Yobu
9 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.
Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+
7 Amauza dzuwa kuti lisawale,
Ndipo amaphimba nyenyezi.+
8 Kumwamba anakutambasula yekha,+
Ndipo amayenda pamafunde aatali a m’nyanja.+
9 Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, gulu la nyenyezi la Kesili,
Gulu la nyenyezi la Kima+ ndi zipinda zamkati za Kum’mwera.
10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+
Ndiponso zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+
14 N’chifukwa chake ndikamamuyankha,
Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.+
15 Choncho, sindingamuyankhe ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona.+
Ndingachonderere amene akutsutsana nane pa mlandu.+
16 Nditamuitana, kodi angandiyankhe?+
Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere.
17 Iye amene wandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho,
Wachulukitsa zilonda zanga popanda chifukwa.+
19 Ngati kuli wamphamvu kwambiri, ndi iyeyo.+
Ngati pali wolimbikitsa chilungamo, ndikufuna andiitane.
20 Ndikanakhala kuti ndikulondola, pakamwa panga pomwe pakanandinena kuti ndine wolakwa.
Ndikanakhala wosalakwa, iye akanandinena kuti ndine wachinyengo.
21 Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, sindikanadziwa zimenezo,
Ndipo ndikanakana moyo wanga.
22 N’chifukwa chake ndikunena kuti zonsezo mfundo yake ndi imodzi, yakuti:
‘Iye amapha osalakwa komanso oipa.’+
23 Anthu atati afe mwadzidzidzi chifukwa cha kusefukira kwa madzi,
Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.
24 Dziko lapansi laperekedwa m’manja mwa woipa.+
Iye amaphimba nkhope za oweruza ake.
Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?
25 Komanso masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+
Iwo athawa ndipo ndithu sadzaona zabwino.
26 Ayenda ngati ngalawa za bango,
Ngati chiwombankhanga chimene chimauluka uku ndi uko pofunafuna chakudya.+
30 Nditati ndisambe madzi a chipale chofewa,
Ndi kusamba m’manja ndi sopo,+
31 Inuyo mungandiviike m’dzenje,
Ndipo zovala zanga zinganyansidwe nane ndithu.
35 Ndilankhule ndipo ndisachite naye mantha,
Chifukwa ine sindiopa kulankhula naye.