti mpingo wakwawo unamva za kudwala kwake? Kodi iye analidi wolephera? Kodi nchifukwa ninji Paulo ananena kuti anayenera kuchitiridwa ulemu? Kodi phindu lenileni la Epafrodito monga munthu linadalira pa mwaŵi wa utumiki umene anali nawo?’ Mafunso oterowo angathandize Mkristu wochita tondovi kuwagwiritsira ntchito mwaumwini ndi kuzindikira kuti sali wolephera.

“Chirikizani Ofooka”

Baibulo limalimbikitsa kuti: “Chirikizani ofooka.” (1 Atesalonika 5:14) Kukhalapo kwa mabwenzi Achikristu amene angapereke chisamaliro chothandiza kuli ubwino wina wa chipembedzo chowona. Mabwenzi enieni ali awo amene “anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka,” ndipo iwo amamamatiradi kwa munthu wochita tondovi. (Miyambo 17:17) Pamene mtumwi Paulo anadzimva ‘wodzichepetsa’ ndipo anali ndi “mkatimo mantha,” anatonthozedwa ndi “kufika kwake kwa Tito.” (2 Akorinto 7:5, 6) Mofananamo, kuchezerana kosangalatsa ndi kutumiza telefoni pa nthaŵi zoyenera kungayamikiridwe mwakuya ndi miyoyo yopsyinjika. Mungafunse ngati pali njira iriyonse imene mungaperekere thandizo, monga ngati kupereka mauthenga, kuchita ntchito yapanyumba, kapena zina.a Mkritsu wotchedwa Maria akuti: “Pamene ndinali wochita tondovi, bwenzi linandilembera makalata nthaŵi zingapo ndipo nthaŵi iriyonse anaphatikizapo malemba olimbikitsa. Ndinkaŵerenga kalatayo mobwerezabwereza ndikumalira. Makalata oterowo anali ngati golidi kwa ine.”

Pambuyo polimbikitsa mpingo kuti uthandize “miyoyo yopsyinjika,” Paulo akuti: “Mukhale oleza mtima pa onse. Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa.” (1 Atesalonika 5:14, NW, 15) Kuleza mtima nkofunika, popeza kuti chifukwa cha kupweteka kwamaganizo, kulingalira koipa, ndi kutopa chifukwa chosoŵa tulo, munthu wochita tondovi angayankhe ‘mosonthokera kunena,’ monga mmene anachitira Yobu. (Yobu 6:2, 3) Rachelle, Mkristu amene amayi ake anachita tondovi kwadzawoneni, anavumbula kuti: “Nthaŵi zambiri Amayi ankanena chinachake choipa. Nthaŵi zonsezi, ndinkayesa kudzikumbutsa mtundu wa munthu amene Amayi alidi​—achikondi, achifundo, ndi ooloŵa manja. Ndinadziŵa kuti anthu ochita tondovi amanena zinthu zambiri zimene sakutanthauza. Chinthu choipitsitsa chimene wina angachite ndicho kubwezera mawu kapena machitidwe oipa.”

Akazi ena achikulire Achikristu angakhaledi okhoza kubweretsa mpumulo kwa akazi ena ovutika mwamaganizo. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:9, 10.) Akazi ofikapo Achikristu ameneŵa angachipange kukhala chonulirapo chawo kulankhula motonthoza ndi ameneŵa pa nthaŵi zoyenera. Nthaŵi zina nchoyenerera koposa kuti alongo achikulire Achikristu osati abale apitirize kuthandiza mkazi. Mwakulinganiza zinthu ndi kuzitsogoza bwino, akulu Achikristu angatsimikizire kuti miyoyo yopsyinjika ikulandira chisamaliro chofunikira.

Akulu Okhala Ndi Lilime Lophunzira

Makamaka abusa auzimu ayenera kukhala ndi “kudziŵa ndi chidziŵitso” kotero kuti “adziŵe mmene angalankhulire kuti alimbikitse ofooka.” (Yeremiya 3:15; Yesaya 50:4, Beck) Komabe, ngati mkulu sali wosamala, iye mosadziŵa angapangitse munthu wochita tondovi kudzimva moipirako. Mwachitsanzo, mabwenzi atatu a Yobu akuti anapita kumeneko “kumlirira ndi kumsangalatsa.” Koma mawu awo, osonkhezeredwa ndi lingaliro loipa la tsoka la Yobu, ‘anangomuthyola’ m’malo momtonthoza.​—Yobu 2:11; 8:1, 5, 6; 11:1, 13-19; 19:2.

Nkhani zosiyanasiyana m’mabuku a Watch Tower zandandalitsa malamulo a makhalidwe abwino amene angagwiritsiridwe ntchito pothandiza anthu.b Akulu ambiri agwiritsira ntchito nkhani zoterozo. Komabe, m’zochitika zina, ndemanga zosalingalira zoperekedwa ndi akulu​—kaya zaumwini kapena mu nkhani​—zakhala zovulaza kwambiri. Chotero lolani kuti akulu ‘asanene mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga’ koma ndi ‘kulamitsa kwa lilime la anzeru.’ (Miyambo 12:18) Ngati mkulu alingalira za chiyambukiro cha ndemanga zake asanalankhule, mawu ake angakhale otonthoza. Chotero, akulu, khalani achangu kumvetsera ndi kusafulumira kupanga kumaliza popanda kukhala ndi chithunzi chonse.​—Miyambo 18:13.

Pamene akulu asonyeza chikondwerero chenicheni mwa ochita tondovi, anthu oterowo amadzimva okondedwa ndi oyamikiridwa. Chisamaliro chopanda mpeni kumphasa choterocho chingasonkhezere anthu ameneŵa kunyalanyaza ndemanga zosamangirira zirizonse. (Yakobo 3:2) Kaŵirikaŵiri anthu ochita tondovi amalakidwa ndi malingaliro a liŵongo, ndipo akulu angawathandize kukhala ndi kawonedwe kolinganizika ka zinthu. Ngakhale ngati chimo lalikulu lachitidwa, chisamaliro chauzimu choperekedwa ndi akulu chingathandize ‘kuchiritsa chotsimphina.’​—Ahebri 12:13.

Pamene anthu ochita tondovi akudzimva kuti mapemphero awo ngwosakhutiritsa, akulu angapemphere nawo ndi kuwapempherera. Mwakuŵerenga nawo nkhani zozikidwa pa Baibulo zokhudza kuchita tondovi, akulu ‘angadzoze’ anthu ameneŵa ndi mawu auzimu otonthoza. (Yakobo 5:14, 15) Akulu angathandizenso munthu wochita tondovi kutenga masitepe Amalemba kuthetsa kusamvana kulikonse kumene angakhale nako ndi winawake, ngati zimenezi ndizo ziri vuto. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:23, 24; 18:15-17.) Kaŵirikaŵiri, kulimbana koteroko, makamaka m’banja, kumakhala maziko a kuchita tondovi.

Zindikirani kuti kuchira kumatenga nthaŵi. Ngakhale zoyesayesa zachikondi za Elikana sizinachotse mwamsanga kuchita tondovi kwa Hana. Mapemphero ake a mkaziyo ndi zitsimikizo za mkulu wansembe zinabweretsa mpumulo pomalizira. (1 Samueli 1:12-18) Chotero, khalani woleza mtima ngati pali chivomerezo chochedwa. Ndithudi, akulu sali adokotala ndipo chotero angapeze zoyesayesa zawo kulephera m’zochitika zina. Iwo, limodzi ndi ziŵalo za banja la wochita tondoviyo, angafunikire kumlimbikitsa iyeyo kufuna thandizo la katswiri. Ngati nkoyenera, akulu kapena ziŵalo za banja angalongosole momvekera kwa katswiri aliyense kufunika kwa kulemekeza zitsimikizo zachipembedzo za wochita tondoviyo.

Kufikira kudza kwa dziko latsopano la Mulungu, palibe aliyense amene adzakhala ndi umoyo wangwiro wakuthupi, wamaganizo, kapena wamalingaliro. Panthaŵi ino, Mkristu aliyense amene angataye chimwemwe chake chifukwa cha kuchita tondovi angapeze mphamvu osati kokha ku mpingo Wachikristu komanso kwa Atate wakumwamba, “amene amatonthoza ochita tondovi.”​—2 Akorinto 7:6, New American Standard Bible.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Defeating Depression​—How Others Can Help” mu Awake! ya November 8, 1987, masamba 12-16.

b Onani nkhani zakuti “An Educated Tongue​—‘To Encourage the Weary’” mu The Watchtower ya June 1, 1982, ndi “‘Mawu Auzimu’ kaamba ka Osautsidwa Mwamaganizo” m’kope la Nsanja ya Olonda la November 15, 1988.

[Bokosi patsamba 29]

MMENE MUNGALANKHULIRE MOTONTHOZA

□ MVETSERANI MOSAMALITSA​—Ndi mafunso ozindikira ‘tungani’ malingaliro a mumtima mwa munthuyo. Khalani achangu kumvetsera ndi kusafulumira kufikira malamizidwe musanakhale ndi chithunzi chokwanira.​—Miyambo 20:5; 18:13.

□ SONYEZANI KUMVERA CHIFUNDO​—‘Kuchitira chifundo’ kuyenera kugwirizana ndi ‘chisoni’ pamene mukuyesera kudziika m’malo mwa wochita tondoviyo. ‘Lirani naye wolira.’​—1 Petro 3:8; Aroma 12:15.

□ KHALANI WOPIRIRA​—Kungatenge kukambitsirana kobwerezabwereza, chotero khalani woleza mtima. Nyalanyazani ‘kunena kosonthokera’ kumene wochita tondovi angalankhule chifukwa cha kukwiya.​—Yobu 6:3.

□ LIMBIKITSANI NDI MAWU​—Thandizani wochita tondoviyo kuwona mikhalidwe yake yabwino. Perekani chiyamikiro chachindunji. Sonyezani kuti mavuto, zokumana nazo zoipa zakale, kapena zophophonya sizidziŵitsa mtengo wa wina. Longosolani chifukwa chimene Mulungu amamkondera ndi kumsamalirira.​—Yobu 16:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena