LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 May tsa. 2
  • “Sitikubwelela M’mbuyo”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Sitikubwelela M’mbuyo”
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Zamkatimu
    Galamuka!—2022
  • Yehova Amathandiza Odwala
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • M’kope Ino ya Galamuka!
    Galamuka!—2022
  • Mpaka Pamene Akufa Adzaukitsidwa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 May tsa. 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 4-6

“Sitikubwelela M’mbuyo”

4:16-18

M’bale ali ku okisijini, ndipo akuganizila mmene umoyo udzakhalila m’dziko latsopano

Yelekezelani kuti mabanja aŵili akukhala m’nyumba imodzi koma yamakomo aŵili osiyana. Nyumbayo niyakale komanso yowonongeka. Banja loyamba ni lokwinyilila komanso losakondwa kukhala m’nyumbayo, ndipo m’pomveka. Koma banja laciŵili ni lacimwemwe. Cifukwa ciani? Cifukwa posacedwa lidzakukila m’nyumba yatsopano yokongola.

Olo kuti “cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zoŵaŵa mpaka pano,” atumiki a Yehova ali monga banja laciŵili lija. Ali na ciyembekezo cimene cimaŵapatsa cimwemwe. (Aroma 8:22) Pali pano tili na mavuto amene tikukumana nawo. Palinso mavuto amene takhala tikukumana nawo kwa zaka zambili. Mavuto onsewa ni “akanthawi ndipo ndi opepuka” tikawayelekezela na moyo wosatha umene Mulungu adzatipatsa m’dziko latsopano. Kusumika maganizo athu pa madalitso a kutsogolo mu Ufumu wa Mulungu, kudzatipatsa cimwemwe, ndipo sitidzataya mtima.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani