Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Adzachita zimenezi popeza udzamvera mawu a Yehova Mulungu wako ndi kusunga malamulo ake ndi mfundo zake zolembedwa m’buku ili la chilamulo,+ chifukwa udzabwerera kwa Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse.+

  • 1 Samueli 7:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+

  • Yeremiya 4:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli, ubwerere kwa ine.+ Ndipo ngati ungachotse zinthu zako zonyansazo chifukwa cha ine,+ sudzakhalanso wothawathawa.

  • Yoweli 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ng’ambani mitima yanu+ osati zovala zanu+ ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu pakuti iye ndi wachisomo, wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Ndithu, iye adzakumverani chisoni chifukwa cha tsokalo.+

  • Malaki 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kuyambira m’masiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawasunge.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa makamu.

      Koma inu mukunena kuti: “Tibwerere motani?”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena