20Tsopano khamu lonse la ana a Isiraeli linafika m’chipululu cha Zini,+ m’mwezi woyamba, ndipo anthuwo anakhala ku Kadesi.+ Kumeneko n’kumene Miriamu+ anafera n’kuikidwa m’manda.
14 chifukwa amuna inu munapandukira mawu anga m’chipululu cha Zini, pa nthawi imene khamu lija linakangana nanu.+ Munalephera kundilemekeza+ pa madzi amene anatuluka patsogolo pa khamulo, madzi a Meriba+ ku Kadesi,+ m’chipululu cha Zini.”+
51 Izi zili choncho chifukwa anthu inu munachita mosakhulupirika kwa ine+ pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, m’chipululu cha Zini. Ndiponso chifukwa chakuti anthu inu simunandilemekeze pakati pa ana a Isiraeli.+