19 Ndiyeno Ayuda anafika kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo ndipo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala ndi kumukokera kunja kwa mzindawo, poganiza kuti wafa.+
2 Koma mukudziwa kuti choyamba titavutika+ ndi kuchitidwa zachipongwe+ ku Filipi,+ tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula+ kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.
11 Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo,+ ndi ku Lusitara.+ Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.+