Yobu
18 Tsopano Bilidadi wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Kodi zikutengerani nthawi yaitali bwanji anthu inu kuti musiye kulankhula?
Muyenera kumvetsa kuti kenako tilankhule.
4 Iwe amene ukukhadzula moyo wako mumkwiyo wako,
Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe?
Kapena mwala ungasunthe pamalo ake chifukwa cha iwe?
10 Chingwe choti chim’kole chabisidwa pansi,
Ndipo msampha woti um’gwire uli panjira yake.
11 Paliponse, zoopsa zadzidzidzi zimamuchititsa mantha,+
Ndipo zimamuthamangitsa zili pafupi naye kwambiri.
13 Mwana woyamba wa imfa azidzanyotsola khungu la munthuyo n’kumadya.
Iye adzadya ziwalo zake.
18 Adzamuchotsa powala n’kumukankhira kumdima.
Adzamuthamangitsa panthaka ya padziko lapansi.
19 Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,+
Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala monga mlendo.
20 Pa tsiku la tsoka lake anthu a Kumadzulo adzayang’ana modabwa,
Ndipo anthu a Kum’mawa adzanjenjemera.
21 Izi n’zimene zimachitikira malo okhala munthu woipa,
Ndipo awa ndiwo malo a munthu wosadziwa Mulungu.”