Agalatiya
1 Ine Paulo,+ ndine mtumwi,+ osati wochokera kwa anthu kapena woikidwa kudzera mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu+ ndi mwa Mulungu Atate+ amene anamuukitsa kwa akufa.+ 2 Ineyo, pamodzi ndi abale onse amene ali ndi ine,+ ndikulembera kalata mipingo ya ku Galatiya:+
3 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+ 4 Iye anadzipereka chifukwa cha machimo athu,+ kuti atilanditse ku nthawi* yoipayi,+ mogwirizana ndi chifuniro+ cha Mulungu ndi Atate wathu. 5 Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya.+ Ame.
6 Ndine wodabwa kuti mwapatutsidwa mwamsanga, kuchoka kwa Iye+ amene anakuitanani mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Khristu,+ ndipo mwakopeka ndi uthenga wabwino wamtundu wina.+ 7 Koma umenewo sikuti ndi uthenganso wabwino, kungoti pali anthu ena amene akukusokonezani+ ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 8 Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma nkhaniyo n’kukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa.+ 9 Monga mmene tanenera kale, ndikunenanso kuti, Aliyense amene akulengeza nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma yosiyana ndi imene munalandira,+ ameneyo akhale wotembereredwa.
10 Kodi ndiye kuti tsopano ndikufuna kukopa anthu kapena Mulungu? Kapena kodi ndikungofuna kukondweretsa anthu?+ Ndikanakhala kuti ndikukondweretsabe anthu,+ sindikanakhala kapolo wa Khristu.+ 11 Pakuti ndikufuna mudziwe, abale, kuti uthenga wabwino umene ndinaulengeza monga uthenga wabwino sunachokere kwa anthu.+ 12 Uthengawu sindinaulandire kwa munthu, ndipo sindinachite kuuphunzira mwanjira ina, koma Yesu Khristu ndiye amene anandiululira uthenga umenewu.+
13 Munamva ndithu zimene ndinali kuchita ndili m’Chiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri+ mpingo wa Mulungu ndi kupitirizabe kuuwononga.+ 14 Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.+ Pakuti ndinali wodzipereka kwambiri+ pa miyambo+ ya makolo anga. 15 Koma pamene Mulungu, amene anandichititsa kuti ndibadwe, anandiitana+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kunamukomera 16 kuulula za Mwana wake kudzera mwa ine,+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za iye.+ Sindinapite kukakambirana ndi anthu a thupi la nyama ndi magazi nthawi yomweyo.+ 17 Sindinapitenso ngakhale ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ndisanakhale ine,+ koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwereranso ku Damasiko.+
18 Ndiye pambuyo pa zaka zitatu ndinapita ku Yerusalemu+ kukacheza kwa Kefa+ ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19 Koma sindinaone mtumwi winanso kupatulapo Yakobo,+ m’bale+ wa Ambuye. 20 Zimene ndikukulemberanizi, ndikukuuzani pamaso pa Mulungu kuti sindikunama.+
21 Kenako ndinalowa+ m’madera a Siriya ndi Kilikiya. 22 Koma nkhope yanga inali yosadziwika kumipingo yogwirizana ndi Khristu, ya ku Yudeya.+ 23 Iwo ankangomva kuti: “Munthu amene anali kutizunza kale uja,+ tsopano akulengeza uthenga wabwino wonena za chikhulupiriro chimene anali kuwononga.”+ 24 Choncho anthuwo anayamba kulemekeza+ Mulungu chifukwa cha ine.