Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 14:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Chifukwa chakuti iweyo wagonjetsa+ Edomu, mtima wako wayamba kudzikuza.+ Sangalala ndi ulemu umene wapeza+ ndipo khala m’nyumba mwako momwemo. N’chifukwa chiyani ukufuna kumenya nkhondo+ pamene zinthu sizikukuyendera bwino?+ Iweyo ndi Ayuda amene uli nawowo mugonja.”

  • 2 Mbiri 26:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+

  • Miyambo 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+

  • Ezekieli 28:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:

      “‘“Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ndipo ukunena kuti, ‘Ndine mulungu.+ Ndakhala pampando wa mulungu+ pakatikati pa nyanja,’+ ngakhale kuti ndiwe munthu wochokera kufumbi+ osati mulungu,+ ndipo umadziona ngati mulungu . . .

  • Danieli 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzitukumula ndiponso pamene anaumitsa mtima wake ndi kuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena