Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 3 John 1-14
  • 3 Yohane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 3 Yohane
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
3 Yohane

Kalata Yachitatu ya Yohane

1 Ine monga mkulu,+ ndikulembera wokondedwa Gayo, amene ndimamukonda kwambiri.+

2 Wokondedwa,+ ndimapemphera kuti zinthu zonse zikuyendere bwino+ ndiponso kuti ukhale ndi thanzi labwino,+ monga mmenenso moyo wako ukuyendera bwino.+ 3 Ndinasangalala kwambiri pamene abale anabwera ndi kupereka umboni wa mmene ukupitira patsogolo m’choonadi, ndipo ndikusangalala chifukwa ukupitirizabe kuyenda m’choonadi.+ 4 Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.+

5 Wokondedwa, ukugwira ntchito mokhulupirika pa chilichonse chimene ukuchitira abale,+ amene sukuwadziwa n’komwe.+ 6 Abalewo achitira umboni ku mpingo za chikondi chako. Anthu oterewa akamachoka, utsanzikane nawo m’njira imene Mulungu angasangalale nayo,+ 7 chifukwa iwo anapita kukalalikira za dzina la Mulungu, ndipo sanatenge chilichonse+ kwa anthu a mitundu ina. 8 Choncho, ife tili ndi udindo wolandira bwino anthu amenewa ndi kuwachereza,+ kuti akhale antchito anzathu m’choonadi.+

9 Ndinalemba nkhani inayake kumpingo, koma Diotirefe, amene amakonda kukhala woyamba+ pakati pawo, salandira mwaulemu+ chilichonse chochokera kwa ife.+ 10 N’chifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula ntchito zake zimene akupitirizabe kuchita.+ Iye amatinenera zamwano,+ komanso chifukwa chosakhutira ndi zinthu zimenezi, iye salandira abalewo+ mwaulemu, ndipo amene amafuna kulandira+ abalewo, amawatsekereza+ ndi kuwachotsa+ mumpingo.

11 Wokondedwa, usamatsanzire zinthu zoipa koma uzitsanzira zabwino.+ Munthu amene amachita zabwino ndi wochokera kwa Mulungu.+ Koma wochita zoipa sadziwa Mulungu.+ 12 Anthu onse amuchitira umboni Demetiriyo.+ Choonadinso chikumuchitira umboni. Ifenso tikuchitira umboni,+ ndipo iwenso ukudziwa kuti umboni umene timapereka ndi woona.+

13 Ndinali ndi zambiri zoti ndikulembere, koma sindikufuna kuti ndipitirize kukulembera ndi inki ndi cholembera.+ 14 Koma ndikuyembekezera kukuona posachedwapa ndipo tidzalankhulana pamasom’pamaso.+

Mtendere ukhale nawe.+

Anzathu kuno akukupatsa moni.+ Iwenso undiperekere moni+ kwa anzathu kumeneko aliyense payekhapayekha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena