Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+

      Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+

      Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera.

      Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake.

  • 1 Samueli 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+

      Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+

      Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+

      Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+

      Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+

  • Salimo 7:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mulungu ndi Woweruza wolungama,+

      Ndipo Mulungu amapereka ziweruzo tsiku lililonse.

  • Salimo 50:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Ndipo kumwamba kukunena za chilungamo chake,+

      Pakuti Mulungu ndiye Woweruza.+ [Seʹlah.]

  • Mlaliki 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ine ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mulungu woona adzaweruza munthu wolungama ndi munthu woipa,+ pakuti iye ali ndi nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena