Salimo
Nyimbo ya Davide yotamanda Mulungu.
א [Aleph]
ב [Beth]
ג [Gimel]
ד [Daleth]
4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo.
Adzanena za ntchito zanu zamphamvu.+
ה [He]
5 Iwo adzanena za mphamvu zanu zodabwitsa+
Ndipo ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zodabwitsa.
ו [Waw]
6 Anthu adzanena za zochita zanu zochititsa mantha,*
Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.
ז [Zayin]
7 Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka,+
Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa cha chilungamo chanu.+
ח [Heth]
8 Yehova ndi wokoma mtima* komanso wachifundo,+
Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi chikondi chokhulupirika.+
ט [Teth]
9 Yehova ndi wabwino kwa aliyense,+
Ndipo ntchito zake zonse zimasonyeza kuti ndi wachifundo.
י [Yod]
כ [Kaph]
11 Iwo adzalengeza za ulemerero wa ufumu wanu+
Komanso adzalankhula za mphamvu zanu,+
ל [Lamed]
12 Kuti anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+
Ndiponso kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+
מ [Mem]
13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
Ndipo ulamuliro wanu udzakhalapo ku mibadwo yonse.+
ס [Samekh]
14 Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa+
Ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.+
ע [Ayin]
15 Zamoyo zonse zimayangʼana kwa inu mwachiyembekezo.
Mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+
פ [Pe]
16 Mumatambasula dzanja lanu
Nʼkukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.+
צ [Tsade]
17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,+
Ndipo ndi wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.+
ק [Qoph]
ר [Resh]
19 Amakwaniritsa zolakalaka za anthu amene amamuopa.+
Amamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo amawapulumutsa.+
ש [Shin]
ת [Taw]