Genesis 49:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ Salimo 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+ Salimo 72:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Mafumu onse adzamugwadira ndi kumuweramira.+Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.+ Chivumbulutso 6:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Nditayang’ana, ndinaona hatchi* yoyera.+ Wokwerapo+ wake ananyamula uta.+ Iye anapatsidwa chisoti chachifumu,+ ndi kupita kukagonjetsa adani ake+ ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.+ Chivumbulutso 19:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse.
10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+
9 Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+
2 Nditayang’ana, ndinaona hatchi* yoyera.+ Wokwerapo+ wake ananyamula uta.+ Iye anapatsidwa chisoti chachifumu,+ ndi kupita kukagonjetsa adani ake+ ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.+
15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse.