Yobu
30 “Tsopano anthu amene ndi ana aang’ono poyerekeza ndi ine,+
Akundiseka.+
Anthu amene abambo awo sindikanalola
Kuwaika pamodzi ndi agalu oweta nkhosa zanga.
3 Chifukwa cha njala ndiponso kusowa, iwo ali ngati akufa.
Amatafuna dera lopanda madzi,+
Limene dzulo kunali mphepo yamkuntho ndi chiwonongeko.
4 Iwo anali kubudula chitsamba cha mchere m’tchire,
Ndipo mizu ya timitengo ndiyo inali chakudya chawo.
7 Amalira mokuwa ali pakati pa zitsamba,
Amaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.
8 Ana a munthu wopusa,+ komanso ana a munthu wopanda dzina.
Iwo akwapulidwa n’kuthamangitsidwa m’dziko.
11 Pakuti iye anakhwefula chingwe cha uta wanga n’kunditsitsa,
Ndipo zingwe za pakamwa pa hatchi,* iwo anazisiya zomasula chifukwa cha ine.
12 Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati kagulu ka anthu oipa.
Amasula mapazi anga,
Koma andiikira zopinga zovulaza kwambiri.+
14 Amabwera ngati akudutsa pampata waukulu,
Amakokoloka ndi madzi a mvula yamkuntho.
15 Zoopsa zadzidzidzi zandibwerera.
Ulemerero wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo,
Ndipo chipulumutso changa chapita ngati mtambo.
18 Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu, chovala* changa chimasintha,
Ndipo chimandithina ngati kolala yothina.
19 Iye wanditsitsa mpaka m’dothi,
Moti ndikukhala ngati fumbi ndi phulusa.
22 Mwandiuluza ndi mphepo, mwandinyamula nayo.
Kenako mwandisungunula ndi mkokomo wake.
24 Koma palibe amene amatambasula dzanja lake polimbana ndi mulu wa zinthu zowonongeka.+
Komanso pa kuwonongeka kwa munthu, palibe amene amapempha thandizo la zinthu zimenezo.
25 Ndithu, ndalirira munthu amene zinthu sizikumuyendera bwino.+
Moyo wanga walirira munthu wosauka.+
26 Ngakhale kuti ndinkadikirira zabwino, zoipa n’zimene zinabwera.+
Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima.
27 Matumbo anga anawira ndipo sanakhale chete.
Masiku a masautso anandipeza.
28 Ndinayendayenda mwachisoni+ pamene kunalibe kuwala.
Ndinaimirira mumpingo, ndipo ndinkangofuula popempha thandizo.
30 Khungu langa linakhala lakuda+ ndipo linayoyoka pathupi panga.
Mafupa anga anatentha chifukwa chouma.
31 Zeze wanga anangokhala wolirirapo,
Ndipo chitoliro changa chinangokhala choimbapo mawu a anthu olira.