Aheberi
4 Chotero, popeza lonjezo lolowa mu mpumulo wake lidakalipo,+ samalani kuopera kuti pa nthawi ina, wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+ 2 Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ monga mmenenso unalengezedwera kwa makolo athu.+ Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo,+ chifukwa sanakhale ndi chikhulupiriro+ ngati cha amene anamvera mawuwo.+ 3 Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira+ mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti ntchito zake zinali zitatha+ kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.*+ 4 Pakuti penapake, ponena za tsiku la 7, anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+ 5 Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+
6 Choncho, popeza kuti ena ayenerabe kulowa mu mpumulo umenewo, ndipo amene anali oyamba kuwalalikira uthenga wabwino+ sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+ 7 iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+ 8 Pakuti ngati Yoswa+ anawalowetsa m’malo ampumulo,+ Mulungu sakananenanso pambuyo pake+ za tsiku lina. 9 Chotero mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10 Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu,+ ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake,+ monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.
11 Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+ 12 Pakuti mawu+ a Mulungu ndi amoyo+ ndi amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo+ ndi mzimu,+ komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.+ 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
14 Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+ 15 Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni+ pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16 Choncho, tiyeni tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu+ ndi ufulu wa kulankhula,+ kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.+