Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tp mutu 9 tsamba 94-107
  • Mtendere ndi Chisungiko pa Dziko Lonse Lapansi—Chiyembekezo Chodalirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtendere ndi Chisungiko pa Dziko Lonse Lapansi—Chiyembekezo Chodalirika
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maziko Amphamvu Achidaliro
  • Dziko Lapansi Liyenera Kukhala Malo Okhala Okongola
  • Kutha kwa Umphaŵi ndi Ukapolo wa Chuma
  • Thanzi Losatha ndi Moyo
  • Kukhoza kwa Dziko Lapansi Kokhala ndi Chiwerengero cha Anthu Choterocho
  • Maziko Otsimikizirika Achimwemwe Chosatha
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Ulamuliro Wolungama Udzampangitsa Paradaiso
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
Onani Zambiri
Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
tp mutu 9 tsamba 94-107

Mutu 9

Mtendere ndi Chisungiko pa Dziko Lonse Lapansi—Chiyembekezo Chodalirika

1, 2. Kodi ndimikhalidwe yotani yonenedweratu m’Baibulo, imene ikapangitsa dziko lapansili kukhala malo osangalatsa kwambiri kukhalamo?

DZIKO lapansili likanakhala malo osangalatsa ndi okondweretsa kukhalamo ngati mikhalidwe ya mtendere weniweni, ndi chisungiko inafunga kulikonse. Ngakhale kuli kwakuti siziri choncho konse tsopano, Baibulo limaneneratu kuti dziko lapansi lidzakhalabe malo abwino kwambiri kumene banja laumunthu lidzasangalala ndi moyo mokwanira.

2 Kwenikweni kodi nchiyani chimene Baibulo limalonjeza? Kodi tingatsimikizire motani kuti zidzakwaniritsidwa?

Maziko Amphamvu Achidaliro

3, 4. (a) Kodi timaphunziranji m’kudalirika kwa malamulo otsimikizirika amene akuyendetsa chilengedwe chonse? (b) Kodi ndani amene ali Wopanga malamulo amenewo, ndipo chotero kodi ndim’chiyaninso mmene tiri ndi chifukwa chabwino cha kuikamo chidaliro chathu?

3 Pali malamulo otsimikizirika amene akuyendetsa chilengedwe chonse. Ambiri a iwo timangowalingalira kukhala otero basi. Kutuluka kwa dzuŵa, kuloŵa kwa dzuŵa, mawonekedwe a mwezi, ndi nyengo zimadza ndi kuchoka m’mkhalidwe umene umachititsa kukhazikika kwa kukhala ndi moyo kwa anthu. Anthu amapanga makalendala ndi kulinganiza ntchito zawo m’zaka zambiri pasadakhale. Iwo amadziŵa kuti mayendedwe a dzuŵa, mwezi, ndi mapulaneti ngodalirika. Kodi tingaphunzirenji m’zimenezi?

4 Wopanga malamulo amenewo ali wodalirika kotheratu. Tingathe kudalira pa zimene amanena ndi kuchita. Muli m’dzina lake, monga Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti Baibulo limalonjeza dongosolo latsopano lolungama. (Yesaya 45:18, 19) Kawirikawiri m’zochita zathu za nthawi zonse za moyo watsiku ndi tsiku, mwachibadwa timadalira pamlingo wakutiwakuti pa anthu ena—awo amene amadza ndi zakudya kumsika, awo amene amapereka makalata, ndi mabwezi apamtima. Pamenepa, kodi sikuli kwanzeru kuika chidaliro chachikulu kwambiri mwa Mulungu ndi m’kutsimikizirika kwa kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake?—Yesaya 55:10, 11.

5. Kodi ndimotani mmene kupanda lingaliro ladyera lirilonse m’chimene Mulungu walonjeza kumatipatsira chikhulupiriro?

5 Ngakhale kuli kwakuti kaŵirikaŵiri malonjezo a anthu ngosadalirika, malonjezo a Mulungu ali odalirika kotheratu ndipo ali kaamba ka phindu lathu, osati lake. Ngakhale kuli kwakuti Mulungu samafuna kanthu kalikonse kwa ife, iye amapeza chikondwerero mwa awo amene amamkhulupirira chifukwa cha kumkonda iye ndi njira zake zolungama.—Salmo 50:10-12, 14.

