2 Mafumu
11 Tsopano Ataliya,+ mayi wa Ahaziya+ ataona kuti mwana wake wafa, anapha ana onse achifumu.+ 2 Koma Yehoseba+ mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa+ m’chipinda chamkati chogona kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe. 3 Anapitiriza kubisidwa m’nyumba ya Yehova zaka 6, pamene Ataliya anali kulamulira dzikolo.+
4 M’chaka cha 7, Yehoyada+ anatumiza uthenga kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu Achikariya,+ ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 othamanga.+ Anawaitanitsa kuti abwere kwa iye kunyumba ya Yehova ndipo anachita nawo pangano+ n’kuwalumbiritsa+ kunyumba ya Yehova. Kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja. 5 Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Gawo limodzi mwa magawo atatu a inu lidzabwere pa tsiku la sabata kudzalondera nyumba ya mfumu mosamala.+ 6 Gawo lina limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata+ chotchedwa Maziko, ndipo gawo linanso limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata kumbuyo kwa asilikali othamanga. Muzidzasinthana kulondera mosamala nyumbayo.+ 7 Magulu awiri a inu amene adzatuluke pa sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu. 8 Mudzaizungulire mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga zida zake m’manja, ndipo aliyense wolowa pakati pa mizere ya anthu adzaphedwe. Muzidzakhala limodzi ndi mfumuyo ikamatuluka ndiponso ikamalowa.”
9 Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata,+ pamodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata, n’kupita kwa wansembe Yehoyada. 10 Tsopano wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira za Mfumu Davide, zomwe zinali m’nyumba ya Yehova.+ 11 Asilikali othamanga+ anaimirira, aliyense atatenga zida zake m’manja, kuyambira kumbali yakumanja* ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere* ya nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 12 Kenako anatulutsa mwana+ wa mfumu uja. Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu+ n’kumudzoza.+ Ndiyeno anayamba kuwomba m’manja+ n’kumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+
13 Ataliya atamva anthu akuchita phokoso komanso akuthamanga, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+ 14 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala+ malinga ndi mwambo wawo. Anaonanso atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba malipenga. Nthawi yomweyo Ataliya+ anang’amba zovala zake n’kuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+ 15 Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa,+ kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu! Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!”+ Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Muonetsetse kuti asaphedwere m’nyumba ya Yehova.” 16 Choncho anamugwira n’kumutulutsira pakhomo la kunyumba ya mfumu+ lolowera mahatchi,+ ndipo anam’phera pamenepo.+
17 Kenako Yehoyada anachita pangano+ pakati pa Yehova,+ mfumu,+ ndi anthu, kuti anthuwo azisonyeza kuti ndi anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+ 18 Pambuyo pake, anthu onse a m’dzikolo anapita kukachisi wa Baala n’kukagwetsa maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha patsogolo pa maguwa ansembewo.+
Kenako wansembe Yehoyada anaika anthu kuti aziyang’anira nyumba ya Yehova.+ 19 Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100, asilikali olondera mfumu Achikariya,+ asilikali othamanga,+ ndi anthu onse a m’dzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anadzera njira ya pachipata+ cha asilikali othamanga, mpaka anafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu+ wa mafumu. 20 Anthu onse a m’dzikolo anapitiriza kusangalala,+ ndipo mumzindawo munali bata. Ataliya anali atamupha ndi lupanga panyumba ya mfumu.+