Habakuku
3 Ili ndi pemphero la mneneri Habakuku limene anaimba ngati nyimbo yoimba polira:* 2 “Inu Yehova, ndamva uthenga wonena za inu.+ Ndachita mantha ndi ntchito zanu, Inu Yehova.+
M’zaka zimenezi sonyezani ntchito zanu! m’zaka zimenezi chititsani ntchito zanu kuti zidziwike. Pa nthawi ya mkwiyo wanu kumbukirani kusonyeza chifundo.+
3 Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo anabwera kuchokera kuphiri la Parana.+ [Seʹlah.]+
Ulemerero wake unaphimba kumwamba+ ndipo dziko lonse linamutamanda.+
4 Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa masana.+ Kuwala kwa mitundu iwiri kunali kutuluka m’dzanja lake ndipo m’dzanja lakemo ndi mmene munali kubisala mphamvu zake.+
5 Mliri unali kuyenda patsogolo pake+ ndipo matenda otenthetsa thupi anali kuyenda patsogolo pa mapazi ake.+
6 Iye anaima chilili kuti agwedeze dziko lapansi.+ Anayang’ana mitundu ya anthu ndipo mitunduyo inadumpha.+
Mapiri amuyaya anaphwanyidwa.+ Zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale* zinawerama.+ Zimenezi ndi njira zake zakalekale.
7 Ndinaona mahema a Kusani ali ndi nkhawa. Nsalu za mahema a m’dziko la Midiyani+ zinayamba kunjenjemera.+
8 Inu Yehova, kodi mwapsera mtima mitsinje?+ Kodi mkwiyo wanu wayakira nyanja+ pamene inu munakwera pamahatchi anu?+ Magaleta anu anabweretsa chipulumutso.+
9 Munachotsa uta moikamo mwake.+ Zimene mafuko a anthu ananena ndiwo malumbiro awo.+ [Seʹlah.] Munagawa dziko lapansi pogwiritsa ntchito mitsinje.+
10 Mapiri anakuonani ndipo anamva ululu waukulu.+ Mvula yamphamvu yamabingu inadutsa. Madzi akuya anachita mkokomo+ ndipo anathuvuka m’malere.
11 Kumwamba,+ dzuwa ndi mwezi zinaima.+ Mivi yanu inapitiriza kuyenda ngati kuwala.+ Kunyezimira kwa mkondo wanu kunakhala ngati kuwala kounikira.+
12 Munadutsa m’dziko lapansi ndi kulidzudzula mwamphamvu. Inu mutakwiya munapuntha mitundu ya anthu ngati mbewu.+
13 Munapita kuti mukapulumutse anthu anu,+ kuti mukapulumutse wodzozedwa wanu. Munaphwanyaphwanya mtsogoleri wa nyumba ya wochimwa.+ Nyumbayo inafafanizidwa mpaka kudenga moti maziko a nyumbayo anaonekera.+ [Seʹlah.]
14 Munabaya*+ mitu ya asilikali ake ndi zida zake zomwe, pamene iwo anali kubwera ngati mphepo yamkuntho kuti adzandimwaze.+ Kukondwera kwawo chifukwa cha tsoka langa kunali ngati kwa anthu amene akonzeka kuti ameze munthu wosautsidwa m’malo obisalamo.+
15 Munadutsa panyanja ndi mahatchi anu, munadutsa pamadzi ambiri.+
16 Nditamva mawu ake, m’mimba mwanga munayamba kubwadamuka ndipo milomo yanga inanjenjemera. Mafupa anga anayamba kuwola+ ndipo ndinanthunthumira chifukwa cha mmene zinthu zinalili. Choncho ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso.+ Tsiku limeneli lidzabwera kwa anthu+ ngati mmene munthu amabwerera kwa adani ake kuti awaukire.