LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w18 May masa. 12-16
  • Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabala Zipatso mwa Kupilila’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabala Zipatso mwa Kupilila’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI NTHAWI ZINA TIKHOZA KULEFUKA?
  • KODI TIMABALA BWANJI ZIPATSO?
  • N’CIANI CINGATITHANDIZE KUBALA ZIPATSO MOPILILA?
  • “DZANJA LAKO LISAPUME”
  • Sangalalani Ndi Nchito Yanu Yakhama
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Cifukwa Cake ‘Timapitiliza Kubala Zipatso’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi ‘Mumamvetsa Tanthauzo la Malemba’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
w18 May masa. 12-16
M’bale Sergio na mlongo Olinda akugaŵila mabuku ofotokoza Baibo, kwa anthu amene akupita pa sitesheni ya basi

Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabala Zipatso mwa Kupilila’

‘Komano zogwela panthaka yabwino, ndi anthu amene . . . amabeleka zipatso mwa kupilila.’—LUKA 8:15.

NYIMBO: 68, 72

MUNGAFOTOKOZE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani nthawi zina tingafooke ngati timalalikila m’gawo la anthu opanda cidwi?

  • Tidziŵa bwanji kuti tonse tingathe kubala zipatso pa nchito yathu yolalikila?

  • N’ciani cimene cingatithandize kupitiliza kubala zipatso mopilila?

1, 2. (a) Timalimbikitsiwa bwanji na zitsanzo za ofalitsa amene amatumikila mokhulupilika m’magawo ouma? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Kodi Yesu anakamba ciani za kulalikila m’gawo la “kwawo”? (Onani mau amunsi.)

A SERGIO na akazi awo a Olinda ni apainiya a zaka za m’ma 80, ndipo amakhala ku America. Masiku ano, kuyenda kumawavuta cifukwa ca kuŵaŵa mendo. Olo zili conco, m’mamaŵa amayenda pansi kupita ku malo opezeka anthu ambili m’tauni yawo, ndipo amafika kumeneko ku ma 07:00hrs. Akhala akucita izi kwa zaka zambili. Iwo amakhala pafupi na sitesheni ya basi n’kumagaŵila mabuku ofotokoza Baibo kwa anthu opita pamalowa. Ambili amangowanyalanyaza, koma iwo sacokapo, ndipo amaonetsa nkhope zacimwemwe kwa aliyense amene wawayang’ana. Nthawi ikakwana 12:00hrs, amayenda pang’ono-pang’ono kubwelela ku nyumba. Pa 07:00hrs tsiku lokonkhapo, mukawapeza afika kale pa malowa. Ndipo caka na caka, banja lokhulupilika limeneli lakhala likulalikila uthenga wa Ufumu pamalowa m’maŵa uliwonse, kwa masiku 6 pa wiki.

2 Mofanana ndi m’bale Sergio na mlongo Olinda, abale na alongo ambili okhulupilika pa dziko lonse lapansi akhala akulalikila kwa zaka zambili m’magawo a anthu opanda cidwi. Ngati umu ni mmene zinthu zilili kwa imwe, tikukuyamikilani ngako cifukwa ca mzimu wanu wopilila.a Kukhulupilika kwanu potumikila Yehova kumalimbikitsa ambili, ngakhale aciyambakale m’coonadi. Onani ndemanga izi zimene oyang’anila dela ena anakamba: “Pamene nilalikila na abale na alongo okhulupilika amenewa, nimalimbikitsiwa ngako na citsanzo cawo.” Winanso anati: “Kukhulupilika kwawo kumanilimbikitsa kupitiliza kulalikila mopilila ndi molimba mtima.” Komanso wina anati: “Citsanzo cawo cimanikondweletsa.”

3. Kodi tidzakambilana mafunso atatu ati? Cifukwa ciani?

3 Kuti tisabwelele m’mbuyo pogwila nchito yolalikila imene Yesu anatipatsa, tiyeni tikambilane mafunso aya: N’cifukwa ciani nthawi zina tikhoza kulefuka pogwila nchitoyi? Kodi timabala bwanji zipatso? Nanga n’ciani cingatithandize kupitiliza kubala zipatso mopilila?

N’CIFUKWA CIANI NTHAWI ZINA TIKHOZA KULEFUKA?