6. Kodi nchikhulupiriro chotani chimene Baibulo limatithandiza kupeza?

6 Ndiponso, Baibulo limasonkhezera mphamvu zathu za kulingalira. Silimafunsira chikhulupiriro chosalingalira kapena kukhulupirira ziri zonse. Kunena zowona, limalongosola chikhulupiriro chowona kukhala “chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa, chisonyezero chowonekera bwino cha zenizeni ngakhale zisanapenyedwe.” (Ahebri 11:1, NW) M’Baibulo, Mulungu amatipatsa maziko amphamvu a chikhulupiriro. Mphamvu ya maziko amenewo imafikira kukhala yowoneka mowojezerekawonjezereka pamene tikula m’chidziŵitso cha Mawu a Mulungu ndi kuwona chowonadi chake chikugwira ntchito m’miyoyo yathu ndi m’kukwaniritsidwa kwa maulosi ake.—Salmo 34:8-10.

7. Pamene tipenda malonjezo a Baibulo amadalitso amtsogolo kodi nchiyani chimene sitiyenera kuyembekezera kuti kuwakhulupirira kuyenera kufuna kwa ife?

7 Malonjezo Abaibulo a madalitso amtsogolo amaposa kwambiri zimene anthu angayese kupereka. Komabe malonjezo amenewo samatifunikiritsa kukhulupirira zinthu zimene zimasemphana ndi zonse zimene anthu akumana nazo. Ndiponso iwo saali osemphana ndi zikhumbo zachibadwa zaumunthu. Talingalira ena a madalitso abwino kwambiri amenewa ndi kuwona mmene amenewa ali owona.

Dziko Lapansi Liyenera Kukhala Malo Okhala Okongola

8, 9. (a) Kodi ndilingaliro lotani limene liyenera kuperekedwa ku maganizo athu ndi liwu lakutilo “paradaiso”? (b) Kodi chinthu choterocho chinayamba chakhalapo padziko lapansi? (c) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti chiri chifuno cha Mulungu chakuti Paradaiso afunge padziko lonse lapansi?

8 Liwu lakuti “paradaiso” lachokera ku mawu ofanana ogwiritsiridwa ntchito m’nthawi zakale (Chiheberi, par·desʹ; Chiperesi, pai·ri·daeʹza; Chigiriki, pa·raʹdei·sos), mawu amene anagwiritsiridwa ntchito kulongosola zinthu zimene panthawiyo zinali kwenikweni padziko lapansi. Mawu amenewa ali ndi lingaliro lalikulu la paki kapena munda wa maluŵa wonga paki. Monga momwe kunaliri m’nthawi zakale, chimodzimodzinso lerolino pali malo ambiri otero, ena a iwo ndimapaki aakulu kwambiri. Ndipo munthu ali ndi chikumbo chachibadwa cha kukongola kwawo. Baibulo limalonjeza kuti nthawi idzafika pamene pulaneti lonseli lidzakhala munda wonga paki woterowo kapena paradaiso!

9 Pamene Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba anawapatsa monga malo okhala munda wa Edene, dzina limene limatanthauza “Paradaiso Wachikondwerero.” Koma Paradaisoyo sanayenera kudzalekezera kumalo amodzi amenewo. Mulungu anati kwa iwo: “Mubalane, muchuluke, mudzadze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28; 2:8, 9) Kumeneko kukalowetsamo kufutukulira malire a Paradaiso kumalekezero a dziko lapansi, chifuno cholongosoledwa mwa umulungu chimene sichinathetsedwe ndi njira ya kusamvera kwa Adamu ndi Hava. Yesu Kristu mwiniyo anasonyeza chidaliro m’chifunochi pamene analonjeza mwamuna amene anafa pambali pake kuti akakhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo m’Paradaiso pa dziko lapansi. (Luka 23:39-43) Kodi zidzachitika motani?

10. Mogwirizana ndi kunena kwa Chivumbulutso 11:18, kodi nzolinga zotani za Paradaiso zimene Mulungu amalonjeza kuzichotsa?

10 Mu “chisautso chachikulu” chikudzacho Mulungu adzachotsa zopinga zonse za Paradaiso wake alinkudza padziko lapansi mwa ‘kuwononga awo owononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Chotero Mulungu adzachita chimene maboma a anthu sakanatha kuchita konse. Iye adzachotsa awo onse amene mwadyera amaipitsa dziko lapansi kukhutiritsa umbombo wawo wa zamalonda, onse amene amathira nkhondo zosakaza, ndi onse amene amagwiritsira ntchito molakwa dziko lapansi chifukwa chakuti samalemekeza mphatso zambiri zimene Mulungu wapereka.

11. (a) Kodi nchochitika cha m’mbiri chotani chimene chimasonyeza kuti kubwezeretsedwa kwa Paradaiso kudziko lapansi sikuli kosemphana ndi zimene anthu akumana nazo? (b) Kodi ichi chimalimbikitsa chikhulupiriro chathu m’dalitso liti lolonjezedwa?

11 Pamenepo dziko lonse lapansi lidzaphuka ndi kukongola. Utsopano ndi chiyero panthawi imeneyo zidzakhala m’mpweya wake, madzi, ndi nthaka. Kubwezeretsedwa kwa Paradaiso kumeneku sindiko kathu kosakhulupirika, ndiponso sikuli kotsutsana ndi zimene anthu akhala nazo. Zaka mazana ambiri zapitazo, pamene mtundu wa Israyeli unatuluka mu ukapolo m’Babulo, Yehova Mulungu anaubwezeretsa kudziko la kwawo, limene panthawiyo linali chipululu. Komabe, chifukwa cha dalitso la Mulungu pa iwo ndi ntchito yawo, posapita nthawi dzikolo linakhala lokongola kwambiri kuti anthu owazungulira anadzuma kuti: ‘Lasanduka ngati munda wa Edene!’ Linakhalanso lobala zipatso zambiri, likumachotsa chiwopsezo chiri chonse cha njala ndi mpupuluzi. (Ezekieli 36:29, 30, 35; Yesaya 35:1, 2; 55:13) Chimene Mulungu anachita kalelo chinasonyeza pamlingo waung’ono chimene adzachitabe pamlingo wa dziko lonse kukwaniritsa malonjezo ake. Anthu onse owerengedwa kukhala oyenerera kukhala ndi moyo panthawiyo adzasangalala ndi zisangalalo zoperekedwa ndi Mulungu za moyo m’Paradaiso.—Salmo 67:6, 7; Yesaya 25:6.

Kutha kwa Umphaŵi ndi Ukapolo wa Chuma

12. Kodi ndimikhalidwe yachuma ndi yogwirira ntchito yotani imene iyenera kukonzedwa ngati titi tikhale ndi chisangalalo chenicheni m’moyo?

12 Umphaŵi ndi ukapolo ku madongosolo a chuma a mitundu nzofala padziko lonse lapansi. Sikukanakhala chisangalalo chenicheni cha Paradaiso ngati anthu mamiliyoni ambiri anapitirizabe kugwira ntchito imene inawalipira kokha ndalama zosakwanira kapena kugwira ntchito yotopetsa zimene zimapangitsa munthuyo kukhala ngati dzino losaganiza la gudumu m’makina aakulu.

13-15. (a) Kodi nkuti kumene timapeza chitsanzo cha m’mbiri chimene chimatisonyeza chomwe chiri chifuno cha Mulungu m’nkhaniyi? (b) Kodi ndimotani mmene kakonzedwe kameneka kanathandizira chisungiko ndi chisangalalo cha moyo wa munthu aliyense ndi banja?

13 Chifuno cha Mulungu kaamba ka munthu m’nkhaniyi chikuwonedwa mwanjira imene anayendetsera zinthu ndi Israyeli wakale. Mmenemo, banja lirilonse linalandira chuma cha cholowa cha kadziko. (Oweruza 2:6) Ngakhale kuli kwakuti limeneli likanatha kugulitsidwa, ndipo ngakhale kuli kwakuti anthu alionse paokha akanathadi kudzigulitsa mu ukapolo ngati anali ndi ngongole, Yehova anapangabe makonzedwe kutetezera kuwonjezeka kwa kukhala ndi malo aakulu kwambiri adziko kapena ukapolo wanthawi yaitali wa anthu. Motani?

14 Mwanjira ya makonzedwe a m’Chilamulo chimene iye anapatsa anthu ake. Chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ukapolo chinali ‘chaka chachimasuko’ pamene Mwisrayeli aliyense wokhala mu ukapolo motero ayenera kumasulidwa. Ndiponso, chaka chirichonse cha50 chinali “chaka choliza lipenga” chaka chamtundu wonsewo, chaka “cholalikira ufulu” kwa onse okhala m’dzikomo. (Deuteronomo 15:1-9; Levitiko 25:10) Pamenepo chuma chiri chonse cha cholowa chogulitsidwa chinali kubwezeredwa kwa mwini wake woyambirira. Onse okhala mu ukapolo anali kumasulidwa, ngakhale kuli kwakuti zaka zisanu ndi ziŵiri zinali zisanathe. Inali nthawi yosangalatsa ya kugwirizana kwa chimwemwe kwabanja ndi chiyambi chatsopano m’moyo mwandalama. Chotero, palibe kadziko kali konse kamene kakanagulutsidwa kwanthawi yonse. Kwenikweni, kugulitsidwa kwake, kunali kokha kubwereketsa kumene kukanatha, podzafika, m’chaka Choliza Lipenga.—Levitiko 25:8-24.

15 Zonsezi zinathandizira kukhazikika kwa chuma ndi kwa mtunduwo ndi chisungiko ndi mtendere wabanja lirilonse. Pamene malamulo amenewa anasungidwa, mtunduwo unachititsidwa kusaloŵa m’mkhalidwe wosakondweretsa umene timawuwona lerolino m’maiko ambirimbiri kumene kuli magulu oyenedera limodzi a olemeretsetsa ndi osaukitsitsa. Mapindu kwa munthu aliyense analimbikitsa mtunduwo, pakuti palibe aliyense amene anafunikira kukhala wosowa ndi wopsinjika ndi mikhalidwe yoipa yandalama. Monga momwe kunasimbidwira mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Solomo, “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake.” (1 Mafumu 4:25) Lerolino anthu ambiri sangagwiritsire ntchito maluso awo onse ndi malingaliro awo chifukwa chakuti iwo amangika m’madogosolo a zachuma amene amawakakamiza kutumikira zikhumbo za oŵerengeka kapena ngakhale za mmodzi yekha. M’malamulo a Mulungu munthu wogwira ntchito zolimba anathandizidwa kupereka maluso ake ku ubwino ndi chisangalalo cha onse. Chimenechi chikutipatsa chisonyezero cha lingaliro la kufunika kwa munthuyo ndi ulemu zimene awo opeza moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu adzasangalala nazo.

16. Ponena za mikhalidwe yokhalira moyo ndi mkhalidwe wa munthu wa chuma, kodi nchiyani chimene Ufumu wa Mulungu udzagawira nzika zake zonse?

16 Padziko lonse lapansi ulosi wa Mika 4:3, 4 udzakhala ndi kukwaniritsidwa kwakukulu. Anthu okonda mtendere okhala mu ulamuliro wolungama wa Mulungu “adzakhala munthu yense patsimde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wa kuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wamakamu padanena.” Palibe aliyense wa nzika za Ufumu wa Mulungu amene adzakhala m’nyumba zokhala mopanikizana ndi zauve. Iwo adzakhala ndi malo ndi nyumba zimene ziri za iwo eni. (Yesaya 65:21, 22) Mfumuyo, Kristu Yesu, kalekale analonjeza kuti, ‘ofatsa adzalandira dziko lapansi,’ ndipo iye ali ndi ulamuliro wonse ‘kumwamba ndi dziko lapansi’ wa kutsimikizira kuti izi zikuchitika—Mateyu 5:5; 28:13.

Thanzi Losatha ndi Moyo

17-19. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti thanzi labwino ndi moyo wautali ndizo zikhumbo zachibadwa za anthu? (b) Kodi ndimaumbomi otani onena za moyo wamunthu ndi onena za zomera amene amapangitsa kufupika kwa utali wa moyo wamunthu kuwonekera kukhala kwachilendo? (c) Kodi pali chiyani ponena za ubongo wa munthu chimene chimasonyeza kuti kuli kwanzeru kukhulupirira kuti munthu analinganizidwira kukhala ndi moyo kosatha?

17 Komabe, palibe ulionse wa mikhalidwe yabwino kwambiri imeneyi, imene inganpagitse moyo kukhala wamtendere kwenikweni ndi wosungika malinga ngati matenda, ukalamba, ndi imfa zinaphimba mtsogolo. Kodi kuli kosayenera kapena kosemphana ndi zimene munthu wakumana nazo kuyembekezera mpumulo ku zinthu zosautsa zimenezi? Ndithudi sikuli kosemphana ndi chibadwa cha munthu kufuna umenewu, pakuti anthu awonongera nthawi za moyo wawo ndi ziŵerengero zosaneneka za ndalama kuyesayesa kukukwaniritsa.

18 Chotero chiyembekezo cha thanzi losatha ndi moyo sichiri konse chosayenerera. Ndithudi, chimene chiridi chosayenerera ndi ichi: Mwamsanga pamene anthu afikira msinkhu umene iwo ayamba kukhala ndi chidziŵitso, nzeru, ndi luso la kuchita zinthu zoyenera, iwo amayamba kukalamba ndiyeno potsirizira pake kufa. Chikhalirechobe, pali mitengo imene imakhala ndi moyo kwazaka zikwi zambiri! Kodi nchifukwa ninji munthu, amene anapangidwa m’chifanefane cha Mulungu, ayenera kukhala ndi moyo kokha kachidutswa kanthawi zimene mitengo yosazindikira imakhala nayo? Kodi iye moyenerera sayenera kukhala ndi moyo wotalikirapo, kwambirimbiri?

19 Kwa akatswiri ophunzira za ukalamba, dongosololo likali chikhalirebe chinsinsi chachikulu. Chimene chirinso chinsinsi ndicho chenicheni chakuti ubongo wa munthu walinganizidwira kusunga pafupifupi kuchuluka kopanda mapeto kwa chidziŵitso. Monga momwe wolemba zasayansi anenera ubongo uli “wokhoza bwino lomwe kwambiri kusenza katundu aliyense wa chidziŵitso ndi kukumbukira amene munthu akuyembekezeredwa kuikamo—ndiponso kuŵirikiza nthawi mamiliyoni ambiri kuposa kuchuluka kumeneko.”55 Chimenecho chitanthauza kuti umbongo wanu uli wokhoza bwino lomwe kusenza osati kokha katundu aliyense amene mungaikemo m’nthawi ya moyo wazaka 70 kapena 80 komanso kuŵirikiza nthawi mamiliyoni chikwi chimodzi! Nzosadabwitsa kuti munthu ali ndi ludzu la chidziwitso loterolo, monga ngati chikhumbo cha kuphunzira kuchita ndi kutsiriza zinthu. Komabe iye amadodometsedwa ndi kufupika kwa moyo wake. Kodi nkoyenera kuti ukulu wodabwitsa waubongo wa munthu uyenera kukhalapo ndiyeno osagwiritsira ntchito kachidutswa chabe ka mphamvu yake? Kodi sikoyenera kwambiri kugamula kuti, monga momwe Baibulo limasonyezera, kuti Yehova analinganiza munthu kuti akhale ndi moyo kosatha pa dziko lapansi ndipo anampatsa ubongo woyenerana kwambiri ndi chifuno chimenecho?

20. Kodi nchiyani chimene Baibulo limanena kuti Mulungu analonjeza kuchitira anthu ponena za ziyambukiro zauchimo, kuphatikizapo imfa yeniyeniyo?

20 Baibulo limasonyeza kuti poyambirira munthu anali ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha koma anautaya mwa chipanduko: “Mwa munthu mmodzi [Adamu] uchimo unaloŵa m’dziko ndi imfa mwa uchimo, ndipo motero imfa inafikira kwa anthu onse chifukwa chakuti iwo onse anali atachimwa.” (Aroma 5:12, NW) Koma Baibulo lirinso ndi lonjezo la Mulungu lakuti m’Paradaiso wobwezeretsedwa, “sipadzakhalanso imfa; sipadzakhalanso maliro, kapena kulira kapena choŵaŵitsa.” (Chivumbulutso 21:3, 4; yerekezerani ndi 7:16, 17.) Limalongosola kuti moyo wosatha, wopanda ziyambukiro zauchimo, ndiwo chifuno cha Mulungu kaamba ka anthu. (Aroma 5:21; 6:23) Kuwonjezera apa, ilo limanjeza kuti madalitso a Dongoslo Latsopano la Mulungu adzatsegulidwira mabiliyoni ambiri a awo amene anafa kale. Motani? Mwachiukiriro chimene chimakhuthula manda a anthu onse. Mwa chidaliro Yesu ananeneratu kuti: “Ora lirinkunza m’limene onse amene ali m’manda achikumbukiro adzamva mawu ake nadzatuluka.”—Yohane 5:28, 29, NW.

21, 22. Kodi nchifukwa ninji chiyembekezo cha kubwezeretsedwa kuthanzi lokwanira sichiri kanthu kena kamene kali kakakulu kopambanitsa kukayembekezera?

21 Sayansi ya mamkhwala lerolino ikutulutsa “mankhwala ozizwitsa” ndi kuchita maopareshoni ocholowana amene akanawonekera kukhala osatheka ngakhale m’zaka makumi ochepa zapitazo. Kodi tiyenera kukaikira kuti Iye amene analenga anthu angachite zocholowana zozizwizitsa kwambiri za kuchiritsa? Ndithudi Mlengi ali ndi mphamvu ya kubwezeretsa thanzi labwino kwa anthu a mitima yolungama, ngakhale kusintha mchitidwe wa kukalamba. Ndipo iye angachite izi popanda kugwiritsira ntchito mankhwala, maopareshoni kapena ziŵalo zochita kupanga. Mwa kulingalira, Mulungu wapereka umboni wakuti madalitso otero saali opambanitsa kuwayembekezera.

22 Mulungu anapatsa mphamvu Mwana wake pamene anali padziko lapansi kuchita ntchito zamphamvu za kuchiritsa. Ntchito zimenezi zimatsimikiziritsa kuti palibe chofooka, chilema, kapena nthenda imene ingalake mphamvu ya Mulungu ya kuchiritsa. Pamene munthu amene thupi lake linakutidwa ndi khate anapempha Yesu kumchiritsa, Yesu mwachifundo anakhudza munthuyo nati: “Takonzedwa.” Ndipo, monga momwe cholembedwa cha m’mbiricho chikunenera, “pomwepo khate lake linachoka.” (Mateyu 8:2, 3) Yesu anachita zinthu zonga izi mowonedwa mokwanira ndi mboni zambiri, monga momwe wolemba mbiri Mateyu akusimbira kuti: “Makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa . . . ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.” (Mateyu 15:30, 31) Dziŵerengereni cholembedwacho pa Yohane 9:1-21 kuti muwone mmene mbiri ya kuchiritsa kotero iriri yotsimikizirika ndi yowona kwenikweni. Kutsimikizirika kwa zochitikazi kwachitiridwa umboni ndi mboni zambiri, kuphatikizapo dokotala, sing’anga Luka.—Marko 7:32-37; Luka 5:12-14, 17-25; 6:6-11; Akolose 4:14.

23, 24. Kodi nchifukwa ninji sikuli kosayenerera kukhulupirira kuti akufa adzabwezeretsedwa kumoyo mu Ufumu wa Mulungu?

23 Kaamba ka zifukwa zofananazo sitifunikira kuwona kukhala losakhulupirika lonjezo Labaibulo lakuti “kudzakhala kuuka” kwa akufa. (Machitidwe 24:15) Ngakhale zaka zambiri pambuyo pa imfa, mawu a munthu, kawonekedwe, ndi zochita zingathe kutulutsidwa pa filimu kapena pa vidiyo tepu. Kodi Iye amene analenga munthu, amenenso amadziŵa maatomu ndi mamolekyule enieni akaumbidwe ka munthu, sangakhoze kuchita zazikulu kuposa izi? Makompyuta opangidwa ndi anthu angathe kusunga ndi kugwirizanitsa mabiliyoni enieni a zidutswa za ziŵerengero. Koma Mulungu anapanga chilengedwe chonse chochititsa mantha limodzi ndi milalang’amba yake mabiliyoni ambiri (mamiliyoni zikwi zambiri), mlalang’amba ulionse uli ndi nyenyezi mabiliyoni ambiri. Zimenezo zikufika chionkhetso matiliriyoni, makwadiriliyoni, ndipo ngakhale kuposa! Komabe, Salmo 147:4 limati: “Aŵerenga nyenyezi momwe ziri; azitcha maina zonsezi”! Ndithudi kukanakhala kosavuta kwa Mulungu, amene ali ndi mlingo waukulu motero wa chikumbukiro, kukumbukira maumunthu a anthu kuti awabwezeretse kumoyo.—Yobu 14:13.

24 Kachiŵirinso, Yehova anapereka zitsanzo za m’mbiri kulimbikitsa chikhulupiriro chathu m’chiyembekezo chodabwitso chotero. Anapatsa Mwana wake mphamvu yosonyeza pamlingo waung’ono zimene adzachita pamlingo waukulu mkati mwa kulamulira kwake kolungama padziko lapansi. Yesu anaukitsa anthu akufa angapo, kaŵirikaŵiri akuwonedwa bwino lomwe ndi openyerera. Lazaro, amene iye anaukitsa pafupi ndi Yerusalemu, anali atakhala wakufa kwautali wokwanira kuti thupi lake liyambe kuvunda. Ndithudi chiyembekezo chachiukiriro chiri ndi maziko amphamvu.—Luka 7:11-17; 8:40-42, 49-56; Yohane 11:38-44.

Kukhoza kwa Dziko Lapansi Kokhala ndi Chiwerengero cha Anthu Choterocho

25, 26. Pamene akufa adzaukitsidwa, kodi malo okhala munthu aliyense adzapezeka kuti?

25 Kodi pulaneti lino lingapereke malo abwino okhalapo kwa chiŵerengero cha anthu choterocho chonga chimene chikachokera m’chiukiriro cha akufa? Kunatenga zaka zoposa 5 000 kuti chiŵerengero cha anthu cha dziko lapansi chifike biliyoni imodzi kuchiyambi kwa ma1800. Lerolino, chiri pafupifupi mabiliyoni asanu.

26 Chifukwa cha chimenechi, awo amene ali ndi moyo lerolino amaimira chigawo chachikulu cha chiwonkhetso cha anthu amene anakhalako. Ena ayerekezera kuti chiwonkhetso cha chiŵerengero cha anthu m’mbiri yonse ya anthu chiri pafupifupi 15 000 000 000. Chigawo chamtunda wa dziko lapansi chiri choposa maekala 36 000 000 000 (15 000 000-000 ha). Chimenecho chikapatsa munthu aliyense maekala oposa aŵiri (1 ha). Sikokha kuti chimenechi chikapereka malo olimapo chakudya, komanso chikapereka malo ankhalango, mapiri, ndi zigawo zina zokongola—popanda kuthithikana kosafunika m’Paradaiso. Ndiponso Baibulo limasonyeza kuti sionse amene akukhala ndi moyo tsopano adzapulumuka ndi kukhala m’Dogosolo Latsopano limenelo. Ndithudi, Yesu anati, “Chipata chiri chachikulu, ndinjira yakumka nayo kukuwonongeka ndi yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.” Iye ananenanso kuti pamene chiwonongeko cha dziko chifika, awo amene saali kuchita chifuniro cha Mulungu ‘adzachoka kuloŵa m’kudulidwa kosatha.’—Mateyu 7:13; 25:46.

27. Kodi dziko lapansi lingathe kutulutsa chakudya chokwanira kaamba ka anthu onsewo?

27 Koma kodi dziko lapansi likatha kutulutsa chakudya chokwanira kwa anthu ambirimbiri? Asayansi lerolino amanena kuti likatha kutero, ngakhale pansi pa mikhalidwe yamakono. Lipoti la mu The Toronto Star linati: “Mogwirizana ndi kunena kwa Gulu la Mitundu Yogwirizana la Chakudya ndi Malimidwe (FAO) pali kale dzinthu zokwanira zolimidwa padziko lonse kudyetsera munthu aliyense padziko lapansi ndi makalore 3 000 patsiku, chimene chiri . . . pafupifupi 50 peresenti kuposa muyezo wochepetsetsa wa mlingo wovomerezedwa.”56 Ponena za mtsogolo, linalongosola kuti ngakhale pansi pa mikhalidwe ya lerolino, pakayenera kukhala chakudya chokwanira kukhutiritsa zosoŵa kuŵirikiza kaŵiri chiwerengero cha anthu chadziko chamakono. Ndiponso, tiyenera kukumbukira kuti Yehova adzatsogolera anthu ake kugwiritsira ntchito kukhoza kwa kutulutsa zakudya koyenerera kwa dziko lapansi, pakuti Salmo 72:16 limatitsimikizira kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.”

28. Kodi chifukwa ninji palibe upandu wakuti popeza kuti anthu adzakhala ndi moyo kosatha, dziko lapansi likakhala lokhalidwa mopanikizana m’kupita kwa nthawi?

28 Tiyenera kudziŵa chimene chiri chifuno cha Mulungu, monga momwe chinalongosoledwera poyambirira kwa anthu aŵiri oyamba. Iwo anauzidwa ‘kudzadza dziko lapansi ndi kuligonjetsa,’ akumafutukulira malire a Edene kumalekezero a dziko lapansi. (Genesis 1:28) Mwachiwonekere, ichi chitanthauza kudzadza dziko lapansi kumlingo wabwino, osati kulidzadza mopambanitsa ndi anthu. Zimenezo zikaperekabe mpata wa dziko lapansi ‘logonjetsedwa’ kukhala paki ya dziko lonse mofanana ndi malo okhala okongola oyambirira a munthu. Chotero, lamulo la Mulungu limasonyeza kuti m’nthawi yokwanira ya Mulungu ndi njira, kukula kwa chiŵerengero cha anthu kudzalamuliridwa.

Maziko Otsimikizirika Achimwemwe Chosatha

29. Kodi nchiyambukiro chotani chimene maunansi ndi anthu ena chiri nacho pa chimwemwe cha munthu?

29 Komabe, ngakhale malo okhala okongola, ulemelero wa chuma, kugwira ntchito yosangalatsa, ndi thanzi labwino sizikanatsimikizira chimwemwe chanu chosatha. Ambiri lerolino ali ndi zinthuzi ndipo komabe ali opanda chimwemwe. Chifukwa ninji? Chifukwa cha anthu owazinga amene angakhale adyera, olongolola, achinyengo, kapena audani. Chimwemwe chosatha m’Dongosolo Latsopano la Mulungu chidzachokera kwakukulukulu m’mkhalidwe wa anthu wosinthidwa padziko lapansi. Chikondi chawo ndi ulemu kwa Mulungu ndi chikhumbo chawo cha kuchita zifuno zake zidzabweretsa kulemerera kwauzimu. Popanda zimenezo, kulemerera kwa zinthu zakuthupi kumakhala kosakhutiritsa ndi kopanda tanthauzo.

30. Kodi tikudziŵa motani kuti awo amene akukhala ndi moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu adzakhala anthu okha amene akuthandizira mtendere ndi chisungiko cha ena?

30 Inde, chiridi chisangalalo kukhala pafupi ndi anthu okoma mtima, odzichepetsa, aubwenzi—anthu amene mungawakondedi ndi kuwadalira, amene amalingalira mofananamo ponena za inu. (Salmo 133:1; Miyambo 15:17) Kukonda Mulungu ndiko kumene kumatsimikizira kukondadi mnansi, kumene kudzapangitsa moyo kukhala wokondweretsa kwambiri m’Dongosolo Lake Latsopano lolungama. Awo anse amene Mulungu adzapatsa moyo wamuyaya adzakhala atatsimikizira chikondi chawo kwa iye ndi kwa anthu anzawo. Pokhala ndi anthu oterowo monga anansi anu, mabwenzi, ndi atsamwali ogwira nawo ntchito, mudzakhala okhoza kusangalala ndi mtendere weniweni ndi chisungiko ndi chimwemwe chosatha.—1 Yohane 4:7, 8, 20, 21.

31. Ngati ife tifunadi moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu, kodi tiyenera kuchitanji tsopano?

31 Ndithudi, chiyembekezo chokondweretsa chotero chiri chokutsegukirani! Chotero njira yanzeru yeniyeni ndiyo kudziŵa chimene chiri chofunika kuti muchilandire. Tsopano ndiyo nthawi yogwirizanitsa moyo wanu ndi zofunika za Mulungu kaamba ka awo amene adzapulumuka kupyola “chisautso chachikulu” chikudzacho.—2 Petro 3:11-13.

[Chithunzi patsamba 98]

Tsiku lidzafika posachedwa pamene dziko lonse lapansi lidzasandulizidwa kukhala paradaiso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena