Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda September-October
“Mukaona mavuto amene timakumana nao paumoyo, kodi muganiza kuti mau a Yesu akuti tisade nkhawa ndi othandiza? [Ŵelengani Mateyu 6:25, ndipo yembekezani ayankhe.] Magazini ya Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza mmene kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo kungakuthandizileni kucepetsa nkhawa zokhudza ndalama, mavuto a m’banja ndi mavuto aumwini.”
Galamukani! October
“Tikuceza ndi anthu mwacidule kaamba kakuti ambili amadzifunsa cifukwa cake Mulungu amalola anthu kuvutika. Kodi mukuona kuti kufunsa Mulungu funso limeneli n’kupanda ulemu? [Yembekezani ayankhe.] Munthu wokhulupilika Yobu nayenso anafuna kufunsa Mulungu. [Ŵelengani Yobu 23:3-5.] Magaziniyi ikufotokoza mafunso atatu amene anthu ambili angakonde kufunsa Mulungu, ngati angakhale ndi mpata wocita zimenezo. Ndipo ikufotokozanso mayankho okhutilitsa a m’Baibulo.”