Nyimbo ya Solomo
4 “Ndiwe wokongola kwabasi,+ wokondedwa wanga. Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa+ munsalu yako yophimba kumutuyo.+ Tsitsi lako likuoneka ngati gulu la mbuzi+ zimene zikudumphadumpha potsetsereka kuchokera kudera lamapiri la Giliyadi.+ 2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zazikazi zomwe angozimeta kumene,+ zimene zikuchokera kozisambitsa, zonse zitabereka mapasa, popanda imene ana ake afa. 3 Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri, ndipo kulankhula kwako n’kosangalatsa.+ M’mbali mwa mutu wako muli ngati khangaza* logamphula pakati, munsalu yako yophimba kumutuyo.+ 4 Khosi lako+ lili ngati nsanja+ ya Davide. Lili ngati nsanja yomangidwa ndi miyala yokhala m’mizeremizere, yomwe akolekapo zishango 1,000, zishango zonse zozungulira+ za amuna amphamvu. 5 Mabere ako awiri+ ali ngati ana awiri aang’ono, ngati ana amapasa a insa yaikazi, amene akudya msipu pakati pa maluwa akutchire.”+
6 “Nthawi ya kamphepo kayaziyazi isanakwane+ ndiponso mithunzi isanachoke, ndipita kuphiri la mule ndiponso kuphiri la lubani.”+
7 “Ndiwe wokongola paliponse,+ wokondedwa wanga, ndipo mwa iwe mulibe chilema chilichonse.+ 8 Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,+ tiye tichoke ku Lebanoni.+ Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana, kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri,+ ngakhalenso pamwamba pa phiri la Herimoni.+ Utsetsereke kuchokera m’mapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.* 9 Wachititsa mtima wanga kugunda, iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Wachititsa mtima wanga kugunda ndi diso lako limodzi lokha,+ ndiponso ndi diso limodzi lokha la mkanda wa m’khosi mwako. 10 Chikondi chimene umandisonyeza n’chokoma,+ iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza n’chabwino kuposa vinyo ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola n’koposa zonunkhira za mitundu yonse.+ 11 Milomo yako imangokhalira kukha uchi wapachisa,+ iwe mkwatibwi wanga. Uchi+ ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lako, ndipo kununkhira kwa zovala zako kuli ngati kununkhira+ kwa nkhalango ya Lebanoni. 12 Mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda.+ Iye ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda, ndiponso ngati kasupe wotsekedwa. 13 Khungu lako lili ngati munda wokongola* wokhala ndi mitengo ya makangaza ya zipatso zabwino kwambiri,+ mitengo ya maluwa ofiirira, mitengo ya nado,+ 14 maluwa a safironi,+ mabango onunkhira,+ sinamoni,+ komanso mitengo yosiyanasiyana ya lubani, mule, aloye,+ ndi zonunkhira zonse zabwino kwambiri.+ 15 Khungu lako lilinso ngati kasupe wa m’munda, chitsime cha madzi abwino,+ ndiponso timitsinje tochokera ku Lebanoni.+ 16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto. Bwera, iwe mphepo yakum’mwera.+ Womba pamunda wanga+ kuti kununkhira kwake kumveke.”
“Wachikondi wanga alowe m’munda wake kuti adzadye zipatso zake zokoma kwambiri.”