3 Yohane
Kalata Yachitatu ya Yohane
1 Ine monga mkulu,+ ndikulembera wokondedwa Gayo, amene ndimamukonda kwambiri.+
2 Wokondedwa,+ ndimapemphera kuti zinthu zonse zikuyendere bwino+ ndiponso kuti ukhale ndi thanzi labwino,+ monga mmenenso moyo wako ukuyendera bwino.+ 3 Ndinasangalala kwambiri pamene abale anabwera ndi kupereka umboni wa mmene ukupitira patsogolo m’choonadi, ndipo ndikusangalala chifukwa ukupitirizabe kuyenda m’choonadi.+ 4 Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.+
5 Wokondedwa, ukugwira ntchito mokhulupirika pa chilichonse chimene ukuchitira abale,+ amene sukuwadziwa n’komwe.+ 6 Abalewo achitira umboni ku mpingo za chikondi chako. Anthu oterewa akamachoka, utsanzikane nawo m’njira imene Mulungu angasangalale nayo,+ 7 chifukwa iwo anapita kukalalikira za dzina la Mulungu, ndipo sanatenge chilichonse+ kwa anthu a mitundu ina. 8 Choncho, ife tili ndi udindo wolandira bwino anthu amenewa ndi kuwachereza,+ kuti akhale antchito anzathu m’choonadi.+
9 Ndinalemba nkhani inayake kumpingo, koma Diotirefe, amene amakonda kukhala woyamba+ pakati pawo, salandira mwaulemu+ chilichonse chochokera kwa ife.+ 10 N’chifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula ntchito zake zimene akupitirizabe kuchita.+ Iye amatinenera zamwano,+ komanso chifukwa chosakhutira ndi zinthu zimenezi, iye salandira abalewo+ mwaulemu, ndipo amene amafuna kulandira+ abalewo, amawatsekereza+ ndi kuwachotsa+ mumpingo.
11 Wokondedwa, usamatsanzire zinthu zoipa koma uzitsanzira zabwino.+ Munthu amene amachita zabwino ndi wochokera kwa Mulungu.+ Koma wochita zoipa sadziwa Mulungu.+ 12 Anthu onse amuchitira umboni Demetiriyo.+ Choonadinso chikumuchitira umboni. Ifenso tikuchitira umboni,+ ndipo iwenso ukudziwa kuti umboni umene timapereka ndi woona.+
13 Ndinali ndi zambiri zoti ndikulembere, koma sindikufuna kuti ndipitirize kukulembera ndi inki ndi cholembera.+ 14 Koma ndikuyembekezera kukuona posachedwapa ndipo tidzalankhulana pamasom’pamaso.+
Mtendere ukhale nawe.+
Anzathu kuno akukupatsa moni.+ Iwenso undiperekere moni+ kwa anzathu kumeneko aliyense payekhapayekha.