4. (a) Kodi mzimu wa Ayuda wotsutsa unamukhudza bwanji Paulo? (b) N’cifukwa ciani Paulo anamvela mwanjila imeneyo?

4 Ngati nthawi zina mumalefulidwa polalikila m’gawo la anthu opanda cidwi, musadabwe nazo. Olo mtumwi Paulo, nthawi ina anamvelapo conco. Mu utumiki wake wa zaka pafupi-fupi 30, iye anathandiza anthu ambili-mbili kukhala ophunzila a Khristu. (Mac. 14:21; 2 Akor. 3:2, 3) Komabe, sanakwanitse kuthandiza Ayuda ambili kukhala olambila oona. Ambili anali kumutsutsa, ndipo ena anali kum’zunza. (Mac. 14:19; 17:1, 4, 5, 13) Kodi mzimu wotsutsa wa Ayuda unamukhudza bwanji Paulo? Iye anati: “Ndikunena zoona mwa Khristu . . . ndili ndi cisoni cacikulu ndipo mtima ukundipweteka nthawi zonse.” (Aroma 9:1-3) N’cifukwa ciani Paulo anamvela conco? Cifukwa nchito yolalikila anali kuikonda. Anali kulalikila Ayuda cifukwa anali kuwadela nkhawa kwambili. Conco, cinamuŵaŵa kuona kuti iwo anakana cifundo ca Mulungu.

5. (a) N’ciani cimatisonkhezela kulalikila anansi athu? (b) N’cifukwa ciani n’zosadabwitsa kuti nthawi zina timalefulidwa?

5 Mofanana ndi Paulo, timalalikila anthu cifukwa timawakonda na mtima wonse. (Mat. 22:39; 1 Akor. 11:1) Tidziŵa madalitso ambili-mbili amene anthu angalandile ngati asankha kutumikila Yehova, ndipo timafuna kuti nawonso akalandile madalitso amenewo. Tikaganizila za anthu a m’gawo lathu, timafunitsitsa kuwathandiza kuona zinthu zabwino zimene akuphonya. N’cifukwa cake timapitiliza kuwalimbikitsa kuphunzila coonadi ponena za Yehova na colinga cake kwa anthu. Ndipo pamene tilalikila, timakhala ngati tikuwauza kuti: ‘Takubweletselani mphatso yabwino kwambili. Conde ilandileni.’ Motelo, n’zosadabwitsa kuti ngati anthuwo akana mphatsoyo, ‘mtima umatipweteka.’ Kumvela mwanjila imeneyi sikutanthauza kuti tilibe cikhulupililo, koma ni umboni wakuti nchito yolalikila timaikonda. Conco, olo kuti nthawi zina timakumana ndi zolefula, timapilila. Mlongo Elena, amene watumikila monga mpainiya kwa zaka zoposa 25, anati: “Nimaona kuti nchito yolalikila ni yovuta. Koma palibe nchito ina imene ningakonde kugwila kuposa imeneyi.” Ni mmene ise tonse timaonela.

KODI TIMABALA BWANJI ZIPATSO?

6. Kodi tidzakambilana funso iti? Nanga tidzakambilana ciani kuti tipeze yankho yake?

6 Timadziŵa bwanji kuti timabalabe zipatso ngakhale ngati tikulalikila m’gawo louma? Kuti tiyankhe funso lofunika limeneli, tiyeni tikambilane mafanizo aŵili a Yesu okamba za kufunika ‘kobala zipatso.’ (Mat. 13:23) Fanizo yoyamba ni ya mtengo wa mpesa.

7. (a) M’fanizo la Yesu, kodi “mlimi,” “mpesa,” na “nthambi” zake ziimila ndani? (b) Kodi tifuna kupeza yankho pa funso iti?

7 Ŵelengani Yohane 15:1-5, 8. Onani kuti Yesu anauza atumwi ake kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiliza kubala zipatso zambili ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzila anga.” Yesu anakamba kuti iye ni “mpesa weni-weni,” Yehova ni “mlimi,” ndipo ophunzila ake ni “nthambi.”b Nanga zipatso zimene otsatila a Khristu afunika kubala n’ciani? M’fanizo limeneli, Yesu sanachule mwacindunji kuti zipatso zimenezi n’ciani. Koma anakamba mfundo inayake yofunika imene ingatithandize kupeza yankho.

8. (a) M’fanizo la Yesu, n’cifukwa ciani zipatso sizitanthauza ophunzila atsopano? (b) Kodi malamulo amene Yehova amatipatsa amakhala otani?

8 Pokamba za Atate wake, Yesu anati: “Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula.” M’mau ena, tingakambe kuti Yehova amationa kukhala atumiki ake kokha ngati tibala zipatso. (Mat. 13:23; 21:43) Conco, m’fanizo limeneli, zipatso zimene Mkhristu aliyense afunika kubala sizitanthauza ophunzila atsopano amene tingapange iyai. (Mat. 28:19) Cikanakhala kuti zimatanthauza ophunzila amene timapanga, ndiye kuti atumiki okhulupilika amene sakhala na mwayi wopanga ophunzila cifukwa colalikila m’gawo louma, akanakhala ngati nthambi zosabala za m’fanizo la Yesu. Koma sizingakhale conco iyai. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti sitingakakamize anthu kukhala ophunzila a Khristu. Ndipo Yehova ni wacikondi. Satilamula kucita zinthu zimene sitingakwanitse. Koma nthawi zonse, amatilamula kucita zimene tingakwanitse. Conco, iye sangaone atumiki ake kukhala osayenelela, cabe cifukwa cakuti alibe maphunzilo a Baibo.—Deut. 30:11-14.

9. (a) Kodi timabala zipatso mwa kugwila nchito yanji? (b) Ni fanizo iti imene tidzakambilana? Cifukwa?

9 Nanga zipatso zimene tifunika kubala n’ciani? Mwacionekele, zipatso zimenezi zimatanthauza nchito imene aliyense wa ise angakwanitse kucita. Kodi “kubala zipatso” kutanthauza ciani? Kutanthauza kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.c (Mat. 24:14) Fanizo la Yesu la wofesa mbewu limatsimikizila mfundo imeneyi. Lomba tiyeni tikambilane fanizo limenelo.

10. (a) M’fanizo la Yesu la wofesa mbewu, kodi mbewu na nthaka ziimila ciani? (b) N’ciani cimene mmela wa tiligu umabala?

10 Ŵelengani Luka 8:5-8, 11-15. M’fanizo la wofesa mbewu, mbewu ikuimila “mau a Mulungu,” kapena kuti uthenga wabwino wa Ufumu. Nthaka ikuimila mtima wa munthu wophiphilitsa. Mbewu imene inagwela pa nthaka yabwino inazika mizu, inamela, kenako inakula n’kukhala mmela wa tiligu. Ndiyeno, ‘inabala zipatso kuwilikiza maulendo 100.’ Koma kodi zipatso zimene mmela wa tiligu umabala n’ciani? Kodi umabala tummela tung’ono-tung’ono twa tiligu? Iyai, umabala mbewu yatsopano, imene m’kupita kwa nthawi, nayonso imakula n’kukhala mmela wa tiligu. M’fanizo la Yesu, mbewu imodzi ya tiligu inakula n’kubala mbewu zina (kapena kuti zipatso) zokwana 100. Kodi mfundo imeneyi igwilizana bwanji na nchito yathu yolalikila?

Mlongo akubala zipatso mopilila mwa kucita ulaliki wa pa foni, wa ku nyumba ndi nyumba, wa mwayi, ndi wa poyela

Kodi timabala bwanji zipatso mwa kupilila? (Onani palagilafu 11)

11. (a) Kodi fanizo la wofesa mbewu ligwilizana bwanji na nchito yathu yolalikila? (b) Timabala bwanji mbewu zatsopano za Ufumu?

11 Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyelekezele kuti zaka zambili m’mbuyomo, a Mboni za Yehova kapena makolo athu acikhristu anatilalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo anakondwela poona kuti tinali na mtima wabwino ndipo tinalandila uthenga wa Ufumu umene uli ngati mbewu. Ndipo mofanana ndi nthaka yabwino ya m’fanizo la Yesu, tinalandila uthengawo na kuukhulupilila. Zotulukapo zake, uthenga wa Ufumu umene uli ngati mbewu unazika mizu mumtima mwathu na kukula n’kukhala monga mmela wa tiligu. Patapita nthawi, tinakhala wokonzeka kubala zipatso. Ndipo monga mmene taonela, zipatso zimene mmela wa tiligu umabala si tummela twatsopano tung’ono-tung’ono. Koma umabala mbewu. N’cimodzi-modzi na ise. Zipatso zimene timabala si ophunzila atsopano, koma ni mbewu zatsopano za Ufumu.d Kodi timabala bwanji mbewu zatsopano za Ufumu? Mwa kulalikila uthenga wa Ufumu. Nthawi iliyonse pamene tilengeza uthenga wa Ufumu, timakhala ngati tikufesa mbewu zolingana ndi zimene zinafesedwa mumtima mwathu. (Luka 6:45; 8:1) Conco, fanizo la Yesu la wofesa mbewu litiphunzitsa kuti malinga ngati tipitiliza kulalikila uthenga wa Ufumu, ndiye kuti ‘tikubala zipatso mwa kupilila.’

12. (a) Tingaphunzile ciani m’fanizo la Yesu la mpesa ndi la wofesa mbewu? (b) Nanga zimene taphunzilazo zakukhudzani bwanji?

12 Kodi tingaphunzile ciani m’fanizo la Yesu la mpesa ndi la wofesa mbewu? Mafanizo amenewa atithandiza kuona kuti kubala zipatso sikudalila mmene anthu a m’gawo lathu amalabadilila uthenga wa Ufumu tikawalalikila. Koma kumadalila kukhulupilika kwathu pa nchitoyi. Paulo anakamba mfundo imodzi-modziyo, pamene anati: “Aliyense payekha adzalandila mphoto yake mogwilizana ndi nchito yake.” (1 Akor. 3:8) Inde, tidzalandila madalitso malinga na nchito imene timagwila, osati zotulukapo za nchitoyo. Mlongo Matilda, amene watumikila monga mpainiya kwa zaka 20, anati: “Zimanikondweletsa kudziŵa kuti Yehova adzatidalitsa cifukwa ca nchito imene timagwila modzipeleka.”

N’CIANI CINGATITHANDIZE KUBALA ZIPATSO MOPILILA?

13, 14. Malinga na Aroma 10:1, 2, ni zifukwa ziti zimene zinacititsa Paulo kusaleka kulalikila kwa anthu amene sanali kulandila uthenga wa Ufumu?

13 N’ciani cimene cingatithandize kupitiliza kubala zipatso mopilila? Monga mmene taonela, Paulo anapwetekedwa mtima poona mmene Ayuda anali kutsutsila uthenga wa Ufumu. Olo zinali conco, iye sanaleke kuwalalikila. Onani zimene iye analemba m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma pofotokoza mmene anali kuonela Ayuda. Iye anati: “Cimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzelo langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. Pakuti ndikuwacitila umboni kuti ndi odzipeleka potumikila Mulungu, koma samudziŵa molondola.” (Aroma 10:1, 2) Kodi Paulo anafotokoza zifukwa ziti zimene anapitilizila kugwila nchito yake yolalikila?

14 Coyamba, Paulo anakamba kuti anapitiliza kulalikila kwa Ayuda cifukwa anali ‘kufunitsitsa mumtima mwake’ kucita zimenezo. Iye anali kufunitsitsa kuti Ayuda ena akapulumuke. (Aroma 11:13, 14) Caciŵili, Paulo anakamba za ‘pembedzelo lake kwa Mulungu,’ kaamba ka Ayuda. Iye anali kucondelela Mulungu m’pemphelo kuti athandize Ayuda kulabadila uthenga wa Ufumu. Cacitatu, Paulo anakamba kuti Ayuda anali “odzipeleka potumikila Mulungu.” Iye anaona kuti anthu amenewo anali na mtima wofuna kucita zabwino. Paulo anali kudziŵa kuti anthu oona mtima komanso odzipeleka pa zinthu zabwino, angathe kusintha n’kukhala otsatila a Khristu acangu.

15. Tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? Fotokozani zitsanzo.

15 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? Coyamba, tiyenela kuyesetsa na mtima wonse kusakila anthu ‘amene ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ Caciŵili, tiyenela kucondelela Yehova m’pemphelo kuti atsegule mitima ya anthu oona mtima. (Mac. 13:48; 16:14) Silvana, mpainiya amene watumikila kwa zaka pafupi-fupi 30, anati: “Nikalibe kufika pa nyumba ya munthu m’gawo langa, nimapemphela kwa Yehova kuti anithandize kukhala na maganizo oyenelela.” Timapemphelanso kwa Mulungu kuti, kupitila mwa angelo, atithandize kupeza anthu oona mtima. (Mat. 10:11-13; Chiv. 14:6) Robert, amene watumikila monga mpainiya kwa zaka zoposa 30, anati: “Kuseŵenzela pamodzi na angelo amene amadziŵa bwino zocitika mu umoyo wa anthu n’kokondweletsa.” Cacitatu, timayesetsa kuona zabwino mwa anthu, kuphatikizapo zizindikilo zoonetsa kuti angathe kukhala atumiki a Mulungu. Carl, mkulu amene anabatizika zaka zoposa 50 m’mbuyomo anati, “Nimayesetsa kuona zizindikilo zilizonse zoonetsa kuti munthu ni woona mtima, monga kumwetulila, nkhope ya ubwenzi, kapena funso locokela pansi pa mtima.” Inde, monga Paulo, tingapitilize kubala zipatso mopilila.

“DZANJA LAKO LISAPUME”

16, 17. (a) N’ciani cimene tiphunzilapo pa malangizo a pa Mlaliki 11:6? (b) Fotokozani citsanzo coonetsa mmene nchito yathu yofesa mbewu za Ufumu imakhudzila anthu amene amationa.

16 Ngakhale zioneke kuti uthenga wa Ufumu umene timalalikila suwafika pa mtima anthu, sitiyenela kudelela mphamvu ya uthenga umenewu. (Ŵelengani Mlaliki 11:6.) N’zoona kuti anthu ambili samvetsela uthenga wathu. Ngakhale n’conco, iwo amaona zimene timacita. Amaona kavalidwe kathu kabwino, khalidwe laulemu, na mtima wathu waubwenzi. M’kupita kwa nthawi, khalidwe lathu labwino lingathandize anthu ena kusintha maganizo awo olakwika ponena za Mboni za Yehova. M’bale Sergio na mlongo Olinda, amene tawachula poyamba paja, anadzionela okha kusintha kwa conco.

17 M’bale Sergio anati: “Kwa kanthawi ndithu, sitinali kupita pa malo athu ocitila ulaliki wa poyela cifukwa codwala. Tsiku lina titapitanso pa malowo, munthu wina wopita na njila anatifunsa kuti, ‘N’cifukwa ninji simunali kuoneka? Tinakusowani.’” Nayenso mlongo Olinda mwacimwemwe anati: “Madilaiva a basi anali kutikwezela manja, ndipo ena anali kukamba mokweza ali m’motoka yawo kuti, ‘Mucita nchito yabwino!’ Ena a iwo anatipempha magazini.” Tsiku lina, banjali linacita cidwi pamene munthu wina anaima pa kasitandi kawo ka ulaliki na kuwapatsa maluwa okongola. Komanso munthuyo anawayamikila kaamba ka nchito imene amagwila.

18. Kodi mwatsimikiza mtima ‘kubala zipatso mwa kupilila’? Cifukwa ciani?

18 Sitiyenela kulola ‘dzanja lathu kupuma’ pa nchito yofesa mbewu za Ufumu. Tikatelo, tidzakhalabe na mwayi wamtengo wapatali wocitila “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Koposa zonse, tidzakhala na cimwemwe coculuka, cimene cimabwela cifukwa codziŵa kuti Yehova amatikonda, popeza iye amakonda onse amene ‘amabala zipatso mwa kupilila!’

a Yesu nayenso anavomeleza kuti kulalikila m’gawo la “kwawo” kunali kovuta. Mfundo imeneyi inalembewa m’mabuku onse anayi a Uthenga Wabwino.—Mat. 13:57; Maliko 6:4; Luka 4:24; Yoh. 4:44.

b Olo kuti nthambi za m’fanizoli ziimila Akhristu amene adzakhala na moyo kumwamba, fanizoli lili na mfundo zopindulitsa kwa atumiki onse a Mulungu.

c “Kubala zipatso” kungatanthauzenso kukhala na “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. Koma m’nkhani ino na yokonkhapo, tidzakambilana kwambili za kubala “cipatso ca milomo yathu” kapena kuti kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu.—Agal. 5:22, 23; Aheb. 13:15.

d Panthawi ina, Yesu anayelekezela nchito yopanga ophunzila na nchito yofesa na kukolola mbewu.—Mat. 9:37; Yoh. 4:35-38.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani