CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 20-21
“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
Nthawi za m’Baibo, asodzi oleza mtima, akhama, komanso okonzeka kupilila mavuto pa nchito yawo anali kugwila nsomba zambili. (w12 8/1 mape. 18-20) Makhalidwe amenewa anali othandiza kwa Petulo kuti akhale msodzi wabwino wa anthu. Komabe, iye anafunika kusankha cimene adzaika patsogolo mu umoyo wake, kaya nchito yake yakuthupi imene anali kukonda kapena nchito yauzimu yodyetsa otsatila a Yesu.
Ni zinthu ziti zimene mwasintha mu umoyo wanu kuti muike zinthu za Ufumu patsogolo?