2 Mbiri
36 Kenako anthu a m’dzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya n’kumulonga ufumu ku Yerusalemu m’malo mwa bambo ake.+ 2 Yehoahazi anali ndi zaka 23 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ 3 Koma mfumu ya Iguputo inamuchotsa pa udindo wake ku Yerusalemu,+ n’kulamula dzikolo kuti limupatse matalente 100 a siliva*+ ndi talente imodzi ya golide.* 4 Kuwonjezera apo, mfumu+ ya Iguputo inaika Eliyakimu+ m’bale wa Yehoahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehoahazi m’bale wakeyo, Neko+ anam’tenga n’kupita naye ku Iguputo.+
5 Yehoyakimu+ anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.+ 6 Kenako Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ kudzam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.+ 7 Ziwiya zina+ za m’nyumba ya Yehova, Nebukadinezara+ anapita nazo ku Babulo n’kukaziika m’nyumba yake yachifumu.+ 8 Nkhani zina+ zokhudza Yehoyakimu ndi zonyansa+ zimene anachita, ndiponso zoipa zimene zinapezedwa zokhudza iye, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. Kenako Yehoyakini+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
9 Yehoyakini+ anali ndi zaka 18 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu+ ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10 Kumayambiriro+ kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma+ asilikali ake omwe anakamutenga n’kubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwinozabwino za m’nyumba ya Yehova.+ Kuwonjezera apo, Nebukadinezara analonga ufumu Zedekiya+ yemwe anali m’bale wa bambo ake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+
11 Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ 12 Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova Mulungu wake, ndipo sanadzichepetse+ pamaso pa mneneri+ Yeremiya+ yemwe anapita kwa iye molamulidwa ndi Yehova. 13 Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anapandukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inali itamulumbiritsa kwa Mulungu,+ ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake+ kuti asabwerere kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. 14 Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+
15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake.+ Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo+ ndiponso malo ake okhala.+ 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.
17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ m’nyumba yopatulika.+ Sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu.+ Mulungu anapereka zonse m’manja mwake. 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo. 19 Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona+ ndi kugwetsa mpanda+ wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino,+ mpaka zonse zinawonongedwa.+ 20 Kuwonjezera apo, Nebukadinezara anagwira anthu amene sanaphedwe ndi lupanga ndipo anawatenga kupita nawo ku Babulo.+ Anthuwo anakakhala antchito+ ake ndi a ana ake kufikira pamene ufumu wa Perisiya+ unayamba kulamulira. 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linali kusunga sabata mpaka linakwaniritsa zaka 70.+
22 M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya,+ Yehova analimbikitsa mtima+ wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova+ kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti: 23 “Koresi mfumu ya Perisiya+ wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu m’dziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira,+ Yehova Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite.’”+