Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 1:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Onani, Yehova Mulungu wanu wakusiyirani dzikoli.+ Pitani, litengeni kuti likhale lanu, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakuuzirani.+ Musaope kapena kuchita mantha.’+

  • Deuteronomo 7:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Usaiope.+ Nthawi zonse uzikumbukira zimene Yehova Mulungu wako anachitira Farao ndi Iguputo yense.+

  • Deuteronomo 31:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+

  • Yoswa 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+

  • Salimo 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+

      Ndingaopenso ndani?+

      Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+

      Ndingachitenso mantha ndi ndani?+

  • Yesaya 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Taonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa.+ Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+ pakuti Ya* Yehova ndiye mphamvu zanga+ ndi nyonga zanga,+ ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+

  • Aroma 8:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena