Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 18:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova,

      Ndinapitiriza kufuulira Mulungu wanga kuti andithandize.

      Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,+

      Ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+

  • Yona 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Nditatsala pangʼono kufa, ndinakumbukira Yehova.+

      Ndipo pemphero langa linafika kwa inu mʼkachisi wanu woyera.+

  • Mateyu 26:38, 39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Kenako anawauza kuti: “Ine ndikumva chisoni* chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+ 39 Choncho atapita patsogolo pangʼono, anagwada mpaka nkhope yake pansi ndipo anapemphera kuti:+ “Atate wanga, ngati nʼkotheka lolani kuti kapu iyi+ indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+

  • Maliko 15:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Cha mʼma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+

  • Aheberi 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamene Khristu anali padzikoli,* anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi,+ ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena