-
Mateyu 26:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Kenako mmodzi wa ophunzira 12 aja, amene ankadziwika kuti Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu+ 15 nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+ 16 Choncho kuyambira nthawi imeneyo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke.
-