Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mkazi wamatsenga musamulole kukhala ndi moyo.+

  • Levitiko 19:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Musamapemphe anthu olankhula ndi mizimu+ kuti akuthandizeni ndipo musamafunse malangizo kwa anthu olosera zamʼtsogolo+ nʼkukuchititsani kukhala odetsedwa. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

  • Levitiko 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Munthu amene wachita zosakhulupirika* podalira anthu olankhulana ndi mizimu+ komanso olosera zamʼtsogolo,+ ndidzadana naye ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+

  • Deuteronomo 18:10-12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+ 11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu.

  • Chivumbulutso 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma anthu amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu,+ achiwerewere,*+ amene amachita zamizimu, olambira mafano ndi anthu onse abodza,+ adzaponyedwa mʼnyanja yoyaka moto ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena