LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 5/1 masa. 8-30
  • Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Yesu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Yesu?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUKHULUPILILA YESU N’KOFUNIKA
  • “INE NDACITITSA KUTI IO ADZIŴE DZINA LANU”
  • Citani Zinthu Mogwilizana Ndi Pemphelo La Yesu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • “Mudzakhala Mboni Zanga”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 5/1 masa. 8-30

KUCEZA NDI MNZATHU

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Yesu?

Tiyeni tione mmene wa Mboni za Yehova angacezele ndi munthu wina. Tiyelekeze kuti wa Mboni, dzina lake ndi M’bale Mumba, afika pakhomo la a Daka.

KUKHULUPILILA YESU N’KOFUNIKA

M’bale Mumba: Muli bwanji a Daka? Ndasangalala kuonananso ndi inu.

A Daka: Ndili bwino. Inenso ndasangalala.

M’bale Mumba: Ndakubweletselani Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! yatsopano. Ndikhulupilila kuti mudzasangalala kwambili ndi nkhani zili m’magaziniwa.

A Daka: Zikomo. Ndasangalala kuti mwabwela lelo. Ndili ndi funso.

M’bale Mumba: Mungafunse.

A Daka: Tsiku lina ndinali kukamba ndi mnzanga wa kunchito. Ndinamuuza nkhani zosangalatsa zili m’magazini amene munandipatsa. Koma iye anandiuza kuti sindiyenela kuwaŵelenga cifukwa Mboni za Yehova sizimam’khulupilila Yesu. Kodi zimenezo ndi zoona? Ndinamuuza kuti ndidzakufunsani ulendo wotsatila.

M’bale Mumba: Mwacita bwino kundifunsa. Mungadziŵe zimene munthu amakhulupilila kokha mutafunsa munthuyo mwacindunji.

A Daka: Inenso ndinaganiza conco.

M’bale Mumba: Zoona n’zakuti Mboni za Yehova zimam’khulupilila Yesu. Ndipo timaona kuti kukhulupilila Yesu n’kofunika kuti munthu apulumuke.

A Daka: Ndinaona kuti mumakhulupilila zimenezi. Koma pamene munthu amene ndimagwila naye nchito anandifunsa, ndinafuna kuti ndimve zambili. Ndikhulupilila kuti sitinakambilanepo nkhaniyi.

M’bale Mumba: Kodi mungakonde kuti ndikuonetseni mavesi a m’Baibulo amene akamba kuti kukhulupilila Yesu n’kofunika? Mavesiwa ndi amene Mboni za Yehova zimaŵelenga mu ulaliki.

A Daka: Ine ndingakonde.

M’bale Mumba: Tiyeni tiyambe ndi Yohane 14:6 kuti timve zimene Yesu iye mwini ananena. Pa lembali pali makambitsilano amene Yesu anali nao ndi atumwi ake. Kuŵelenga pakuti: “Yesu anamuuza kuti: ‘Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.’” Mogwilizana ndi vesili, kodi ndi njila imodzi iti imene tingayandikilile Atate?

A Daka: Ndi kudzela mwa Yesu.

M’bale Mumba: N’zoona. Ndipo izi ndi zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila. Lekani ndikufunsenkoni: Mogwilizana ndi zimene Mulungu amafuna, kodi muganiza kuti munthu ayenela kupempha kudzela mwa ndani?

A Daka: Kudzela mwa Yesu.

M’bale Mumba: N’zoona. Ndipo n’cifukwa cake nthawi zonse popemphela ndimachula dzina la Yesu. Mboni za Yehova nazonso zimachula dzina la Yesu.

A Daka: Cabwino ndamva.

M’bale Mumba: Tiyeni tionenso lemba la Yohane 3:16. Vesili ndi lofunika kwambili cakuti ena amanena kuti uthenga wonse wabwino upezeka m’vesi limeneli. Izi zitanthauza kuti vesili lichula zonse zimene zinalembedwa zokhudza umoyo ndi utumiki wa Yesu padziko lapansi. Kodi mungakonde kuŵelenga lembali?

A Daka: Inde ndingakonde. Lembali likuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

M’bale Mumba: Zikomo. Kodi vesi ili mulidziŵa?

A Daka: Inde ndamva anthu ambili akulichula ndipo mau ake amapezeka pa zizindikilo ndiponso pa zikwangwani.

M’bale Mumba: Anthu ambili amalidziŵa vesili. Onani zimene Yesu anakamba pa lembali. Iye anati anthu angakhale ndi moyo wosatha kaamba ka cikondi ca Mulungu. Koma kodi tiyenela kucita ciani kuti tikapeze moyo?

A Daka: Tiyenela kukhulupilila.

M’bale Mumba: Inde. Makamaka tiyenela kukhulupilila mwana wobadwa yekha Yesu Kristu. Pa tsamba 2 la magazini amene ndakubweletselani pali nkhani imene ionetsa kuti kukhulupilila Yesu kungatithandize kuti tikapeze moyo. Cimodzi mwa zolinga za magazini a Nsanja ya Mlonda ndi ‘kulimbikitsa anthu kukhulupilila Yesu Kristu amene anatifela kuti tikapeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.’

A Daka: Mukunena zoona. M’magazini anu muli umboni wosonyeza kuti Mboni za Yehova zimam’khulupilila Yesu.

M’bale Mumba: Zimenezi n’zoona.

A Daka: Nanga n’cifukwa ciani anthu amanena kuti simukhulupilila Yesu?

M’bale Mumba: Pali zifukwa zambili zimene anthu amanenela conco. Nthawi zina anthu amanena zimenezi cifukwa cakuti anamva zimene ena amakamba. Mwina anaphunzitsidwa zimenezi ndi atsogoleli ao acipembedzo.

A Daka: Ndikuganiza kuti anthu amakamba conco cifukwa cakuti mumadzicha kuti Mboni za Yehova osati Mboni za Yesu.

M’bale Mumba: Mwina cimeneci cingakhale cifukwa cina.

A Daka: N’cifukwa ciani mumakonda kukamba za Yehova?

“INE NDACITITSA KUTI IO ADZIŴE DZINA LANU”

M’bale Mumba: Timakhulupilila kuti kugwilitsila nchito dzina la Mulungu, Yehova monga mmene Yesu Mwana wake anacitila ndi cinthu cofunika. Ganizilani zimene Yesu anakamba popemphela kwa Atate wake pa lemba la Yohane 17:26. Kodi mungaŵelenge vesili?

A Daka: Inde. Lembali linena kuti: “Ine ndacititsa kuti io adziŵe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziŵitsa dzinalo kuti cikondi cimene munandikonda naco cikhale mwa io, inenso ndikhale wogwilizana ndi io.”

M’bale Mumba: Zikomo. Onani kuti Yesu anakamba kuti anadziŵitsa dzina la Mulungu. Kodi muganiza kuti n’cifukwa ciani Yesu anadziŵitsa dzina la Mulungu?

A Daka: Mmm. Sindidziŵa.

M’bale Mumba: Cabwino, mwina tingaŵelenge lemba lina limene limveketsa bwino nkhaniyi. Tiyeni tiŵelenge Machitidwe 2:21. Lembali limati: “Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Ndikhulupilila kuti mukuvomeleza kuti kuitana padzina la Yehova n’kofunika kuti tikapulumuke, ndipo Yesu anadziŵa bwino zimenezi.

A Daka: Inde ndikuvomeleza.

M’bale Mumba: Kuti otsatila a Yesu apulumuke, Yesu anaona kuti n’kofunika kuti io adziŵe dzina la Mulungu ndi kuligwilitsila nchito. Ndipo ici n’cifukwa cacikulu cimene timagwilitsila nchito dzina la Mulungu kwambili. Timaona kuti n’kofunika kuthandiza ena kudziŵa dzina la Mulungu ndi kuitana pa dzinalo.

A Daka: Koma ngakhale kuti anthu sadziŵa dzina la Mulungu kapena kuligwilitsila nchito, io amam’dziŵabe kuti ndi Mulungu.

M’bale Mumba: Mwina zimenezo n’zoona. Komabe mwa kutiuza dzina lake, Mulungu wacititsa kuti zisakhale zovuta kumuyandikila.

A Daka: Kodi mutanthauzanji?

M’bale Mumba: Ganizilani izi: Sitikanafunikila kudziŵa dzina la Mose. Tikanangomudziŵa kuti ndi munthu amene anagawanitsa Nyanja Yofiila kapena munthu amene analandila Malamulo Khumi. N’cimodzimodzi ndi Nowa. Tikanangomudziŵa kuti ndi munthu amene anapanga cingalawa ndi kupulumutsa banja lake ndi nyama. Ngakhale Yesu Kristu tikanangomudziŵa kuti ndi munthu amene anabwela padziko lapansi kudzatifela. Si conco?

A Daka: N’zoona.

M’bale Mumba: Koma Mulungu anaonetsetsa kuti tidziŵe maina a anthu amenewa. Kudziŵa maina ao kumatithandiza kuona nkhani zokhudza umoyo wao kuti ndi zenizeni. Ngakhale kuti sitinakumanepo ndi Mose, Nowa ndi Yesu, kudziŵa maina ao kumatithandiza kukhulupilila kuti io anakhalakodi.

A Daka: Sindinaganizepo conco. Koma zimene mwanena n’zoona.

M’bale Mumba: Ici n’cifukwa cake Mboni za Yehova zimagwilitsila nchito dzina la Mulungu. Timafuna kuthandiza anthu kukhulupilila kuti Yehova Mulungu ndi munthu weniweni amene io angamuyandikile. Panthawi imodzimodzi timalemekeza kwambili udindo umene Yesu ali nao pa kutithandiza kuti tikapulumuke. Mwina tingaŵelenge lemba limodzi kapena angapo kuti timvetse bwino nkhaniyi.

A Daka: Tingaŵelenge.

M’bale Mumba: Poyamba taŵelenga Yohane 14:6. Kumbukilani kuti Yesu anakamba kuti iye ndi “njila, coonadi ndi moyo.” Tiyeni tione zimene iye anakamba pa Yohane 14:1. Kodi mungaŵelenge zimene Yesu anakamba kothela kwa vesi loyamba?

A Daka: Cabwino. Lembali limati: “Khulupililani Mulungu, khulupililaninso ine.”

M’bale Mumba: Zikomo. Kodi tinganene kuti munthu ayenela kusankha kukhulupilila Yesu kapena Yehova?

A Daka: Iyai. Yesu anakamba kuti tiyenela kukhulupilila onse, Yehova ndi Iye.

M’bale Mumba: N’zoona zimenezo. Ndipo ndikhulupilila kuti inunso mudziŵa kuti kungonena kuti ndimakhulupilila Mulungu ndi Yesu si kokwanila. Zocita zathu ziyenela kusonyeza kuti timakhulupililadi Mulungu ndi Yesu.

A Daka: Ndithudi.

M’bale Mumba: Koma kodi munthu angasonyeze bwanji kuti amakhulupililadi Mulungu ndi Yesu? Mwina tingadzakambilane funso limeneli nthawi ina.a

A Daka: Cabwino tidzakambilana.

Kodi muli ndi funso pankhani ina ya m’Baibulo? Kodi mukufuna kudziŵa zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila? Ngati n’conco, mwamsanga funsani Mboni za Yehova. Iwo adzasangalala kukambilana nanu nkhaniyi.

a Ngati mukufuna kudziŵa zambili onani nkhani 12 m’buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli lipezekanso pa webusaiti ya jw.org.

Tiyenela kukhulupilila Yesu kuti tikapulumuke

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani