Yobu
11 Tsopano Zofari wa ku Naama+ anayankha kuti:
2 “Kodi mawu ambirimbiri anganenedwe osayankhidwa?
Kapena kodi munthu wongodzitama angakhale wosalakwa?
3 Kodi zolankhula zako zopanda pake zingachititse anthu kukhala chete?
Ndipo kodi upitirizabe kunyoza popanda wokudzudzula?+
4 Komanso ukunena kuti, ‘Zimene ndimaphunzitsa + ndi zoyera,
Ndipo Mulungu amandiona kuti ndine woyera.’+
6 Bwenzi atakuuza chinsinsi cha nzeru,
Chifukwa zinthu za nzeru ndiponso zopindulitsa n’zambiri.
Komanso bwenzi utadziwa kuti Mulungu wachititsa kuti zolakwa zako zina ziiwalike.+
7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,+
Kapena kodi ungadziwe mapeto a kukula kwa Wamphamvuyonse?
8 N’zofika kutali kuposa kumwamba. Ungachite chiyani iwe?
N’zozama kuposa Manda.+ Ungadziwe chiyani iwe?
9 N’zazitali kuposa kutalika kwa dziko lapansi,
N’zazikulu kuposa nyanja.
10 Iye akadutsa n’kupereka winawake,
N’kumuitanitsira bwalo, ndani angatsutsane naye?
12 Ngati mbidzi yooneka ngati bulu ingabadwe munthu,
Ndiye kuti munthu wanzeru zoperewera angamvetse zinthu.
13 Ngati iweyo ungakonzekeretsedi mtima wako,
Ndi kutambasulira manja ako kwa iye,+
14 Ndiponso ngati m’manja mwako muli choipa, uchikankhire kutali,
Ndipo m’mahema ako musakhale zopanda chilungamo.
16 Pakuti iweyo udzaiwala mavuto.
Ndipo udzawakumbukira ngati madzi amene anadutsa.