Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

      Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+

      Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+

  • 2 Samueli 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 N’chifukwa chake ndinudi wokwezeka,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Ngakhale kuti tamva za milungu ina yambirimbiri, palibe Mulungu wina+ koma inu nokha.+

  • 1 Mafumu 8:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu+ amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse,+ inu mumawasungira pangano ndi kukoma mtima kosatha.+

  • Salimo 71:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+

      Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+

      Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+

  • Salimo 86:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+

      Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+

  • Yeremiya 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndithudi palibe aliyense wofanana ndi inu Yehova.+ Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu ndi lalikulu ndi lamphamvu.+

  • Yeremiya 49:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango+ kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano. Iye adzafika pamalo otetezeka+ odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzamuthamangitsa pamalowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo, pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena