Yobu
29 Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo kuti:
2 “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili m’miyezi yakale,+
Ngati mmene ndinalili m’masiku amene Mulungu anali kundiyang’anira,+
3 Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,
Pamene ndinkayenda mu mdima iye akundiunikira ndi kuwala kwake.+
4 Ngati mmene ndinalili m’masiku amene ndinali mnyamata,+
Pamene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima, ndipo anali pahema wanga,+
5 Pamene Wamphamvuyonse anali nane,
Pamene antchito anga onse anandizungulira,
6 Pamene ndinkasambitsa mapazi anga m’mafuta a mkaka,
Ndiponso pamene miyala inkanditulutsira mitsinje ya mafuta.+
7 Ndikapita kuchipata cha mzinda,+
Ndinkakonzako malo anga okhala pabwalo la mzinda.+
11 Khutu likamva, linkanena kuti ndine wodala,
Ndipo diso likaona, linkandichitira umboni.
12 Pakuti ndinkapulumutsa wosautsika wopempha thandizo,+
Ndiponso mwana wamasiye* ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+
13 Madalitso+ a munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa ankabwera kwa ine,
Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+
14 Ndinkavala chilungamo, ndipo icho chinkandiveka.+
Chilungamo changa chinali ngati malaya akunja odula manja, ndi nduwira.*
16 Ndinali bambo weniweni kwa osauka,+
Ndipo mlandu wa munthu amene sindinali kumudziwa ndinkaufufuza.+
17 Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+
Ndipo wogwidwa, ndinkamulanditsa kukamwa kwa wochita zoipayo.
20 Ulemerero wanga ndili nawobe,
Ndipo uta umene uli m’manja mwanga uziponya mivi mobwerezabwereza.’