Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Yesaya 65:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Sharoni+ adzakhala malo odyetserapo nkhosa.+ Chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ng’ombe za anthu anga amene andifunafuna.+

  • Yeremiya 50:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli+ ndi ku Basana.+ Iye adzakhutira m’madera amapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+

  • Ezekieli 34:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa+ pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko ena ndi kuzibweretsa m’dziko lawo.+ Ndidzazidyetsa m’mapiri a ku Isiraeli, m’mphepete mwa mitsinje komanso m’malo onse a m’dzikolo okhalako anthu.+

  • Ezekieli 34:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Nkhosazo ndidzazidyetsera m’malo a msipu wabwino ndipo zizidzakhala m’mapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi m’malo abwino kwambiri.+ Zizidzadya msipu wobiriwira bwino m’mapiri a ku Isiraeli.”

  • Mika 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.+ Ndidzasonkhanitsa otsala a Isiraeli.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola, komanso ngati gulu la ziweto limene lili pamalo amsipu.+ Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena