-
Genesis 12:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu nʼkumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbadwa* zako.”+ Choncho Abulamu anamanga guwa lansembe pamalo amene Yehova anaonekera kwa iye. 8 Patapita nthawi, anasamuka pamalopo nʼkupita kudera lamapiri, kumʼmawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga tenti yake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kumʼmawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe+ nʼkuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+
-