Yoweli
3 “Ndiyeno masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ ndidzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo.+ 2 Ine ndidzasonkhanitsanso pamodzi mitundu yonse ya anthu+ ndi kuibweretsa m’chigwa cha Yehosafati+ ndipo ndidzaiweruza chifukwa cha anthu anga ndi cholowa changa, Isiraeli.+ Mitundu imeneyi inamwaza Isiraeli pakati pa mitundu ya anthu ndiponso inagawana dziko langa.+ 3 Mitunduyi inali kuchitira maere anthu anga+ ndipo inali kupereka mwana wamwamuna kuti akhale malipiro a hule.+ Inali kupereka mwana wamkazi kuti akhale malipiro a vinyo woti amwe.
4 “Tsopano ndili nawenso chiyani iwe Turo ndi Sidoni+ ndiponso inu nonse okhala m’chigawo cha Filisitiya?+ Kodi zimenezi ndi zimene mukundipatsa monga mphoto yanga? Ngati mukundipatsa zimenezi, ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+ 5 Chifukwa chakuti anthu inu mwatenga siliva ndi golide wanga,+ mwabweretsa zinthu zanga zamtengo wapatali mu akachisi anu,+ 6 mwagulitsa ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu+ kwa ana a Agiriki,+ ndi cholinga choti muwachotse ndi kuwapititsa kutali ndi dziko lawo,+ 7 tsopano ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa+ ndipo ndikubwezerani zimene munachita.+ 8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa ana a Yuda.+ Ana a Yudawo adzawagulitsa kwa amuna a ku Sheba,+ mtundu wa anthu akutali.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.
9 “Anthu inu, lengezani pakati pa mitundu ina kuti,+ ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu!+ Amuna onse ankhondo abwere!+ 10 Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo+ kuti zikhale mikondo ing’onoing’ono. Munthu wofooka anene kuti: “Ndine mwamuna wamphamvu.”+ 11 Inu mitundu ya anthu yokhala mozungulira, bwerani mudzathandizane+ ndipo nonse musonkhane pamodzi.’”+
Inu Yehova, bweretsani ankhondo anu kumalo amenewo.+
12 “Mitundu ya anthu inyamuke ndi kubwera kuchigwa cha Yehosafati,+ pakuti kumeneko ndidzakhala pansi kuti ndiweruze mitundu yonse ya anthu yokhala mozungulira.+
13 “Yambani kumweta ndi chikwakwa,+ pakuti zokolola zacha.+ Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri.+ 14 Makamu ambirimbiri a anthu ali m’chigwa+ choweruzira mlandu, pakuti tsiku la Yehova layandikira m’chigwa choweruzira mlandu.+ 15 Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima, ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala.+ 16 Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+ 17 Pamenepo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu,+ amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+ Yerusalemu adzakhala malo anga opatulika,+ ndipo alendo sadzadutsanso mmenemo.+
18 “Nthawi imeneyo mapiri adzachucha vinyo wotsekemera.+ Mkaka udzayenda pazitunda ndipo m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi. Kasupe wamadzi adzatuluka m’nyumba ya Yehova+ ndi kuthirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe.+ 19 Iguputo adzasanduka bwinja,+ Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu+ chifukwa cha chiwawa chimene anachitira ana a Yuda, ndiponso chifukwa chokhetsa magazi osalakwa m’dziko la Yudalo.+ 20 Koma mu Yuda mudzakhala anthu mpaka kalekale,+ ndipo mu Yerusalemu mudzakhala anthu ku mibadwomibadwo.+ 21 Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+ ndipo Yehova azidzakhala mu Ziyoni.”+