Deuteronomo
13 “Mneneri+ kapena wolota maloto+ akauka pakati panu n’kukupatsani chizindikiro kapena chodabwitsa cholosera zam’tsogolo,+ 2 ndipo chizindikiro kapena chodabwitsa chimenecho chachitikadi,+ chimene anachita ponena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina imene simunaidziwe, ndipo tiitumikire,’ 3 musamvere mawu a mneneriyo kapena wolotayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mukukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.+ 4 Muzitsatira Yehova Mulungu wanu, muzimuopa, muzisunga malamulo ake, muzimvera mawu ake, muzim’tumikira ndi kum’mamatira.+ 5 Ndipo mneneri+ kapena wolota malotoyo muzimupha,+ chifukwa walankhula mopandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi kukuwombolani m’nyumba yaukapolo. Munthu ameneyo walankhula zimenezo kuti akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuyendamo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+
6 “M’bale wako, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi ako, kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, mkazi wako wokondedwa kapena bwenzi lako lapamtima,+ akayesa kukupatutsa mwamseri pokuuza kuti, ‘Tiye tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene iwe kapena makolo ako sanaidziwe, 7 milungu ina mwa milungu ya anthu okuzungulirani, okhala pafupi nanu kapena okhala kutali, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena, 8 usavomereze zofuna zake kapena kumumvera.+ Diso lako lisamumvere chifundo ndipo usamumvere chisoni+ kapena kum’bisa kuti um’teteze. 9 Koma umuphe ndithu.+ Dzanja lako lizikhala loyamba kum’ponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ 10 Uzim’ponya miyala kuti afe,+ chifukwa anali kufuna kukupatutsa ndi kukuchotsa kwa Yehova Mulungu wako, amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+ 11 Pamenepo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha, ndipo sadzachita chinthu choipa chilichonse chofanana ndi chimenechi pakati panu.+
12 “Mu umodzi mwa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti mukhalemo, mukadzamva kuti, 13 ‘Pakati panu papezeka anthu opanda pake+ amene akufuna kupatutsa anthu mumzinda wawo,+ ponena kuti: “Tiyeni tikatumikire milungu ina,” milungu imene inu simunaidziwe,’ 14 muzifunafuna, kufufuza ndi kufunsitsa za nkhani imeneyo.+ Mukapeza kuti ndi zoonadi, choipa chimenechi chachitikadi pakati panu, 15 muzipha ndithu anthu a mumzindawo ndi lupanga.+ Muziwononga+ ndi lupanga mzindawo ndi chilichonse chimene chili mmenemo, kuphatikizapo ziweto zake. 16 Zofunkha zake zonse muzizisonkhanitsa pakati pa bwalo la mzindawo. Pamenepo muzitentha mzindawo+ ndi zofunkha zake zonse monga nsembe yathunthu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Ndipo mzindawo uzikhala bwinja mpaka kalekale.+ Usadzamangidwenso. 17 Ndipo kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa* kasamamatire kudzanja lanu,+ kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova usiye kukuyakirani+ ndipo akuchitireni chifundo ndi kukumverani chisoni,+ kutinso akuchulukitseni, monga mmene analumbirira makolo anu.+ 18 Motero muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mwa kusunga malamulo ake+ onse amene ndikukupatsani lero, kuti muzichita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+