Nehemiya 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+ Salimo 78:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iye anang’amba miyala m’chipululu+Kuti awapatse madzi akumwa ochuluka ngati a m’nyanja.+ Salimo 105:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+ Salimo 114:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,+Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.+ Yesaya 43:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Zilombo zakutchire zidzanditamanda.+ Mimbulu ndi nthiwatiwa+ zidzanditamanda chifukwa ndidzapereka madzi ndi mitsinje m’chipululu,+ kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe, Yesaya 48:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+
15 Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+
41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+
8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,+Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.+
20 Zilombo zakutchire zidzanditamanda.+ Mimbulu ndi nthiwatiwa+ zidzanditamanda chifukwa ndidzapereka madzi ndi mitsinje m’chipululu,+ kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe,
21 Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+