Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 106:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+

      Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+

      Kuti titamande dzina lanu loyera,+

      Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+

  • Yesaya 65:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana,+ ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo yemwe adzalandire cholowa cha mapiri anga.+ Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapatsidwa dziko lamapirilo,+ ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+

  • Yeremiya 23:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Ine ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera m’mayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+

  • Yeremiya 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+

  • Ezekieli 11:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera m’mayiko amene ndinakubalalitsirani, ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.”+

  • Ezekieli 28:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena