Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 11:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 M’tsiku limenelo, Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri+ kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,+ ku Hamati ndi m’zilumba za m’nyanja.+

  • Yeremiya 30:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+

  • Yeremiya 32:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 ‘Inetu ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa m’dziko lino ndi kuwachititsa kukhala mwamtendere.+

  • Ezekieli 20:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 “‘Ndikadzakulowetsani m’dziko la Isiraeli,+ dziko limene ndinalumbira nditakweza dzanja kuti ndidzalipereka kwa makolo anu, anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+

  • Ezekieli 34:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa+ pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko ena ndi kuzibweretsa m’dziko lawo.+ Ndidzazidyetsa m’mapiri a ku Isiraeli, m’mphepete mwa mitsinje komanso m’malo onse a m’dzikolo okhalako anthu.+

  • Ezekieli 36:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 ‘Ndidzakutengani pakati pa anthu a mitundu ina n’kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko onse. Kenako ndidzakubweretsani m’dziko lanu.+

  • Ezekieli 37:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho losera, uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatsegula manda anu,+ inu anthu anga, ndipo ndidzakutulutsani m’mandamo ndi kukubweretsani m’dziko la Isiraeli.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena