Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Nahum 1:1-3:19
  • Nahumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nahumu
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nahumu

NAHUMU

1 Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu* wa ku Elikosi:

 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.

Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake.+

Yehova amabwezera adani ake,

Ndipo adani ake amawasungira mkwiyo.

 3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+

Koma Yehova salephera kulanga munthu woyenera kulangidwa.+

Njira yake ili mumphepo yowononga ndiponso yamkuntho.

Ndipo mitambo ili ngati fumbi lopondapo mapazi ake.+

 4 Amadzudzula nyanja+ ndiponso kuiphwetsa.

Ndipo amaumitsa mitsinje yonse.+

Zomera za ku Basana ndi za ku Karimeli zimafota,+

Nawonso maluwa a ku Lebanoni amafota.

 5 Mapiri akuluakulu amagwedezeka chifukwa cha iye.

Ndipo mapiri angʼonoangʼono amasungunuka.+

Dziko lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha nkhope yake

Pamodzi ndi nthaka komanso zinthu zonse zokhala mʼdzikomo.+

 6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+

Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+

Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto,

Ndipo miyala idzaphwanyidwa chifukwa cha iye.

 7 Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo pa nthawi yamavuto.+

Amadziwa* amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+

 8 Adzafafaniza mzinda* umenewo ndi madzi osefukira,

Ndipo mdima udzathamangitsa adani ake.

 9 Kodi Yehova mungamukonzere chiwembu chotani?

Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso.

Sipadzakhalanso masautso.+

10 Iwo alukanalukana ngati minga,

Ndipo ali ngati anthu oledzera.

Koma adzawotchedwa ngati mapesi ouma.

11 Mwa iwe mudzatuluka winawake amene adzakonzera Yehova chiwembu,

Ndiponso kupereka malangizo achabechabe.

12 Yehova wanena kuti:

“Ngakhale kuti iwo anali ndi mphamvu zambiri komanso anali ambiri,

Adzadulidwa ndipo sadzakhalaponso.*

Ndakusautsa,* koma sindidzakusautsanso.

13 Tsopano ndidzathyola goli lake nʼkulichotsa pa iwe,+

Ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo.

14 Ponena za iwe,* Yehova walamula kuti,

‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako.

Ndidzachotsa zifaniziro zosema ndi zifaniziro zachitsulo mʼnyumba* za milungu yako.

Ndidzakukonzera manda chifukwa uli ngati chinthu chonyansa.’

15 Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.

Iye akulengeza za mtendere.+

Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza,

Chifukwa munthu aliyense wopanda pake sadzadutsa pakati pako.

Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”

2 Womwaza wabwera kudzalimbana nawe.*+

Teteza malo amene ali ndi mpanda wolimba kwambiri.

Londera njira yako.

Konzekera kumenya nkhondo* ndipo sonkhanitsa mphamvu zako zonse.

 2 Chifukwa Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.

Limodzi ndi ulemerero wa Isiraeli.

Popeza owononga awawononga,+

Ndipo asakaza mphukira zawo.

 3 Zishango za amuna amphamvu zaviikidwa mu utoto wofiira,

Asilikali ake avala zovala zofiira kwambiri.

Zitsulo za magaleta ake ankhondo zili waliwali ngati moto,

Pa tsiku limene akukonzekera nkhondo.

Ndipo mikondo ya mitengo ya junipa* aipukuta.

 4 Magaleta awo ankhondo akuthamanga kwambiri mʼmisewu.

Iwo akuthamanga uku ndi uku mʼmabwalo a mzinda.

Akuwala ngati matochi komanso kungʼanima ngati mphezi.

 5 Mfumu idzaitanitsa asilikali ake amaudindo akuluakulu.

Iwo azidzapunthwa pamene akuthamanga,

Adzathamangira kumpanda wa mzinda.

Iwo adzakhwimitsa chitetezo.

 6 Zotsekera madzi amʼmitsinje zidzatsegulidwa,

Ndipo nyumba yachifumu idzagwa.

 7 Nkhani imeneyi ndi yotsimikizirika. Mzindawo wavulidwa nʼkuchititsidwa manyazi,

Anthu ake atengedwa ndipo akapolo ake aakazi akulira.

Akumveka ngati nkhunda pamene akudziguguda pamtima.

 8 Kuyambira kalekale, Nineve+ anali ngati dziwe la madzi,

Koma tsopano anthu ake akuthawa.

Ena akufuula kuti: “Taimani! Taimani!”

Koma palibe amene akubwerera.+

 9 Tengani siliva wawo, tengani golide,

Iwo ali ndi chuma chankhaninkhani.

Ali ndi zinthu zosiyanasiyana zamtengo wapatali.

10 Mzindawu watsala wopanda kanthu, wawonongedwa ndipo wakhala bwinja.+

Mitima yawo yasungunuka ndi mantha, mawondo ndi ziuno zawo zikunjenjemera.

Nkhope zawo zonse zili ndi nkhawa.

11 Ali kuti malo amene mikango yamphamvu+ inkadyerako?

Malo amene mikango inkatsogolera ana ake,

Popanda aliyense woiwopseza?

12 Mkango unkakhadzula nyama yokwanira kuti udyetse ana ake.

Ndipo unkapha nyama kuti upatse mikango yaikazi.

Mapanga ake ankakhala odzaza ndi nyama,

Ndipo mʼmalo ake obisalamo munkakhala nyama zokhadzulakhadzula.

13 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, “Ine ndikukuukira.+

Nditentha magaleta ako ankhondo mpaka akhala phulusa.+

Ndipo lupanga lidzapha mikango yako yamphamvu.

Ndidzachititsa kuti usagwirenso nyama padziko lapansi,

Ndipo mawu a anthu amene umawatuma kukanena uthenga sadzamvekanso.”+

3 Tsoka mzinda wokhetsa magazi!

Mzindawo wadzaza ndi chinyengo ndi zauchifwamba,

Ndipo nthawi zonse umatenga zinthu za anthu omwe wagonjetsa.

 2 Kukumveka kulira kwa mikwapulo ndiponso phokoso la mawilo,

Mgugu wa mahatchi* ndi kuthamanga kwa magaleta.

 3 Komanso pali asilikali okwera pamahatchi, malupanga owala ndiponso mikondo yonyezimira.

Palinso anthu ambiri ophedwa komanso milu ya mitembo,

Moti mitembo ili paliponse.

Anthu akupunthwa pamitemboyo.

 4 Zili choncho chifukwa cha kuchuluka kwa zochita zake zauhule.

Iye ndi mkazi wokongola mochititsa kaso ndiponso waluso lamatsenga.

Ndipo amakopa mitundu ya anthu ndi uhule wake komanso mabanja ndi zochita zake zamatsenga.

 5 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Taona! Ine ndikukuukira,*+

Ndipo ndidzakuvula zovala zako nʼkukuphimba nazo kumaso.

Ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ione maliseche ako,

Ndipo maufumu adzaona kuti wachititsidwa manyazi.

 6 Ndidzakuponyera zinthu zonyansa.

Ndidzakuchititsa kukhala chinthu chonyozeka,

Ndiponso chochititsa mantha.+

 7 Aliyense wokuona adzakuthawa+ ndipo adzanena kuti,

‘Nineve wawonongedwa!

Ndani adzamumvere chisoni?’

Kodi anthu oti akutonthoze ndidzawapeza kuti?

 8 Kodi iwe uli pabwino kuposa No-amoni*+ amene anali pafupi ndi ngalande zochokera mumtsinje wa Nailo?+

Iye anazunguliridwa ndi madzi.

Nyanja inali chuma chake ndiponso khoma lake.

 9 Mphamvu zake zopanda malire zinkachokera ku Itiyopiya ndi ku Iguputo.

Anthu a ku Puti+ ndi a ku Libiya ankamuthandiza.+

10 Koma No-amoni anatengedwa kupita kudziko lina,

Anamugwira nʼkupita naye ku ukapolo.+

Ana ake anaphwanyidwaphwanyidwa mʼmakona a misewu yonse.

Ndipo anthu ake olemekezeka anawachitira maere.

Anthu ake onse otchuka amangidwa mʼmatangadza.

11 Iwenso udzaledzera,+

Ndipo udzabisala.

Udzafunafuna malo oti uthawireko kuti mdani wako asakupeze.

12 Malo ako onse okhala ndi mipanda yolimba ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi nkhuyu zoyambirira kupsa.

Munthu akagwedeza mitengoyo, nkhuyu zakezo zimagwera mʼkamwa mwa munthu wozidya.

13 Taona! Asilikali ako ali ngati akazi.

Mageti a dziko lako adzatsegulidwa kuti adani ako alowemo.

Ndipo moto udzawotcheratu mipiringidzo ya mageti ako.

14 Tunga madzi pokonzekera nthawi imene adani adzakuzungulire.+

Limbitsa malo ako okhala ndi mipanda yolimba.

Lowa mʼmatope ndi kupondaponda dothi.

Gwira chikombole.

15 Koma ngakhale utero, moto udzakuwotcheratu.

Lupanga lidzakudula.+

Ndipo lidzakudya ngati mmene dzombe lingʼonolingʼono limadyera zomera.+

Dzichulukitseni ngati dzombe lingʼonolingʼono,

Dzichulukitseni ngati dzombe.

16 Iwe wachulukitsa amalonda ako kuposa nyenyezi zakumwamba.

Dzombe lingʼonolingʼono limafundula* kenako nʼkuulukira kutali.

17 Alonda ako ali ngati dzombe.

Ndipo akapitawo ako ali ngati gulu la dzombe.

Pa tsiku lozizira limakhala mʼmakoma.

Koma dzuwa likawala, dzombelo limauluka nʼkupita kutali.

Ndipo palibe amene amadziwa kumene lapita.

18 Abusa ako ayamba kuodzera, iwe mfumu ya Asuri,

Ndipo anthu ako olemekezeka akungokhala mʼnyumba zawo.

Anthu ako amwazikana mʼmapiri,

Ndipo palibe amene akuwasonkhanitsa.+

19 Mavuto ako sadzakupatsa mpata wopuma.

Bala lako lafika posachiritsika.

Onse amene adzamve za iwe, adzawomba mʼmanja.+

Chifukwa palibe amene sanavutike ndi zoipa zako zosatha.”+

Kutanthauza “Wotonthoza.”

Kapena kuti, “Amasamalira.”

Umenewu ndi mzinda wa Nineve.

Mabaibulo ena amati, “adzadutsa.”

Kutanthauza Yuda.

Kutanthauza Asuri.

Kapena kuti, “mu akachisi.”

Kutanthauza Nineve.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Limbitsa chiuno chako.”

Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.

Ena amati “mahosi.”

Kutanthauza Nineve.

Kutanthauza Thebesi.

Kapena kuti, “limasuwa.”

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani