NYIMBO 22
Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere
Losindikizidwa
1. Yehova Mulungu wathu
Ndinu wamuyaya.
Mwapatsa Yesu Ufumu
Mwa kufuna kwanu.
Yesu adzalamulira
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Tsopano yafika
Nthawi ya chipulumutso.
Ufumu wayamba
Tikupemphatu: “Ubwere!”
2. Nthawi ya Satana itha
Posachedwa pompa.
Mavuto onse adzatha
M’dziko latsopano.
Yesu adzalamulira
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Tsopano yafika
Nthawi ya chipulumutso.
Ufumu wayamba
Tikupemphatu: “Ubwere!”
3. Angelo onse kumwamba
Akusangalala.
Satana wachotsedwako
Kulitu mtendere.
Yesu adzalamulira
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Tsopano yafika
Nthawi ya chipulumutso.
Ufumu wayamba
Tikupemphatu: “Ubwere!”
(Onaninso Dan. 2:34, 35; 2 Akor. 4:18.)