Deuteronomo
6 “Tsopano amenewa ndiwo malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu walamula kuti ndikuphunzitseni,+ kuti muzikazitsatira m’dziko limene mukuwolokerako kukalitenga kukhala lanu. 2 Muyenera kuphunzira zimenezi kuti muziopa+ Yehova Mulungu wanu, n’cholinga choti masiku onse a moyo wanu muzisunga mfundo zake ndi malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ ndiponso kuti masiku anu atalike.+ 3 Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira mfundo ndi malamulo ake mosamala,+ kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ ndi kuti muchuluke kwambiri m’dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga mmene Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.+
4 “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.*+ 5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse,+ moyo wako wonse,+ ndi mphamvu zako zonse.+ 6 Ndipo mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako,+ 7 ndi kuwakhomereza mwa ana ako.+ Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona+ ndi podzuka. 8 Uziwamanga padzanja lako+ monga chizindikiro, ndipo azikhala ngati chomanga pamphumi pako,*+ 9 ndiponso uziwalemba pafelemu la khomo la nyumba yako ndi pazipata za mzinda wanu.+
10 “Ndiyeno Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene analumbirira makolo ako Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsa,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yooneka bwino imene sunamange ndiwe,+ 11 yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino zimene sunaikemo ndiwe, ndi zitsime* zimene sunakumbe ndiwe, minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene sunabzale ndiwe, n’kudya ndi kukhuta,+ 12 samala kuti usaiwale+ Yehova amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo. 13 Uziopa Yehova Mulungu wako+ ndi kum’tumikira,+ ndipo uzilumbira pa dzina lake.+ 14 Musatsatire milungu ina, milungu iliyonse ya anthu okuzungulirani,+ 15 (pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi).+ Musatsatire milungu ina kuopera kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu ungakuyakireni,+ ndipo angakufafanizeni padziko lapansi.+
16 “Musamuyese, Yehova Mulungu wanu,+ mmene munamuyesera pa Masa.*+ 17 Muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ maumboni ake+ ndi zigamulo+ zake zimene wakupatsani.+ 18 Ndipo muzichita zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova kuti zikuyendereni bwino,+ ndi kuti mukalowedi m’dziko labwino limene Yehova analumbirira makolo anu,+ ndi kulitenga kukhala lanu, 19 mwa kukankhira adani anu kutali monga mmene Yehova analonjezera.+
20 “Mwana wako akadzakufunsa tsiku lina m’tsogolo+ kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo izi zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani, zimatanthauza chiyani?’ 21 Pamenepo mwana wakoyo udzamuyankhe kuti, ‘Tinakhala akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu.+ 22 Motero Yehova anali kuchita zizindikiro ndi zozizwitsa+ zazikulu ndiponso zodzetsa masoka, mu Iguputo yense, kwa Farao ndi kwa onse a m’nyumba mwake ife tikuona.+ 23 Ndipo anatitulutsa kumeneko kuti atibweretse kuno kudzatipatsa dziko limene analumbirira makolo athu.+ 24 Choncho Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa,+ tiziopa Yehova Mulungu wathu ndi kupindula nthawi zonse,+ kuti tikhale ndi moyo monga mmene zilili lero.+ 25 Ndipo tikatsatira malamulo onsewa monga mmene Yehova Mulungu wathu watilamulira,+ ndiye kuti tikuchita chilungamo+ pamaso pake.’