Maliko
7 Tsopano Afarisi ndi alembi ena ochokera ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu.+ 2 Ndipo pamene anaona ena mwa ophunzira ake akudya chakudya ndi manja oipitsidwa, kapena kuti, m’manja mosasamba*+ . . . 3 pakuti Afarisi ndi Ayuda onse sadya osasamba m’manja mpaka m’zigongono, posunga mwambo wa makolo. 4 Akabwera kuchokera kumsika, sadya mpaka atadziyeretsa mwa kudziwaza madzi. Palinso miyambo ina yambiri+ imene anailandira ndipo akuisunga, monga kuviika makapu, mitsuko ndi ziwiya zamkuwa m’madzi+ . . . 5 choncho Afarisi ndi alembi amenewa anam’funsa iye kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira anu satsatira miyambo ya makolo, koma amadya chakudya ndi manja oipitsidwa?”+ 6 Iye anawayankha kuti: “Yesaya analosera moyenera za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenera kuti,+ ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine.+ 7 Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’+ 8 Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumirira mwambo wa anthu.”+
9 Pamenepo anapitiriza kuwauza kuti: “Mochenjera, mumakankhira pambali malamulo+ a Mulungu kuti musunge mwambo wanu. 10 Mwachitsanzo, Mose ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,’+ komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+ 11 Koma anthu inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene mukanatha kupindula nacho, ndi khobani,+ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa+ kwa Mulungu,)”’ . . . 12 anthu inu simulolanso munthuyo kuchitira bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+ 13 Mwa kuchita zimenezi, mumapangitsa mawu a Mulungu+ kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wanu umene munaupereka kwa anthu. Ndipo mumachita zinthu zambiri+ zofanana ndi zimenezi.” 14 Atatero, anaitananso khamu la anthuwo kuti abwere kwa iye, ndipo anayamba kulankhula nawo kuti: “Mverani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.+ 15 Palibe chilichonse chochokera kunja kwa munthu ndi kulowa m’thupi mwake chimene chingaipitse munthu, koma zotuluka mwa munthu ndi zimene zimaipitsa munthu.”+ 16* ——
17 Tsopano atalowa m’nyumba ina kutali ndi khamu la anthulo, ophunzira ake anayamba kumufunsa za fanizo lija.+ 18 Chotero iye anawafunsa kuti: “Kodi nanunso ndinu osazindikira ngati iwo aja?+ Kodi inunso simudziwa kuti palibe chochokera kunja kwa thupi n’kudutsa m’thupi mwa munthu chimene chingamuipitse, 19 popeza sichidutsa mumtima mwake, koma m’matumbo mwake, ndipo chimakatuluka kuchimbudzi?”+ Pamenepo anagamula kuti zakudya zonse n’zoyera.+ 20 Kenako anafotokozanso kuti: “Chotuluka mwa munthu n’chimene chimaipitsa munthu.+ 21 Pakuti mkatimo, mumtima mwa munthu,+ mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama,*+ zakuba, zaumbanda,+ 22 zachigololo, kusirira kwa nsanje,+ kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira,+ diso la kaduka, mnyozo, kudzikweza, ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena. 23 Zoipa zonsezi zimatuluka mkatimo ndipo zimaipitsa munthu.”+
24 Atanyamuka kumeneko, analowera kumadera a Turo ndi Sidoni.+ Kumeneko anakalowa m’nyumba ina, ndipo sanafune kuti aliyense adziwe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziwabe.+ 25 Nthawi yomweyo, mayi wina amene anali ndi mwana wamkazi wogwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye ndipo anabwera ndi kugwada, n’kumuweramira mpaka nkhope yake pansi.+ 26 Mayiyu anali Mgiriki, wachisurofoinike. Iye anapempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wakeyo.+ 27 Koma Yesu anayamba n’kunena kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana+ ndi kuponyera tiagalu.”+ 28 Koma poyankha mayiyo ananena kuti: “Inde mbuyanga, komabe tiagalu timadya nyenyeswa+ za anawo pansi pa tebulo.”+ 29 Yesu atamva mawuwo anauza mayiyo kuti: “Chifukwa wanena zimenezi, pita, chiwandacho chatuluka mwa mwana wakoyo.”+ 30 Choncho anapita kunyumba kwake ndipo anakapeza+ mwanayo atagona pabedi chiwandacho chitatuluka.
31 Tsopano pobwerera kuchoka m’madera a Turo, anadutsa ku Sidoni ndi kufika kunyanja ya Galileya mpaka kukadutsa mkati mwa zigawo za Dekapole.+ 32 Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wogontha komanso wovutika kulankhula. Iwo anamupempha kuti aike dzanja lake pa munthuyo.+ 33 Koma iye anatenga munthuyo ndi kuchoka naye pakhamu la anthulo kupita naye pambali. Kumeneko anapisa zala zake m’makutu a munthuyo, ndipo analavula ndi kukhudza lilime lake.+ 34 Pamenepo anayang’ana kumwamba,+ kenako anausa moyo*+ ndi kumuuza kuti: “Efata,” kutanthauza kuti, “Tseguka.” 35 Atatero, makutu ake anatseguka,+ lilime lake lomangikalo linamasuka, moti anayamba kulankhula bwinobwino. 36 Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimenezo.+ Koma ankati akawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense, m’pamenenso iwo anali kuzifalitsa kwambiri.+ 37 Inde, iwo anali kudabwa kwambiri+ ndipo anali kunena kuti: “Wachita zinthu zonse bwinobwino ndithu. Ngakhale ogontha akumva ndipo osalankhula akuwalankhulitsa.”+