Salimo
Salimo la Davide.
א [Aleph]
2 Iwo adzafota mwamsanga ngati udzu+
Ndipo adzanyala ngati msipu wobiriwira.
ב [Beth]
3 Uzikhulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino.+
Ukhale padziko lapansi* ndipo uzichita zinthu mokhulupirika.+
4 Uzisangalala* chifukwa cha Yehova,
Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.
ג [Gimel]
6 Iye adzachititsa kuti kulungama kwako kuwale ngati mʼmawa,
Ndipo chilungamo chako adzachichititsa kuti chiwale ngati dzuwa masana.
ד [Daleth]
7 Khala chete pamaso pa Yehova+
Ndipo umuyembekezere moleza mtima.
Usakhumudwe ndi munthu
Amene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+
ה [He]
ו [Waw]
10 Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.+
Udzayangʼana pamene ankakhala,
Ndipo sadzapezekapo.+
ז [Zayin]
12 Munthu woipa amakonzera chiwembu munthu wolungama,+
Ndipo amamukukutira mano.
13 Koma Yehova adzamuseka,
Chifukwa akudziwa kuti mapeto ake adzafika.+
ח [Heth]
14 Oipa asolola malupanga awo ndipo akunga mauta* awo,
Kuti agwetse oponderezedwa ndi osauka,
Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma lupanga lawo lidzalasa mtima wawo womwe,+
Mauta awo adzathyoledwa.
ט [Teth]
16 Zinthu zochepa zimene munthu wolungama ali nazo ndi zabwino
Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+
17 Chifukwa manja a anthu oipa adzathyoledwa,
Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.
י [Yod]
18 Yehova amadziwa mavuto amene anthu osalakwa akukumana nawo,*
Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+
19 Pa nthawi ya tsoka sadzachita manyazi,
Ndipo pa nthawi ya njala adzakhala ndi chakudya chochuluka.
כ [Kaph]
20 Koma oipa onse adzatheratu,+
Adani a Yehova adzasowa mofulumira ngati malo okongola odyetsera ziweto amene msipu wake wobiriwira suchedwa kufota.
Iwo adzatha mofulumira ngati utsi.
ל [Lamed]
21 Munthu woipa amabwereka zinthu za ena koma osabweza,
Koma wolungama amakhala wowolowa manja* ndipo amagawira ena zinthu zake.+
22 Anthu amene Mulungu wawadalitsa adzalandira dziko lapansi,
Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+
מ [Mem]
נ [Nun]
25 Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,
Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+
Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+
26 Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+
Ndipo ana ake adzalandira madalitso.
ס [Samekh]
27 Pewani kuchita zoipa ndipo muzichita zabwino,+
Mukatero mudzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.
28 Chifukwa Yehova amakonda chilungamo,
Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+
ע [Ayin]
פ [Pe]
30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,*
Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+
צ [Tsade]
32 Woipa amayangʼanitsitsa munthu wolungama,
Ndipo amafuna kuti amuphe.
ק [Qoph]
34 Yembekezera Yehova ndi kutsatira njira zake,
Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.
Oipa akamadzaphedwa,+ iwe udzaona.+
ר [Resh]
35 Ine ndaona munthu wankhanza komanso woipa
Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+
ש [Sin]
37 Onani munthu wosalakwa,*
Ndipo yangʼanitsitsani munthu wolungama,+
Chifukwa tsogolo la munthu ameneyo lidzakhala lamtendere.+
38 Koma anthu onse ochimwa adzawonongedwa.
Mʼtsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+
ת [Taw]
39 Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+
Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.+
40 Yehova adzawathandiza nʼkuwapulumutsa.+
Adzawalanditsa kwa oipa nʼkuwapulumutsa,
Chifukwa athawira kwa iye.+